Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zoipa Zonse Zidzathadi

Zoipa Zonse Zidzathadi

 Zoipa Zonse Zidzathadi

MULUNGU watipatsa Mawu ake ouziridwa amene amafotokoza zimene zimachititsa anthu kuchita zoipa. Iye watipatsanso ufulu wosankha ndiponso anatilenga moti tikhoza kudziletsa. Chifukwa cha zimenezi tingathe kupewa kuchita zoipa. (Deuteronomo 30:15, 16, 19) Choncho, tingathe kuzindikira zizolowezi zilizonse zoipa zimene tingakhale nazo, n’kupeza njira zozithetsera. Tikamapewa kuchita zinthu zoipa, tidzakhala osangalala kwambiri ndiponso tidzasangalatsa anthu anzathu.​—Salmo 1:1.

Koma ngakhale ifeyo titayesetsa bwanji kupewa kuchita zinthu zoipa, anthu ena apitirizabe kuchita zinthu zoipa m’dzikoli. Baibulo limachenjeza kuti: “Koma dziwa kuti, m’masiku otsiriza, idzafika nthawi yovuta yoikika.” Pofotokoza chifukwa chake masiku  otsiriza adzakhala ‘ovuta,’ Baibulo limapitiriza kuti: “Anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, odzimva, odzikweza, onyoza, osamvera makolo, osayamika, osakhulupirika, opanda chikondi chachibadwa, osagwirizanitsika, odyerekeza, osadziletsa, owopsa, osakonda zabwino, achiwembu, aliuma, otukumuka chifukwa cha kunyada, okonda zosangalatsa, m’malo mokonda Mulungu, ooneka ngati odzipereka kwa Mulungu koma mphamvu ya kulambira Mulungu siitha kuwasintha; anthu amenewa, uwapewe.”​—2 Timoteyo 3:1-5.

Mwina mwaona mawu akuti, “masiku otsiriza” mu lemba limene lili pamwambali. Kodi mukuganiza kuti mawu amenewa akutanthauza chiyani? Monga mmene anthu ambiri amadziwira, mawu akuti “masiku otsiriza” amasonyeza kuti chinachake chitha posachedwapa. Kodi chimene chithecho n’chiyani? Taonani zimene Mulungu walonjeza m’Mawu ake.

Anthu onse oipa adzawonongedwa.

“Katsala kanthawi ndipo woipa adzatha psiti: Inde, udzayang’anira mbuto yake, nudzapeza palibe. Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.”​SALMO 37:10, 11.

“Yehova asunga onse akukondana naye; koma oipa onse adzawaononga.”​SALMO 145:20.

Sikudzakhalanso kuponderezana.

“Adzapulumutsa waumphawi wofuulayo; ndi wozunzika amene alibe mthandizi. Adzawombola moyo wawo ku chinyengo ndi chiwawa; ndipo mwazi wawo udzakhala wa mtengo pamaso pake.”​SALMO 72:12, 14.

“Chilengedwecho chidzamasulidwa ku ukapolo wa kuvunda ndi kukhala ndi ufulu waulemerero wa ana a Mulungu.”​AROMA 8:21.

Anthu adzakhala ndi zofunika zonse pa moyo.

“Adzakhala munthu yense patsinde pa mpesa wake, ndi patsinde pa mkuyu wake; ndipo sipadzakhala wakuwawopsa.”​MIKA 4:4.

“Iwo adzamanga nyumba ndi kukhalamo; ndipo iwo adzawoka minda yamphesa, ndi kudya zipatso zake. Iwo sadzamanga, ndi wina kukhalamo; iwo sadzawoka, ndi wina kudya; pakuti monga masiku amtengo adzakhala masiku a anthu anga; ndi osankhidwa anga adzasangalala nthawi zambiri ndi ntchito za manja awo.”​YESAYA 65:21, 22.

Zinthu zizidzachitika mwachilungamo.

“Nanga Mulungu sadzaonetsetsa kuti chilungamo chachitika kwa osankhika ake, amene amafuulira kwa iye usiku ndi usana . . . ? Ndithu ndikukuuzani, Iye adzaonetsetsa kuti chilungamo chachitika kwa iwo mwamsanga.”​LUKA 18:7, 8.

“Yehova akonda chiweruzo [chilungamo], ndipo sataya okondedwa ake: asungika kosatha.”​SALMO 37:28.

Chilungamo chidzalowa m’malo mwa kudzikonda.

“Maweruziro anu ali pa dziko lapansi, okhala m’dziko lapansi adzaphunzira chilungamo.”​—YESAYA 26:9.

“Pali miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano zimene ife tikuyembekeza malinga ndi lonjezo lake, ndipo mmenemo mudzakhala chilungamo.”​2 PETULO 3:13.

Ngakhale Panopo Anthu Akusintha

N’zosachita kufunsa kuti tonsefe tingasangalale ndi malonjezo amenewa. Koma kodi pali umboni wotani wosonyeza kuti malonjezo amenewa adzakwaniritsidwadi? Dziwani kuti panopa tili ndi umboni wosonyeza kuti zimene Mulungu walonjeza zidzachitikadi. Kodi umboni umenewu ndi uti? Umboni  wake ndi wakuti masiku ano anthu ambiri padziko lonse asiya makhalidwe monga kudzikonda, chiwawa ndiponso makhalidwe ena oipa ndipo aphunzira kukhala oona mtima, amtendere ndiponso okoma mtima. Panopa Mboni za Yehova zilipo zoposa 7 miliyoni ndipo zili pa ubale wapadziko lonse. Iwo sakhala ndi mavuto amene amabwera chifukwa chosiyana mayiko, mitundu, zikhalidwe, ndale ndiponso nkhani zachuma zimene kwa nthawi yaitali, zabweretsa mavuto ambiri monga chidani, chiwawa ndiponso kuphana. * Kusintha kumeneku ndi umboni wosatsutsika wakuti zonse zimene Mulungu walonjeza zidzakwaniritsidwadi padziko lonse.

Komabe n’chiyani chimene chachititsa kuti asinthe chonchi? Yankho tingalipeze mu lonjezo lina la m’Baibulo limene mneneri Yesaya analemba. Iye analemba kuti:

“Mmbulu udzakhala pamodzi ndi mwana wa nkhosa, ndipo nyalugwe adzagona pansi ndi mwana wa mbuzi; ndipo mwana wa ng’ombe ndi mwana wa mkango ndi choweta chonenepa pamodzi; ndipo mwana wamng’ono adzazitsogolera, . . . ndipo mkango udzadya udzu ngati ng’ombe. Ndipo mwana wakuyamwa adzasewera pa una wa mamba, ndi mwana woleka kuyamwa adzaika dzanja lake m’funkha la mphiri. Sizidzaipitsa, sizidzasakaza m’phiri langa lonse loyera, chifukwa kuti dziko lapansi lidzadzala ndi odziwa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.”​—Yesaya 11:6-9.

Kodi ulosi umenewu ukungonena za nthawi imene nyama zidzakhala pa mtendere ndi anthu? Ayi. Ulosiwu umanenanso za zinthu zina. Onani kuti mbali yomalizira ya ulosiwu ikusonyeza zimene zidzachititse kuti zinthu zisinthe. “Dziko lapansi lidzadzala ndi odziwa Yehova.” Kodi kudziwa Mulungu kungachititse kuti nyama zisinthe khalidwe? N’zosatheka. Koma anthu ndi amene angathe kusintha chifukwa chodziwa Mulungu. Ulosi umenewu umanena kuti anthu amene anali ndi  makhalidwe oipa ngati a nyama adzasintha n’kukhala ndi makhalidwe ngati a Khristu chifukwa chophunzira ndi kugwiritsa ntchito zimene Baibulo limaphunzitsa.

Mwachitsanzo taganizirani zimene zinachitikira Pedro. * Iye analowa m’gulu lina la zigawenga ndipo ankakhulupirira kuti kuchita zinthu zauchigawenga kuthandiza kuti zinthu zizichitika mwachilungamo. Atamaliza maphunziro a zauchigawengazo, anauzidwa kuti akaphulitse malo ena a apolisi. Koma anamangidwa akukonzekera kuti akachite zachiwembuzo. Pedro anatsekeredwa m’ndende kwa miyezi 18 koma ali m’ndendemo ankapitirizabe kuchita zoukira boma. Pa nthawi imeneyi mkazi wake anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Atatuluka ku ndende, nayenso anayamba kuphunzira Baibulo. Zimene anaphunzira zokhudza Yehova Mulungu zinamuchititsa kusintha khalidwe lake komanso kusintha mmene ankaonera moyo. Iye ananena kuti: “Ndimathokoza kwambiri Yehova kuti pa nthawi yonse imene ndinali chigawenga sindinaphepo munthu. Panopa ndimagwiritsa ntchito lupanga la mzimu wa Mulungu, lomwe ndi Baibulo, kuti ndiwauze anthu uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu umene udzabweretsa mtendere weniweni ndiponso chilungamo.” Pedro anapitanso ngakhale kumalo a apolisi kumene ankafuna kuwaphulitsa aja n’cholinga chakuti akauze anthu uthenga wa mtendere ndiponso za dziko lopanda chiwawa.

 Mawu a Mulungu ali ndi mphamvu yosintha anthu ndipo zimenezi zimatithandiza kukhulupirira kwambiri kuti zimene Mulungu walonjeza kuti adzachotsa zoipa zonse, zidzachitikadi. Inde, nthawi idzafika imene anthu sadzachita zinthu zoipa chifukwa adzasintha n’kukhala anthu abwino. Posachedwapa, Yehova awononga Satana Mdyerekezi, yemwe ndi chimake cha zoipa zonse ndiponso ndi amene wachititsa kuti anthu azichita zinthu zoipa m’dzikoli. Baibulo limati: “Dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Koma posachedwapa iye sadzakhalaponso. Enanso amene adzawonongedwe ndi anthu amene amakanitsitsa kusintha makhalidwe awo oipa. Zidzakhalatu zosangalatsa kwambiri kukhala ndi moyo pa nthawi imeneyo.

Kodi mungatani kuti mudzakhale m’dziko limenelo? Musaiwale kuti ‘kudziwa Yehova’ ndi kumene kukuthandiza kuti anthu asinthe masiku ano ndipo ndi kumenenso posachedwapa kudzasinthe zinthu padziko lonse lapansi. Mofanana ndi zimene anachita Pedro, kuphunzira Baibulo ndiponso kugwiritsa ntchito zimene mwaphunzira, kungachititse kuti nanunso muziyembekezera kudzakhala m’dziko limene “mudzakhala chilungamo.” (2 Petulo 3:13) Choncho, tikukulimbikitsani kugwiritsa ntchito mwayi umene ulipo wophunzira za Mulungu ndi Yesu Khristu. Zimenezo n’zimene zidzachititse kuti mudzapeze moyo wosatha.​—Yohane 17:3.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 21 Kuti mudziwe zambiri, werengani kabuku kakuti, Mboni za Yehova​—Kodi Iwo Ndani? Kodi Amakhulupirira Chiyani? kofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 25 Tasintha dzina.

[Mawu Otsindika patsamba 9]

Nanunso mungayembekezere kudzakhala m’dziko limene “mudzakhala chilungamo.”​—2 PETULO 3:13.