NSANJA YA OLONDA (YOPHUNZIRA) October 2014

Magaziniyi ili ndi nkhani zimene tidzaphunzire kuyambira pa December 1 mpaka 28, 2014.

Anadzipereka ndi Mtima Wonse ku Taiwan

A Mboni za Yehova oposa 100 apita kukatumikira ku Taiwan. Onani mmene zinthu zikuyendera pa moyo wawo komanso zimene zikuwathandiza kutumikira bwino.

Tizikhulupirira Kwambiri Ufumu wa Mulungu

Yehova anagwiritsa ntchito mapangano 6 posonyeza kuti Ufumu wake sudzalephera kukwaniritsa cholinga chake. Kodi mapanganowa angatithandize bwanji kukhulupirira kwambiri Ufumu?

‘Mudzakhala Ufumu wa Ansembe’

Pali mapangano 6 ndipo atatu omalizira angatithandize kukhulupirira kwambiri Ufumu wa Mulungu ndiponso kulalikira uthenga wabwino wokhudza Ufumuwu.

MBIRI YA MOYO WANGA

Zinthu Zosaiwalika pa Utumiki Wanga

Mildred Olson watumikira Yehova kwa zaka zoposa 75. Anachita umishonale ku El Salvador kwa zaka pafupifupi 29. N’chiyani chimamuthandiza kuchitabe zinthu ngati wachinyamata?

Kodi Mumayamikira Mwayi Wogwira Ntchito ndi Yehova?

N’chiyani chimachititsa anthu a Yehova kusiya zofuna zawo kuti azimutumikira?

“Ikani Maganizo Anu pa Zinthu Zakumwamba”

N’chifukwa chiyani anthu amene adzakhale padziko lapansi ayenera kuikanso maganizo awo pa zinthu zakumwamba? Kodi angachite bwanji zimenezi?