Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Tizikhulupirira Kwambiri Ufumu wa Mulungu

Tizikhulupirira Kwambiri Ufumu wa Mulungu

“Chikhulupiriro ndicho chiyembekezo chotsimikizika cha zinthu zoyembekezeredwa.”—AHEB. 11:1.

1, 2. Kodi kuganizira mapangano kungatithandize bwanji? (Onani chithunzi pamwambapa.)

NTHAWI zambiri timanena kuti Ufumu wa Mulungu wokha ndi umene udzathetse mavuto athu onse ndipo timagwiritsa ntchito Baibulo pothandiza anthu kudziwa zimenezi. Timalimbikitsidwanso tikaganizira zimene Ufumuwu udzatichitire. Koma funso ndi lakuti, Kodi timakhulupirira kwambiri kuti Ufumuwu udzakwaniritsa cholinga chake? Kodi n’chiyani chingatithandize kukhulupirira Ufumuwu?—Aheb. 11:1.

2 Mulungu anakhazikitsa Ufumu wa Mesiya pofuna kukwaniritsa cholinga chake. Popeza Yehova ndi woyenera kulamulira, Ufumuwu sudzalephera kuchita zimenezi. Pali mapangano osiyanasiyana amene anakhazikitsidwa pofuna kusonyeza zinthu zina zokhudza Ufumuwu. Amasonyeza Mfumu yake, anthu amene adzalamulire nawo komanso amene adzalamuliridwe. Yehova kapena Yesu ndi amene ankachita mapanganowa. Kuganizira mapanganowa kungatithandize kuti tizikhulupirira kwambiri Ufumu komanso tisamakayikire zoti Mulungu adzakwaniritsa cholinga chake.—Werengani Aefeso 2:12.

3. Kodi tikambirana chiyani m’nkhaniyi komanso yotsatira?

 3 M’nkhaniyi komanso yotsatira tikambirana mapangano akuluakulu okwana 6 okhudza Ufumu umene Yesu Khristu wapatsidwa. Mapangano ake ndi awa, (1) pangano la Abulahamu, (2) pangano la Chilamulo, (3) pangano la Davide, (4) pangano la wansembe ngati Melekizedeki, (5) pangano latsopano ndiponso (6) pangano la Ufumu. Tiona kugwirizana pakati pa mapanganowa ndi Ufumu komanso mmene mapanganowo akuthandizira kuti cholinga cha Mulungu chikwaniritsidwe.—Onani tchati chakuti “ Zimene Mulungu Akuchita Pokwaniritsa Cholinga Chake.”

MULUNGU ANALONJEZA NJIRA YOKWANIRITSIRA CHOLINGA CHAKE

4. Malinga ndi buku la Genesis, kodi Mulungu ankafuna zinthu ziti?

4 Yehova analenga dziko lokongolali kuti anthu azikhalamo ndipo buku la Genesis limatchula zinthu zitatu zimene ankafuna. Zinthu zake ndi izi: (1) Kulenga anthu m’chifanizo chake, (2) kuti anthu olungama adzaze dziko lapansi komanso kulikonza kuti likhale Paradaiso ndiponso (3) kuti anthuwo asadye zipatso za mtengo wodziwitsa chabwino ndi choipa. (Gen. 1:26, 28; 2:16, 17) Zinthu zitatuzi zinali zokwanira ndipo anthu ankafunika kungotsatira ziwiri zomalizirazo kuti cholinga cha Mulungu chikwaniritsidwe. Koma kodi chinachitika n’chiyani kuti mapangano afunike?

5, 6. (a) Kodi Satana anachita zotani pofuna kusokoneza cholinga cha Mulungu? (b) Kodi Yehova anatani Satana atamutsutsa m’munda wa Edeni?

5 Mavuto amene Satana Mdyerekezi anayambitsa ndi amene anachititsa kuti mapangano afunike. Satana ankafuna kusokoneza cholinga cha Mulungu. Kuti achite zimenezi, anaona kuti chidule chake n’kukopa anthu kuti asamvere lamulo limene Mulungu anawapatsa. Iye ananyengerera Hava kuti asamvere lamulo la Mulungu lokhudza mtengo wodziwitsa chabwino ndi choipa. (Gen. 3:1-5; Chiv. 12:9) Pochita zimenezi, Satana anatsutsa zoti Mulungu ndi woyenera kulamulira zimene analenga. Pa nthawi ina, Satana anatsutsanso zoti anthu amatumikira Mulungu ndi zolinga zabwino.—Yobu 1:9-11; 2:4, 5.

6 Kodi Yehova anachita chiyani Satana atamutsutsa mu Edeni? Iye ananena ulosi wofunika kwambiri womwe umatchedwa lonjezo la mu Edeni. Mu ulosiwu analonjeza zimene adzachite pokwaniritsa cholinga chake. N’zoona kuti akanathetsa vutolo popha Satana ndiponso Adamu ndi Hava. Koma anaona kuti kuchita zimenezi si nzeru chifukwa chakuti cholinga chake choti dzikoli lidzaze ndi ana a anthuwo chikanalephereka.—Werengani Genesis 3:15.

7. Kodi lonjezo la mu Edeni linasonyeza kuti njoka ndi mbewu yake zidzawathera bwanji?

7 Mu lonjezo la mu Edeni, Yehova anasonyeza kuti adzawononga njoka ndi mbewu yake. Njokayo ikuimira Satana Mdyerekezi ndipo mbewu yake ikuimira aliyense amene ali ku mbali ya Satana potsutsa ulamuliro wa Mulungu. Yehova anapatsa mbewu ya mkazi wake wakumwamba udindo wowononga adani onse. Choncho lonjezo la mu Edeni linanena zinthu zingapo. Linasonyeza kuti Satana, yemwe anayambitsa mavuto mu Edeni, adzawonongedwa ndipo mavuto onse adzatha. Linasonyezanso njira imene Mulungu adzagwiritsire ntchito pochita zimenezi.

8. Kodi tikudziwa zotani pa nkhani ya mkazi komanso mbewu yake?

8 Kodi mbewu ya mkaziyo ndi ndani? Popeza Satana Mdyerekezi ndi mzimu, mbewu  yoti idzamuwononge iyenera kukhalanso yauzimu osati yapadzikoli. (Aheb. 2:14) Izi zikusonyeza kuti mkazi amene angabereke mwanayu ayenera kukhalanso wauzimu. N’zoona kuti mbewu ya njoka inayamba kuchuluka mwamsanga. Koma panapita zaka pafupifupi 4,000 kuchokera pamene Yehova anapereka lonjezoli, kuti mbewu ya mkaziyu idziwike. Yehova anachita mapangano angapo othandiza anthu kuzindikira mbewuyi komanso kudziwa njira imene adzagwiritse ntchito pothetsa mavuto amene Satana anayambitsa.

PANGANO LOTITHANDIZA KUDZIWA MBEWU YA MKAZI

9. Kodi Yehova anachita pangano lotani ndi Abulahamu, nanga linayamba liti kugwira ntchito?

9 Patapita zaka pafupifupi 2,000 kuchokera pamene lonjezo la mu Edeni linaperekedwa, Yehova anauza Abulahamu kuti achoke mumzinda wa Uri ku Mesopotamiya n’kupita ku Kanani. (Mac. 7:2, 3) Yehova anati: “Tuluka m’dziko lako, pakati pa abale ako, ndi kusiya nyumba ya bambo ako. Upite kudziko limene ndidzakusonyeza. Ine ndidzatulutsa mtundu waukulu mwa iwe. Ndidzakudalitsa ndi kukuza dzina lako, ndipo iwe ukhale dalitso kwa ena. Odalitsa iwe ndidzawadalitsa, ndipo otemberera iwe ndidzawatemberera. Mabanja onse a padziko lapansi adzapeza madalitso chifukwa cha iwe.” (Gen. 12:1-3) M’Baibulo, amenewa ndi malo oyamba ofotokoza pangano limene Yehova Mulungu anachita ndi Abulahamu lomwe limatchedwa pangano la Abulahamu. Sitikudziwa nthawi yeniyeni imene Yehova anachita panganoli ndi Abulahamu. Koma linayamba kugwira ntchito mu 1943 B.C.E. pamene Abulahamu anawoloka mtsinje wa Firate. Pa nthawiyi n’kuti ali ndi zaka 75.

10. (a) Kodi Abulahamu anasonyeza bwanji kuti ankakhulupirira kwambiri malonjezo a Mulungu? (b) Kodi ndi zinthu ziti zokhudza mbewu ya mkazi zimene Yehova ankaulula pang’onopang’ono?

 10 Yehova anabwereza lonjezoli kwa Abulahamu maulendo angapo ndipo ankafotokozanso zinthu zina. (Gen. 13:15-17; 17:1-8, 16) Abulahamu anasonyeza kuti ankakhulupirira kwambiri malonjezo a Mulungu polola kuti apereke mwana wake monga nsembe. Zitatero, Yehova anamutsimikizira za pangano lija ndipo anafotokoza zinthu zina zokhudza lonjezo lakelo. (Werengani Genesis 22:15-18; Aheberi 11:17, 18.) Pangano la Abulahamu litayamba kugwira ntchito, Yehova ankaulula mwapang’onopang’ono zinthu zina zokhudza mbewu ya mkazi. Ananena kuti mbewuyo idzachokera m’banja la Abulahamu, idzakhala anthu ambiri, idzalamulira, idzawononga adani onse komanso idzadalitsa anthu ambiri.

Abulahamu anasonyeza kuti ankakhulupirira kwambiri malonjezo a Mulungu (Onani ndime 10)

11, 12. (a) Kodi Malemba anasonyeza bwanji kuti pangano la Abulahamu lidzakwaniritsidwa m’njira ina yaikulu? (b) Kodi zimenezi zidzathandiza bwanji anthu?

11 N’zoona kuti pangano la Abulahamu linakwaniritsidwa pamene Aisiraeli analowa m’Dziko Lolonjezedwa. Koma Malemba anasonyeza kuti panganoli lidzakwaniritsidwanso m’njira ina yaikulu. (Agal. 4:22-25) Pofotokoza za njira yachiwiriyi, Paulo anasonyeza kuti Khristu ndi mbali yoyamba ya mbewu ya Abulahamu ndipo odzozedwa okwana 144,000 ndi mbali yachiwiri ya mbewuyi. (Agal. 3:16, 29; Chiv. 5:9, 10; 14:1, 4) Ndiyeno mkazi wotchulidwa mu lonjezo la mu Edeni akuimira mbali yakumwamba ya gulu la Yehova ndipo amatchedwa “Yerusalemu wam’mwamba.” (Agal. 4:26, 31) Mogwirizana ndi zimene Mulungu analonjeza m’pangano la Abulahamu, anthu adzapeza madalitso chifukwa cha mbewu ya mkazi.

12 Pangano la Abulahamu lili ngati lumbiro lotsimikizira kuti Ufumu wa Mulungu udzalamuliradi. Limatsimikiziranso kuti Mfumu yake limodzi ndi anthu ena adzalandiradi Ufumuwo. (Aheb. 6:13-18) Kodi panganoli lidzagwira ntchito mpaka liti? Lidzagwira ntchito mpaka pamene Ufumu wa Mesiya udzawononge adani onse a Mulungu ndipo anthu onse padzikoli adzadalitsidwa. (1 Akor. 15:23-26) Koma lemba la Genesis 17:7 limanena kuti “lidzakhala pangano mpaka kalekale.” Zili choncho chifukwa chakuti madalitso amene anthuwo adzalandire adzakhala osatha. Pangano la Abulahamu limasonyeza kuti Yehova watsimikiza kukwaniritsa cholinga chake choti ‘dzikoli lidzaze’ ndi anthu olungama.—Gen. 1:28.

PANGANO LOTSIMIKIZIRA KUTI UFUMU SUDZATHA

13, 14. Kodi pangano la Davide limatitsimikizira chiyani pa nkhani ya Ufumu wa Mesiya?

13 Lonjezo la mu Edeni ndiponso pangano la Abulahamu zimatithandiza kudziwa kuti Ufumu wa Mesiya wakhazikitsidwa potsatira mfundo zachilungamo za Mulungu. (Sal. 89:14) Koma kodi Ufumuwu udzayamba kuchita zachinyengo m’tsogolomu moti udzafunika kusinthidwa? Pali pangano lina limene likutitsimikizira kuti zimenezi sizidzachitika.

14 Pangano lake ndi pangano la Davide. (Werengani 2 Samueli 7:12, 16.) Yehova anachita pangano ndi Davide pamene iye ankalamulira ku Yerusalemu ndipo anamulonjeza kuti Mesiya adzachokera m’banja lake. (Luka 1:30-33) Choncho Yehova anasonyeza kuti munthu wochokera m’banja la Davide adzakhala “woyenerera mwalamulo” kukhala Mfumu ya Ufumu wa Mesiya. (Ezek. 21:25-27) Ufumu wa Davide “udzakhazikika mpaka kalekale” kudzera mwa Yesu. Pajanso Baibulo limanena kuti: “Mbewu yake [ya  Davide] idzakhala mpaka kalekale, ndipo mpando wake wachifumu udzakhala ngati dzuwa.” (Sal. 89:34-37) Choncho pangano la Davide limatitsimikizira kuti Ufumu wa Mesiya sudzayamba kuchita zinthu mwachinyengo komanso zimene udzachite zidzathandiza anthu mpaka kalekale.

PANGANO LOSONYEZA KUTI PADZAKHALA WANSEMBE

15-17. (a) Kodi mbewu ya mkazi inafunika kutumikiranso pa udindo uti ndipo n’chifukwa chiyani? (b) Kodi ndi pangano liti limene linachititsa kuti zimenezi zitheke?

15 Taona kuti mapangano amene Yehova anachita ndi Abulahamu komanso Davide anasonyeza kuti mbewu ya mkazi idzalamulira mu Ufumu. Koma udindo wokhawu si wokwanira kuti anthu a mitundu yonse adalitsidwe. Tikutero chifukwa chakuti anthu onse angadalitsidwe pokhapokha ngati atamasulidwa ku uchimo n’kukhala m’banja la Yehova. Choncho mbewuyo inayenera kutumikiranso pa udindo wa wansembe. Kuti zimenezi zitheke, Yehova anachita pangano la wansembe ngati Melekizedeki.

16 Zimene Yehova anauza Davide zinasonyeza kuti iye adzachita pangano ndi Yesu ndipo panganolo lidzakhala ndi zolinga ziwiri. Choyamba ndi kukhala ‘kudzanja lamanja la Mulungu’ mpaka nthawi yokagonjetsa adani ake. Chachiwiri ndi kukhala “wansembe mpaka kalekale, monga mwa unsembe wa Melekizedeki.” (Werengani Salimo 110:1, 2, 4.) Kodi mawu oti “monga mwa unsembe wa Melekizedeki” akutanthauza chiyani? Kalekalelo, ana a Abulahamu asanalowe m’Dziko Lolonjezedwa, Melekizedeki anali mfumu ya Salemu komanso “wansembe wa Mulungu Wam’mwambamwamba.” (Aheb. 7:1-3) Iye anasankhidwa mwachindunji ndi Yehova kuti akhale wansembe. M’Malemba Achiheberi, Melekizedeki yekha ndi amene anali mfumu komanso wansembe. Baibulo silinena za wansembe amene iye anamulowa m’malo kapena amene anadzalowa m’malo mwake. Choncho tingati anali “wansembe kwamuyaya.”

17 Pogwiritsa ntchito panganoli, Yehova anasankha Yesu kuti akhale “wansembe mpaka muyaya monga mwa unsembe wa Melekizedeki.” (Aheb. 5:4-6) Izi zikutsimikizira kuti Yehova adzagwiritsa ntchito Ufumu wa Mesiya kuti akwaniritse cholinga chimene anali nacho polenga anthu padziko lapansi ndipo zimenezi sizidzalephereka.

MAPANGANO AMATITHANDIZA KUKHULUPIRIRA UFUMU

18, 19. (a) Kodi mapangano amene takambiranawa amasonyeza chiyani pa nkhani ya Ufumu? (b) Kodi tidzakambirana funso liti m’nkhani yotsatira?

18 Taona kuti mapangano amene takambiranawa amanena zinthu zokhudza Ufumu wa Mesiya ndipo amatitsimikizira kuti Ufumuwu ndi wodalirika. Lonjezo limene Yehova anapereka mu Edeni limatitsimikizira kuti iye adzagwiritsa ntchito mbewu ya mkazi pokwaniritsa cholinga chake chokhudza anthu padzikoli. Pangano la Abulahamu linasonyeza banja limene mbewu ya mkazi idzachokera komanso udindo wake.

19 Pangano la Davide linasonyeza kuti mbali yoyamba ya mbewuyi idzachokera m’banja la Davide komanso limapatsa mbewuyi mphamvu yolamulira dziko lonse mpaka kalekale. Pangano la wansembe ngati Melekizedeki linasonyeza kuti mbewuyo idzatumikiranso monga wansembe. Komatu Yesu sadzagwira yekha ntchito yochotsa uchimo. Pali anthu enanso amene asankhidwa kuti akhale mafumu ndi ansembe. Kodi anthuwo ndi ochokera kuti? Tidzakambirana zimenezi m’nkhani yotsatira.