Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Mudzakhala Ufumu wa Ansembe’

‘Mudzakhala Ufumu wa Ansembe’

“Inuyo mudzakhala ufumu wanga wa ansembe ndi mtundu wanga woyera.”—EKS. 19:6.

1, 2. N’chifukwa chiyani mbewu ya mkazi inkafunika kutetezedwa?

ULOSI woyamba m’Baibulo umatithandiza kwambiri kumvetsa zimene Mulungu akuchita pokwaniritsa cholinga chake. Ponena ulosiwu mu Edeni, Yehova analonjeza kuti: “Ndidzaika chidani pakati pa iwe [Satana] ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbewu yako ndi mbewu yake.” Kodi Mulungu ananena kuti chidanicho chidzakhala chachikulu bwanji? Iye anati: “Mbewu ya mkaziyo idzaphwanya mutu wako [wa Satana], ndipo iwe udzaivulaza chidendene.” (Gen. 3:15) Mulungu analosera kuti chidanicho chidzakhala chachikulu kwambiri moti Satana adzachita zonse zimene angathe kuti awononge mbewu ya mkaziyo. Choncho mbewuyi inafunika kutetezedwa.

2 M’pake kuti wamasalimo anapemphera mofuula ponena za anthu a Mulungu kuti: “Taonani! Adani anu akuchita phokoso. Anthu odana nanu kwambiri atukula mitu yawo. Iwo amakumana mwachinsinsi kuti akambirane zochitira chiwembu anthu anu. Ndipo amakonzera chiwembu anthu anu obisika. Iwo anena kuti: ‘Bwerani tiwafafanize kuti asakhalenso mtundu, ndi kuti dzina la Isiraeli lisakumbukikenso.’” (Sal. 83:2-4) Choncho Mulungu  anayenera kuteteza banja limene mbewuyo idzachokere kuti lisawonongedwe kapena kuipitsidwa. Pofuna kuti zimenezi zitheke komanso kuti Ufumu wa Mesiya ukwaniritse cholinga chake, iye anachita mapangano.

PANGANO LOTETEZA MBEWU

3, 4. (a) Kodi pangano la Chilamulo linayamba liti kugwira ntchito ndipo Aisiraeli anavomera kuchita chiyani? (b) Kodi pangano la Chilamulo linathandiza bwanji Aisiraeli?

3 Ana a Abulahamu, Isaki ndi Yakobo anayamba kuchuluka ndipo anakhala mtundu wa Isiraeli. Ndiyeno Yehova anagwiritsa ntchito Mose pochita nawo pangano lapadera. Anawapatsa Chilamulo ndipo Aisiraeliwo anavomera kuti azitsatira Chilamulocho. Baibulo limati: “Ndiyeno [Mose] anatenga buku la pangano ndi kuwerengera anthuwo kuti amve. Zitatero anthuwo anati: ‘Zonse zimene Yehova wanena tidzachita zomwezo ndipo tidzamumvera.’ Pamenepo Mose anatenga magaziwo [a ng’ombe zimene ankapereka nsembe] ndi kuwaza anthuwo, ndipo anati: ‘Awa ndiwo magazi okhazikitsira pangano limene Yehova wapangana nanu mwa mawu onsewa.’”—Eks. 24:3-8.

4 Pangano la Chilamulo linayamba kugwira ntchito paphiri la Sinai mu 1513 B.C.E. Pangano limeneli linachititsa kuti Aisiraeli akhale mtundu wosankhidwa ndi Mulungu. Apa tsopano Yehova anali ngati ‘Woweruza wawo, Wowapatsa Malamulo komanso Mfumu yawo.’ (Yes. 33:22) Zimene zinachitikira Aisiraeli zimasonyeza kuti zinthu zimayenda bwino anthu akamatsatira mfundo za Mulungu koma zimasokonekera akasiya kuzitsatira. Chilamulo sichinkalola Aisiraeli kukwatirana ndi anthu a mitundu ina kapena kulambira milungu ina. Izi zinathandiza kuti ana a Abulahamu asasokonezedwe chifukwa chosakanikirana ndi mitundu ina kapena kulambira milungu yonyenga.—Eks. 20:4-6; 34:12-16.

5. (a) Kodi pangano la Chilamulo linapatsa Aisiraeli mwayi uti? (b) N’chifukwa chiyani Mulungu anakana Aisiraeli?

5 Chilamulo chinkanenanso kuti pazikhala ansembe oti azitumikira Aisiraeli. Ansembewo ankaimira gulu la ansembe oti adzatumikire anthu onse m’tsogolo m’njira yabwino kwambiri. (Aheb. 7:11; 10:1) Chifukwa cha panganoli, Aisiraeli anali ndi mwayi wapadera wokhala mafumu komanso ansembe. Kuti izi zitheke, ankafunika kumvera malamulo a Yehova. (Werengani Ekisodo 19:5, 6.) Koma Aisiraeliwo sanamvere Yehova ndipo anataya mwayiwu. M’malo molandira Mesiya, yemwe ndi mbali yoyamba ya mbewu ya Abulahamu, iwo anamukana. Izi zinachititsa kuti Mulungu awakanenso.

Cholinga cha pangano la Chilamulo sichinalephereke chifukwa cha kusamvera kwa Aisiraeli (Onani ndime 3 mpaka 6)

6. Kodi cholinga cha pangano la Chilamulo chinali chiyani?

6 Cholinga cha pangano la Chilamulo chinali kuteteza mbewu komanso kutsogolera anthu kwa Mesiya. Ngakhale kuti Aisiraeli sanakhulupirike kwa Yehova ndipo analephera kukhala  mafumu ndiponso ansembe, cholingachi sichinalephereke. Chinakwaniritsidwa pamene Khristu anabwera n’kudziwika bwinobwino. N’chifukwa chake Baibulo limati: “Khristu ndiye kutha kwa Chilamulo.” (Aroma 10:4) Komano funso n’kumati, Ndani tsopano anapatsidwa mwayi wokhala mafumu komanso ansembe? Yehova anachititsa kuti pakhale pangano loyambitsa mtundu watsopano.

MTUNDU WATSOPANO

7. Kodi Yehova analosera za chiyani kudzera mwa Yeremiya?

7 Kalekale pangano la Chilamulo lisanathe, Yehova anagwiritsa ntchito Yeremiya polosera kuti adzachita “pangano latsopano” ndi Aisiraeli. (Werengani Yeremiya 31:31-33.) Pangano limeneli ndi losiyana ndi pangano la Chilamulo chifukwa chakuti limathandiza anthu kukhululukidwa popanda kupereka nsembe za nyama. Kodi zimenezi zimatheka bwanji?

8, 9. (a) Kodi ndi zinthu ziti zimene zatheka chifukwa cha magazi a Yesu? (b) Kodi anthu amene ali m’pangano latsopano amapatsidwa mwayi wotani? (Onani chithunzi patsamba 13.)

8 Patapita zaka zambiri, Yesu anayambitsa mwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye pa Nisani 14, 33 C.E. Ponena za kapu ya vinyo, Yesu anauza ophunzira ake 11 okhulupirika kuti: “Kapu iyi ikutanthauza pangano latsopano pamaziko a magazi anga, amene adzakhetsedwa chifukwa cha inu.” (Luka 22:20) Mateyu analemba mawu a Yesuwa kuti: “Vinyoyu akuimira ‘magazi anga a pangano,’ amene adzakhetsedwa chifukwa cha anthu ambiri kuti machimo akhululukidwe.”—Mat. 26:27, 28.

9 Magazi a Yesu ndi amene anachititsa kuti pangano latsopano liyambe kugwira ntchito. Magaziwo amathandizanso kuti machimo akhululukidwe kwamuyaya. Koma Yesu sali m’pangano latsopanoli. Popeza iye alibe uchimo, safunika kukhululukidwa chilichonse. Ana a Adamu ndi amene angathandizidwe ndi magazi a Yesu. Yehova amagwiritsanso ntchito mzimu wake podzoza anthu ena kuti akhale ‘ana ake’ ndipo amakhala m’pangano limeneli. (Werengani Aroma 8:14-17.) Mulungu amaona odzozedwawo kuti ndi osalakwa ngati mmene amamuonera Mwana wake Yesu, yemwe sachimwa. Anthu amene ali m’panganoli amapatsidwa mwayi umene unakanika Aisiraeli wokhala mafumu ndi ansembe. Iwo adzakalamulira limodzi ndi Khristu. Ponena za anthu amenewa, mtumwi Petulo ananena kuti: “Inu ndinu ‘fuko losankhidwa mwapadera, ansembe achifumu, mtundu woyera, anthu odzakhala chuma chapadera, kuti mulengeze makhalidwe abwino kwambiri’ a amene anakuitanani kuchoka mu mdima kulowa m’kuwala kwake kodabwitsa.” (1 Pet. 2:9) Pangano latsopanoli ndi lofunika kwambiri chifukwa limathandiza ophunzira a Yesu kuti akhale mbali yachiwiri ya mbewu ya Abulahamu.

KODI PANGANO LATSOPANO LINAYAMBA LITI KUGWIRA NTCHITO?

10. (a) Kodi pangano latsopano linayamba liti kugwira ntchito? (b) N’chifukwa chiyani tikuyankha choncho?

10 Pangano latsopano silinayambe kugwira ntchito pamene Yesu analitchula pa mwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye. Tikutero chifukwa chakuti magazi a Yesu anayenera kukhetsedwa ndipo nsembe yake inayenera kuperekedwa kwa Yehova kumwamba kuti panganoli liyambe kugwira ntchito. Komanso panafunika kuti Akhristu amene ali m’panganoli adzozedwe ndi mzimu woyera. Choncho pangano latsopano linayamba kugwira ntchito pa Pentekosite mu 33 C.E. pamene ophunzira a Yesu anadzozedwa ndi mzimu woyera.

11. (a) Kodi pangano latsopano limagwirizanitsa bwanji Ayuda ndi anthu ena kuti akhale Isiraeli wauzimu? (b) Kodi anthu oyenera kukhala m’pangano latsopanoli ndi angati?

11 Kudzera mwa Yeremiya, Yehova ananeneratu kuti pangano la Chilamulo ‘lidzatha ntchito.’ Panganoli linatha ntchito pamene pangano  latsopano linayamba kugwira ntchito. (Aheb. 8:13) Ndiyeno pangano latsopanoli linagwirizanitsa Ayuda ndi anthu a mitundu ina, amene anali osadulidwa, kuti akhale ndi mwayi wokalamulira nawo mu Ufumu. Zili choncho chifukwa chakuti pa nthawiyo ‘mdulidwe wake unali wa mumtima osati wa malamulo olembedwa.’ (Aroma 2:29) Pamene Yehova anachita nawo pangano latsopano, zinali ngati ‘waika malamulo ake m’maganizo mwawo ndi kuwalemba m’mitima yawo.’ (Aheb. 8:10) Anthu oyenera kukhala m’pangano latsopanoli ndi okwana 144,000 ndipo iwo ali mu mtundu watsopano wotchedwa “Isiraeli wa Mulungu” kapena kuti Isiraeli wauzimu.—Agal. 6:16; Chiv. 14:1, 4.

12. Kodi pangano la Chilamulo likusiyana bwanji ndi pangano latsopano?

12 Kodi pangano la Chilamulo likusiyana bwanji ndi pangano latsopano? Pangano la Chilamulo linali pakati pa Yehova ndi Aisiraeli pomwe pangano latsopano lili pakati pa Yehova ndi Isiraeli wauzimu. Mose anali mkhalapakati wa pangano la Chilamulo koma mkhalapakati wa pangano latsopano ndi Yesu. Pangano la Chilamulo linkagwira ntchito chifukwa cha magazi a nyama pomwe pangano latsopano linayamba kugwira ntchito chifukwa cha magazi a Yesu. M’pangano la Chilamulo, Mose ndi amene ankatsogolera Aisiraeli pomwe m’pangano latsopano Yesu ndi Mutu wa mpingo ndipo amatsogolera Akhristu odzozedwa.—Aef. 1:22.

13, 14. (a) Kodi pangano latsopano likugwirizana bwanji ndi Ufumu? (b) N’chiyani chinafunika kuti Aisiraeli auzimu akalamulire ndi Khristu kumwamba?

13 Kodi pangano latsopano likugwirizana bwanji ndi Ufumu? Panganoli limathandiza kuti pakhale mtundu woyera umene uli ndi mwayi wodzakhala mafumu ndi ansembe mu Ufumu wakumwamba. Mtundu umenewu ndi mbali yachiwiri ya mbewu ya Abulahamu. (Agal. 3:29) Choncho tingati pangano latsopano limatsimikizira kuti pangano la Abulahamu lidzakwaniritsidwa.

14 Pangano latsopano limachititsa kuti pakhale Isiraeli wa Mulungu woti adzapatsidwe mwayi wokhala “olandira cholowa anzake a Khristu.” Koma panafunika pangano lina lovomereza odzozedwawo kuti akalamulire ndi Yesu monga mafumu ndi ansembe kumwamba. Tiyeni tsopano tikambirane za pangano limeneli.

PANGANO LOVOMEREZA KUTI ENA ALAMULIRE NDI KHRISTU

15. Tchulani pangano limene Yesu anachita ndi atumwi ake okhulupirika.

15 Yesu atayambitsa mwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye, anachita pangano ndi ophunzira ake okhulupirika. Pangano limeneli limatchedwa pangano la Ufumu. (Werengani Luka 22:28-30.) Mapangano amene takambirana aja ankakhala pakati pa Yehova ndi anthu ena koma pangano ili ndi la pakati pa Yesu ndi odzozedwa basi. Yesu ananena kuti akuchita nawo pangano ‘mmene Atate wake wachitira pangano la ufumu ndi iye.’ Apa Yesu ankanena za pangano limene Yehova anachita naye loti adzakhala “wansembe mpaka muyaya monga mwa unsembe wa Melekizedeki.”—Aheb. 5:5, 6.

16. Kodi pangano la Ufumu limavomereza odzozedwa kuti achite chiyani?

16 Atumwi 11 okhulupirikawa ‘anakhalabe ndi Yesu m’mayesero ake.’ Ndiyeno pangano la Ufumu linawatsimikizira kuti adzakhala ndi Khristu kumwamba n’kupatsidwa mipando yachifumu kuti alamulire monga mafumu komanso ansembe. Koma si atumwi 11 okhawo amene anapatsidwa mwayiwu. Yesu ataukitsidwa, anaonekera kwa Yohane m’masomphenya n’kunena kuti: “Wopambana pa nkhondo ndidzamulola kukhala nane pampando wanga wachifumu, monga mmene ine ndinakhalira ndi Atate wanga pampando wawo wachifumu  nditapambana pa nkhondo.” (Chiv. 3:21) Choncho Akhristu odzozedwa onse okwana 144,000 ali m’pangano la Ufumuli. (Chiv. 5:9, 10; 7:4) Pangano limeneli limawavomereza kuti akalamulire ndi Khristu kumwamba. Zili ngati mkazi wakwatiwa ndi mfumu ndipo tsopano akhoza kumalamulira limodzi. Paja Malemba amati odzozedwa ali ngati “mkwatibwi” wa Khristu kapena “namwali woyera” amene adzakwatiwe ndi Khristu.—Chiv. 19:7, 8; 21:9; 2 Akor. 11:2.

TIZIKHULUPIRIRA KWAMBIRI UFUMU WA MULUNGU

17, 18. (a) Fotokozani mwachidule mapangano okhudza Ufumu amene takambirana. (b) N’chifukwa chiyani tiyenera kukhulupirira kwambiri Ufumu wa Mulungu?

17 Mapangano amene takambirana m’nkhani ziwirizi akufotokoza zinthu zina zokhudza Ufumu. (Onani tchati chakuti “Zimene Mulungu Akuchita Pokwaniritsa Cholinga Chake,” chomwe chili m’nkhani yapitayi) Mapanganowa akutitsimikizira kuti Ufumu wa Mulungu udzakwaniritsa cholinga chake. Choncho tiyenera kukhulupirira kwambiri kuti Mulungu adzagwiritsa ntchito Ufumu wa Mesiya kuti akwaniritse cholinga chake chokhudza anthu padziko lapansi.—Chiv. 11:15.

Yehova agwiritsa ntchito Ufumu wa Mesiya kuti akwaniritse cholinga chake padzikoli (Onani ndime 15 mpaka 18)

18 Palibe chifukwa chotichititsa kukayikira kuti Ufumuwu udzabweretsa madalitso osatha kwa anthu. Choncho tiyeni tizilalikira molimba mtima komanso mwakhama kuti Ufumu wa Mulungu wokha ndi umene udzathetse mavuto athu onse.—Mat. 24:14.