Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Anadzipereka ndi Mtima Wonse ku Taiwan

Anadzipereka ndi Mtima Wonse ku Taiwan

M’BALE wina dzina lake Choong Keon ndi mkazi wake Julie, amene panopa ali ndi zaka zoposa 30, anasamukira ku Taiwan. Zaka 5 zapitazo, ankachita upainiya wokhazikika mumzinda wa Sydney ku Australia. M’baleyo anati: “Ku Australia tinali pa ntchito ndipo tinkakhala ndi moyo wabwino. Nyengo inali yabwino komanso moyo unali wosavuta. Tinkasangalalanso kukhala pafupi ndi achibale ndiponso anzathu.” Komabe iwo ankaona kuti akanatha kuchita zambiri potumikira Yehova koma ankaopa kusintha moyo wawo.

Pa msonkhano wachigawo mu 2009, anamva nkhani ina imene inawakhudza kwambiri. Wokamba nkhaniyo ankalankhula makamaka kwa anthu amene akanatha kuwonjezera zimene ankachita mu utumiki. Iye anati: “Taganizirani chitsanzo ichi: Woyendetsa galimoto angathe kuikhotetsera kumanja kapena kumanzere kokha ngati galimotoyo ikuyenda. Nayenso Yesu angatitsogolere kuti tiwonjezere utumiki wathu pokhapokha ngati ifeyo tayamba kale kuyesetsa kukwaniritsa cholinga chathucho.” * M’baleyo ndi mkazi wake anamva ngati wokamba nkhaniyo akulankhula kwa iwowo. Pa msonkhanowo banja lina limene likuchita umishonale ku Taiwan linafunsidwanso. Amishonalewo anafotokoza zinthu zosangalatsa zimene amakumana nazo mu utumiki komanso kuti ku Taiwan kukufunikabe ofalitsa ambiri. Choong Keon ndi Julie anamvanso ngati akulankhula kwa iwowo.

Julie anati: “Msonkhanowu utatha, tinapempha Yehova kuti atithandize kulimba mtima n’kusamukira ku Taiwan.” Ananenanso kuti: “Koma tinkachitabe mantha. Tinkamva ngati kamwana kamene kakufuna kudumphira padziwe lakuya.” Koma lemba la Mlaliki 11:4 ndi limene linawathandiza kuti asiye kukayikakayika. Lembali limati: “Woyang’ana mphepo sadzabzala mbewu, ndipo woyang’ana mitambo sadzakolola.” Mwamuna wake anati: “Tinaganiza zoyamba ‘kubzala ndi kukolola’ osati ‘kumangoyang’ana.’” Iwo anaipempherera nkhaniyi  mobwerezabwereza, kuwerenga mbiri ya amishonale osiyanasiyana komanso kulemberana maimelo ndi anthu amene anasamukira ku Taiwan. Kenako anagulitsa magalimoto awo ndi katundu wina ndipo pambuyo pa miyezi itatu anasamukira ku Taiwan.

ANAONA KUTI KULALIKIRA N’KOSANGALATSA

Panopa, abale ndi alongo oposa 100 ochokera m’mayiko osiyanasiyana akutumikira ku Taiwan m’madera amene kulibe ofalitsa ambiri. Iwo ndi ochokera ku Australia, Britain, Canada, France, Japan, Korea, Spain ndi ku United States, ndipo ndi azaka za pakati pa 21 ndi 73. M’gululi muli alongo osakwatiwa oposa 50. Kodi n’chiyani chalimbitsa mtima abale ndi alongowa kuti asamukire ku Taiwan? Tiyeni tione.

Laura

Laura, yemwe ndi mlongo wosakwatiwa wochokera ku Canada, akuchita upainiya chakumadzulo kwa dziko la Taiwan. Zaka 10 zapitazo, iye sankakonda kulalikira. Laura anati: “Sindinkalalikira kwambiri choncho sindinkasangalala ndi utumiki.” Kenako anzake anamupempha kuti apite nawo ku Mexico kukalalikira kwa mwezi umodzi. Mlongoyu anati: “Apa m’pamene ndinalalikira kwa nthawi yaitali ndipo ndinadabwa kuona kuti kulalikira n’kosangalatsa kwambiri.”

Izi zinachititsa kuti Laura ayambe kuganizira zosamukira mumpingo wa chilankhulo china ku Canada. Iye anayamba kuphunzira Chitchainizi n’kumasonkhana m’kagulu ka chilankhulochi. Ankafunitsitsa kusamukira ku Taiwan ndipo zimenezi zinatheka mu September 2008. Laura anati: “Zinanditengera chaka chathunthu kuti ndiyambe kuzolowera moyo wakuno koma panopa sindifunanso kubwerera ku Canada.” Kodi panopa mlongoyu amamva bwanji akamalalikira? Iye anati: “Kulalikira n’kosangalatsa kwambiri. Ukamaona anthu akusintha moyo wawo chifukwa chophunzira Baibulo komanso kudziwa Yehova, umasangalala kwambiri. Zoterezi zikumachitikachitika ku Taiwan kuno ndipo ndikusangalala kwabasi.”

 VUTO LOSADZIWA CHILANKHULO

Brian ndi Michelle

Brian ndi mkazi wake Michelle ali ndi zaka zoposa 30 ndipo anasamuka ku United States kupita ku Taiwan zaka 8 zapitazo. Koma poyamba ankaona kuti sakuthandiza anthu bwinobwino mu utumiki. Ndiyeno m’bale amene wakhala mmishonale kwa nthawi yaitali anawauza kuti: “Muyenera kukumbukira kuti ngati mwangopereka kapepala kwa munthu wina ndiye kuti mwathandiza kwambiri mu utumiki. N’kutheka kuti ndi nthawi yoyamba kuti munthuyo amve za Yehova.” Zimenezi zinathandiza kwambiri Brian ndi Michelle kuti asataye mtima. M’bale wina anawauza kuti: “Kuti musakhumudwe pophunzira Chitchainizi, musamaganizire zimene mwakwanitsa kuphunzira pambuyo pa tsiku lililonse koma pambuyo pa msonkhano wadera uliwonse.” Panopa Brian ndi Michelle akuchita bwino polankhula Chitchainizi ndipo amaphunzitsa mogwira mtima mu utumiki.

Kodi n’chiyani chingakulimbikitseni kuti musamukire kudziko lina n’kuyamba kuphunzira chilankhulo cha kumeneko? Yesetsani kukaona dziko limene mukufuna kusamukira. Mukafika muzipita ku misonkhano, kucheza ndi abale ndi alongo ndiponso kulowa nawo mu utumiki. Brian anati: “Mutaona kuti anthu ambiri akufuna kuphunzira Baibulo ndiponso kuti abale ndi alongo akulandirani bwino, mudzalimbikitsidwa kusamukira kudzikolo.”

KODI AMAPEZA BWANJI ZOFUNIKA PA MOYO?

Kristin ndi Michelle

Akhristu ambiri amene akuchita upainiya ku Taiwan amaphunzitsa anthu Chingelezi kuti azipeza kangachepe. Kristin ndi Michelle amagulitsa nsomba. Kristin anati: “Sindinachitepo bizinezi imeneyi koma ndi imene ikundithandiza kuti ndizikhalabe kunoko.” Panopa, iye anapeza makasitomala odalirika. Amatha kupeza ndalama zokwanira komanso kukhala ndi nthawi yolalikira kuti asodze anthu.

“MUZISANGALALA PAMENE MUKUYESETSA KUKWANIRITSA ZOLINGA ZANU”

William ndi mkazi wake Jennifer anasamuka ku United States kupita ku Taiwan zaka 7 zapitazo. William anati: “Nthawi zina ndimatopa chifukwa chakuti ndikuphunzira chilankhulo, kuchita upainiya, kutumikira mumpingo komanso kufunafuna tindalama kuti ndisamalire banja langa.” Koma amakhalabe osangalala chifukwa chakuti zolinga zawo zimakhala zoti angazikwanitse. Mwachitsanzo, sakhumudwa akaona kuti akuchedwa kudziwa bwino Chitchainizi. Amadziwa kuti azikwanitsa mwapang’onopang’ono.

Kristin ndi Michelle

William amakumbukira zimene woyang’anira dera wina anamuuza. Anati: “Muzisangalala pamene mukuyesetsa kukwaniritsa zolinga zanu osati pokhapokha ngati mwazikwaniritsa.” Apa ankatanthauza kuti munthu akakhala ndi cholinga, azisangalala ndi zimene akuchita pofuna kukwaniritsa cholingacho. William ananena kuti mawuwa anawathandiza kwambiri kukhala ololera, kumvera malangizo a akulu a kumeneko komanso kusintha zina ndi zina kuti zinthu ziziwayendera potumikira m’dzikolo. Iye anati malangizowa anawathandizanso kuti azisangalala poona malo okongola a ku Taiwan.

Mlongo wina wosakwatiwa dzina lake Megan anasamukanso ku United States kupita ku Taiwan. Nayenso akuyesetsa kukhala wosangalala pamene akuphunzira Chitchainizi. Kumapeto kwa mlungu uliwonse amapita ndi anzake kukalalikira kudoko lotchedwa Kaohsiung. Limeneli ndi doko lalikulu kwambiri ku Taiwan ndipo amasangalala akamalalikira kumeneku. Megan amalalikira nawo m’sitima zam’madzi kwa asodzi ochokera ku Bangladesh, India, Indonesia, Philippines, Thailand, ndi ku Vanuatu. Iye anati: “Popeza asodziwa sachedwa padokoli, timangoyambiratu phunziro. Kuti ndiphunzire ndi ambiri, ndimakambirana nawo m’magulu a anthu 4 kapena 5.” Kodi Megan wafika pati pa  nkhani yophunzira Chitchainizi? Iye anati: “Ndimafuna nditachiphunzira mwamsanga koma ndimakumbukira zimene m’bale wina anandiuza. Anati: ‘Iwe uzingochita zonse zimene ungathe, kotsalako usiyire Yehova.’”

Megan

MOYO WOTETEZEKA, WOSALIRA ZAMBIRI NDIPONSO WOSANGALATSA

Mlongo wina wosakwatiwa dzina lake Cathy, anasamuka ku Britain kupita ku Taiwan. Choyamba anafufuza dziko limene angakakhale motetezeka. Anaipempherera nkhaniyi n’kulembera makalata kumaofesi a nthambi a m’mayiko osiyanasiyana kuti adziwe mavuto amene mlongo wosakwatiwa angakumane nawo m’mayikowo. Atalandira mayankho, anaona kuti ku Taiwan kuli bwino.

Mlongoyu anasamukira m’dzikoli mu 2004 ndipo pa nthawiyi anali ndi zaka 31. Iye akukhala moyo wosalira zambiri ndipo anati: “Ndinafufuza kwa abale ndi alongo kuti ndidziwe kumene ndingagule masamba ndi zipatso zotchipa. Zimene anandiuza zinandithandiza kuti ndisamawononge ndalama zambiri.” Pofotokoza zimene zimamuthandiza kuti azikhala moyo wosalira zambiri, Cathy anati: “Ndimapemphera kwa Yehova kuti andithandize kukhala wokhutira ndi chakudya changa komanso zovala zanga zomwe si zapamwamba. Ndimaona kuti Yehova akuyankha mapemphero anga. Akundithandiza kudziwa zinthu zofunika kwambiri ndiponso kuti ndisamalakelake zinthu zosafunika kwenikweni.” Iye ananenanso kuti: “Moyo wosalira zambiri umandisangalatsa chifukwa umandithandiza kuti ndiziganizira kwambiri zokhudza kutumikira Yehova.”

Cathy

Ngakhale kuti moyo wa Cathy ndi wosalira zambiri, pali zinthu zimene zimamusangalatsa. Mlongoyu anati: “M’dera limene ndimalalikira, anthu ambiri amafuna kumva uthenga wabwino. Zimenezi zimandisangalatsa kwabasi.” Pamene ankafika ku Taiwan, panali mipingo yachitchainizi iwiri yokha mumzinda umene ankachita upainiya. Koma panopa kuli mipingo 7. Cathy anati: “Kunena zoona, ndimasangalala koopsa ndikamaona kuti ndikugwira nawo ntchito yothandiza anthu ambiri kulowa m’gulu la Yehova.”

“NGAKHALE INEYO NDINKAFUNIKAKO”

Kodi Choong Keon ndi Julie, amene tawatchula kumayambiriro aja, zikuwayendera bwanji? M’baleyu ananena kuti poyamba ankadziona kuti ndi wosafunika kwenikweni mumpingo chifukwa chakuti sankadziwa bwino Chitchainizi. Koma umu si mmene abale akumeneko ankamuonera. Iye anati: “Ndinali mtumiki wothandiza, koma mpingo utagawidwa ndinapatsidwa zochita zambiri. Apa ndinayamba kumva kuti ndikuthandizadi dera limene kulibe ofalitsa okwanira.” Iye ananena, uku akumwetulira, kuti: “Ndinasangalala kwambiri kuona kuti ngakhale ineyo ndinkafunikako.” Panopa m’baleyu ndi mkulu ndipo mkazi wake anati: “Timamva bwino kuposa kale chifukwa tikuchita zambiri ndipo tikusangalala. Tinabwera kudzathandiza kunoko koma tikuona kuti ifeyo ndi amene tathandizidwa kwambiri. Tikuthokoza kwambiri kuti Yehova anatilola kudzatumikira kunoko.”

Anthu ogwira ntchito yokolola akufunikabe m’mayiko ambiri. Kodi inuyo mwatsala pang’ono kumaliza sukulu ndipo mukuganizira zoti muchite pa moyo wanu? Kodi simuli pa banja ndipo mukufuna kuchita zambiri m’gulu la Yehova? Kodi mukufuna kuthandiza anthu a m’banja lanu kuti achite zinthu zambiri zosangalatsa potumikira Yehova? Kodi mwapuma pa ntchito ndipo mukhoza kukathandiza anthu chifukwa choti mukudziwa zambiri? Dziwani kuti Yehova adzakudalitsani kwambiri ngati mungasamukire kudera limene kulibe ofalitsa ambiri.

^ ndime 3 Onani buku lakuti ‘Kuchitira Umboni Mokwanira za Ufumu wa Mulungu’ mutu 16 ndime 5 ndi 6.