Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Paulo Analalikira Msilikali Woteteza Mfumu

Paulo Analalikira Msilikali Woteteza Mfumu

Mu 59 C.E., asilikali achiroma anayenda mtunda wautali ndi akaidi n’kulowa mumzinda wa Roma kudzera pachipata chotchedwa Porta Capena. Paphiri lotchedwa Palatine panali nyumba ya Mfumu Nero. Mfumuyi inkatetezedwa ndi asilikali okhala ndi malupanga amene ankawabisa mkati mwa malaya akunja. * Kapitawo wa asilikali dzina lake Yuliyo anayenda ndi akaidiwa kudutsa bwalo la Aroma mpaka kukafika kuphiri la Viminal. Iwo anadutsa munda womwe unali ndi maguwa ambirimbiri a milungu ya Aroma ndipo anakafika kumalo a asilikali.

Chithunzi cha asilikali oteteza mfumu ichi ena amatichinachokera ku Arch of Claudius, ndipo anachipanga mu 51 C.E.

Mmodzi mwa akaidiwo anali mtumwi Paulo. Miyezi ingapo m’mbuyomo, pamene iye anali m’ngalawa, mngelo wa Mulungu anamuuza kuti: “Uyenera kukaima pamaso pa Kaisara.” (Mac. 27:24) Kodi pa nthawiyi Paulo anali atatsala pang’ono kuchitadi zimenezi? Paulo ayenera kuti ankati akayang’ana likulu la mzinda wa Ufumu wa Roma, ankakumbukira mawu amene Ambuye Yesu anamuuza pa Nsanja ya Antoniya ku Yerusalemu. Anamuuza kuti: “Limba mtima! Pakuti wandichitira umboni mokwanira mu Yerusalemu, ndipo ukandichitiranso umboni ku Roma.”—Mac. 23:10, 11.

Mwina Paulo anaima n’kuyang’ana malo ena pamene pankakhala asilikali. Malo amenewa anali mumpanda wachitetezo wa njerwa zofiira komanso panali nsanja. Mkati mwake munali nyumba za asilikali oteteza mfumu  omwe ankagwiranso ntchito ngati apolisi. Panali magulu 12 * a asilikali oteteza mfumu ndiponso magulu ena amene ankakhala kumeneku. Kumalowa kunkakhala masauzande a asilikali ndipo ena anali oyenda pa mahatchi. Malowa ankangosonyezeratu kuti ufumuwu unali wamphamvu. Popeza asilikali oteteza mfumu ankayang’anira akaidi otumizidwa kuchokera m’zigawo zina, Yuliyo anatsogolera gulu lake la akaidi kudutsa pageti lina lalikulu. Apa tsopano anali atafika ndi akaidi amene anayenda nawo kwa miyezi ingapo pa ulendo wovuta kwambiri.—Mac. 27:1-3, 43, 44.

MTUMWI PAULO ANALALIKIRA “POPANDA CHOLETSA”

Mulungu anali atauza Paulo kuti anthu onse amene anali m’ngalawa imene inasweka apulumuka. Pa ulendowu, Paulo analumidwa ndi njoka yapoizoni koma sanafe. Atafika pachilumba cha Melita, iye anachiritsa odwala ndipo anthu anayamba kunena kuti iye anali mulungu. N’kutheka kuti asilikali oteteza mfumu, omwe ankakhulupirira zamatsenga, anamva nkhani zonsezi.

Paulo anali ataona kale abale a ku Roma amene ‘anabwera kudzamuchingamira ku Msika wa Apiyo ndi ku Nyumba Zitatu za Alendo.’ (Mac. 28:15) Popeza anali mkaidi, kodi akanakwanitsa bwanji kulalikira uthenga wabwino ku Roma? (Aroma 1:14, 15) Ena amanena kuti akaidiwa ankapita nawo kwa mkulu wa asilikali. Ngati zinalidi choncho, ndiye kuti Paulo anamupititsa kwa mkulu wa asilikali dzina lake Afranius Burrus. Munthu ameneyu ayenera kuti anali wachiwiri kwa mfumu. * Apatu zikuoneka kuti pa nthawiyi, Paulo sankalonderedwa ndi asilikali ambirimbiri koma msilikali woteteza mfumu mmodzi waudindo wapamwamba kwambiri. Iye ankaloledwa kupeza yekha malo okhala, kulandira alendo komanso kulalikira “popanda choletsa.”—Mac. 28:16, 30, 31.

PAULO ANALALIKIRA KWA ANTHU OTCHUKA NDI ANTHU WAMBA

Mmene mpanda wa malo a asilikali umaonekera masiku ano

Burrus ayenera kuti anafunsa kaye mtumwi Paulo mafunso asanamutumize kwa Nero. Mwina ankamufunsira kunyumba ya mfumu kapena kumalo a asilikali. Apa Paulo anapezerapo mwayi wolalikira “kwa anthu otchuka ndi kwa anthu wamba.” (Mac. 26:19-23) Kaya Burrus anapeza zotani pambuyo pomufunsa mafunso, chomwe tikudziwa n’chakuti anaona kuti Paulo sayenera kukhala kumalo a asilikaliwo. *

 Nyumba imene Paulo ankakhala iyenera kuti inali yaikulu bwino moti ankatha kulandira “akuluakulu a Ayuda” n’kumawalalikira. Ankalalikiranso kwa anthu amene ankabwera “mwaunyinji kumene iye anali kukhala.” Akaidi ena amene ankakhala kumalo a asilikali ankamva Paulo akuchitira umboni mokwanira kwa Ayuda powauza mfundo zokhudza Yesu komanso Ufumu wa Mulungu. Iye anachita zimenezi “kuyambira m’mawa mpaka madzulo.”—Mac. 28:17, 23.

Paulo ali m’ndende, asilikali ankamumva akuuza munthu zoti alembe m’makalata

Gulu la asilikali olondera mfumu linkasinthidwa tsiku lililonse likafika ola la 8. Izi zinkachititsa kuti asilikali olondera Paulo azisinthidwanso nthawi ndi nthawi. Pa zaka ziwiri zimene Paulo anali mkaidi, asilikali omulondera ankamumva akunena uthenga woti ulembedwe m’makalata opita kumipingo ya Aefeso, Afilipi, Akolose ndi Aheberi. Mwina anamuonanso akulemba yekha kalata yopita kwa Mkhristu wina dzina lake Filimoni. Pa nthawi imene anali kundende, Paulo ankaganiziranso za Onesimo amene poyamba anali kapolo koma n’kuthawa. Paulo anali ngati bambo wake ndipo anamulimbikitsa kuti abwerere kwa mbuye wake. (Filim. 10) N’zosakayikitsa kuti Paulo ankalalikiranso asilikali amene ankamuyang’anira. (1 Akor. 9:22) Mwina ankafunsa msilikali wina ntchito za zida zosiyanasiyana n’kuzigwiritsa ntchito m’fanizo lake labwino kwambiri.—Aef. 6:13-17.

 ‘ANALANKHULA MAWU A MULUNGU MOPANDA MANTHA’

Kumangidwa kwa Paulo kunathandiza kuti ‘uthenga wabwino upite patsogolo’ mpaka kufika kwa asilikali oteteza mfumu ndiponso anthu ena. (Afil. 1:12, 13) Anthu amene ankakhala kumalo a asilikali aja ankadziwana ndi mfumu, anthu a m’nyumba ya mfumu komanso anthu ena ambiri mu Ufumu wa Roma. M’nyumba ya mfumu munkakhala achibale a mfumu, atumiki ndiponso akapolo moti ena a iwo anadzakhala Akhristu. (Afil. 4:22) Abale a ku Roma anapeza mphamvu ‘zolankhula mawu a Mulungu mopanda mantha’ chifukwa chakuti Paulo ankalalikira molimba mtima.—Afil. 1:14.

Kaya zinthu zili bwanji pa moyo wathu, tikhoza kulalikira kwa anthu amene amabwera kumene tikukhala

Zimene Paulo anachita polalikira ku Roma zimatilimbikitsa pamene ‘tikulalikira mawu m’nthawi yabwino ndi m’nthawi yovuta.’ (2 Tim. 4:2) Mwachitsanzo, abale athu ena sayenda chifukwa chakuti ali m’malo osungira anthu okalamba, m’zipatala kapena ali m’ndende chifukwa cha chikhulupiriro chawo. Kaya zinthu zili bwanji pa moyo wathu, tikhoza kulalikira kwa anthu amene amabwera kumene tikukhalako. Tikamayesetsa kuchitira umboni pa mpata uliwonse umene tingapeze tidzaona tokha kuti “mawu a Mulungu samangika.”—2 Tim. 2:8, 9.

^ ndime 2 Onani bokosi lakuti “Asilikali Oteteza Mfumu a M’nthawi ya Nero.”

^ ndime 4 Gulu limodzi linkakhala ndi asilikali 1,000.

^ ndime 7 Onani bokosi lakuti “Kodi Sextus Afranius Burrus anali ndani?”

^ ndime 9 Tiberiyo Kaisara anatsekera Herode Agiripa kumalo amenewa mu 36 kapena mu 37 C.E., chifukwa chakuti ananena kuti Kaligula adzakhala mfumu. Kaligula atakhaladi mfumu anathokoza Herode pomupatsa ufumu.—Mac. 12:1.