Anali Wochokera M’banja la Kayafa
Nthawi zina, anthu ofukula za m’mabwinja amapeza zinthu zimene zimakhala ndi umboni wotsimikizira kuti munthu winawake wotchulidwa m’Baibulo analipodi. Mwachitsanzo, mu 2011 akatswiri a ku Israel anafalitsa nkhani imene inasonyeza zimenezi. Nkhani yake inali yonena za bokosi linalake losungiramo mafupa a anthu limene linakwiriridwa zaka 2,000 zapitazo.
Bokosi limeneli linali ndi mawu akuti: “Miriamu mwana wamkazi wa Yeshua mwana wa Kayafa wansembe wa Maaziya wa ku Beth ′Imri.” Mkulu wa ansembe wachiyuda amene anaweruza mlandu wa Yesu ndiponso kugamula kuti aphedwe anali Kayafa. (Yoh. 11:48-50) Wolemba mbiri wina, dzina lake Flavius Josephus, anamutchula kuti “Yosefe yemwenso ankadziwika kuti Kayafa.” Bokosi limeneli liyenera kuti linali la wachibale wake wina. Popeza bokosi lina limene analipeza m’mbuyomo linali ndi mawu onena za mkulu wa ansembeyu ndipo anamutchula kuti Yehosef bar Caiapha, kapena kuti Yosefe mwana wa Kayafa, *ndiye kuti Miriamu ayenera kuti anali m’bale wake wa Kayafa.
Malinga ndi zimene bungwe lina linanena (Israel Antiquities Authority), bokosi la mafupa a Miriamu linalandidwa kuchokera kwa anthu amene analiba kumanda enaake akale. Kafukufuku amene akatswiri ena anapanga komanso mawu amene anali pabokosipa anatsimikizira kuti bokosili linalidi la mafupa a Miriamu.
Bokosi la mafupa a Miriamu likutiuzanso kanthu kena. Limanena za “Maaziya” yemwe anali womaliza pa magulu 24 a nyumba za makolo a ansembe amene ankatumikira pakachisi ku Yerusalemu. (1 Mbiri 24:18) Bungwe lomwe lija linanenanso kuti mawu amene ali pabokosili amasonyeza kuti “Maaziya anali pachibale ndi banja la Kayafa.”
Bokosili lilinso ndi mawu akuti Beth ′Imri. Mawu amenewa angatanthauze zinthu ziwiri. Bungwe lija linanenanso kuti, “n’kutheka kuti Beth ′Imri ndi dzina la banja limene ansembe ankachokera. Ansembe amenewa anali ana a Imeri. Ena mwa anawo anali a m’banja la Maaziya.” (Ezara 2:36, 37; Neh. 7:39-42) “Apo ayi ndiye kuti [Beth ′Imri ndi] malo amene Miriamu kapena banja lake linachokera.” Kaya zoona n’ziti, mfundo ndi yakuti bokosi la mafupa a Miriamu ndi umboni woti Baibulo limanena za anthu komanso mabanja a anthu amene anakhalakodi.
^ ndime 3 Kuti mudziwe zambiri za bokosi la Kayafa onani nkhani yakuti, “Mkulu wa Ansembe Amene Anaphetsa Yesu” mu Nsanja ya Olonda ya January 15, 2006, tsamba 10-13.