Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Munayamba Mwadalitsidwapo Chifukwa Chopatsa?

Kodi Munayamba Mwadalitsidwapo Chifukwa Chopatsa?

Kodi Munayamba Mwadalitsidwapo Chifukwa Chopatsa?

MLONGO wina wokhulupirika wachikristu anali atatha zaka pafupifupi 50 akuchita utumiki wachikristu mosalekeza. Ngakhale kuti anali wofooka ndi ukalamba, mlongoyu ankafunitsitsa atapita ku Nyumba ya Ufumu yomwe inali itangomangidwa kumene. Mbale wina wachikristu anathandiza mlongoyu kuyenda, ndipo analoŵa m’Nyumba ya Ufumuyo ndiye anayenda pang’onopang’ono kulunjika chinthu chimene ankapitira kunyumbayi. Chinthu chake chinali bokosi la zopereka. Atafika pabokosipo iye anaponyamo ndalama yochepa imene anasunga kuti adzapereke n’cholinga choti ithandize pa Nyumba ya Ufumu yatsopanoyo. Ngakhale kuti sanathe kugwira nawo ntchito yomanga nyumbayo, iye ankafuna athandizepo.

Mwina mayi wachikristu ameneyu akukukumbutsani mayi winanso wokhulupirika, “mkazi wamasiye” amene Yesu anamuona akuponya tindalama tiŵiri tating’ono mosungiramo ndalama pakachisi. Sitinauzidwe kuti moyo wa mkaziyu unali wotani, koma masiku amenewo mkazi akakhala wopanda mwamuna ankakhala pa mavuto aakulu a zachuma. Ndithu, Yesu ayenera kuti anamumvera chisoni kwambiri mayiyu, chifukwa choti Yesuyo ankadziŵa bwinobwino mavuto amene mayiyu anali nawo. Posonyeza kuti mayiyu anali chitsanzo kwa ophunzira ake, iye anati mphatso yaing’ono yomwe iye anapereka inali “zonse anali nazo, inde moyo wake wonse.”​—Marko 12:41-44.

Kodi n’chifukwa chiyani mayi wosauka ngati mkazi wamasiyeyu anapereka nsembe yotere? N’zoonekeratu kuti chifukwa chake chinali chakuti iye anali munthu wodzipereka kwambiri kwa Yehova Mulungu, amene likulu lomulambirira linali kukachisi ku Yerusalemu. Ngakhale kuti sakanatha kuchita zinthu zochuluka, iye ankafuna kuthandiza kuti utumiki wopatulika upite patsogolo. Ndipo mosakayikira anasangalala kwambiri chifukwa chopereka zimene akanatha.

Kupatsa Pofuna Kuthandizira Ntchito ya Yehova

M’mbuyo monsemu, kupereka katundu kapena ndalama kwakhala mbali yofunika pa kulambira koyera, ndiponso kwakhala kukupangitsa anthu kusangalala kwambiri. (1 Mbiri 29:9) Mu Israyeli wakale zinthu zimene anthu ankapereka zinkagwira ntchito yokongoletsera kachisi komanso zinkathandizira kuyendetsera ntchito zonse zatsiku ndi tsiku zokhudzana ndi kulambira Yehova. Chilamulo chinanena kuti ana a Israyeli azipereka chakhumi pa zinthu zawo kuti zithandize Alevi, amene ankagwira ntchito za pakachisi. Koma nawonso Alevi ankafunika kupatsa Yehova chakhumi pa zinthu zimene alandira.​—Numeri 18:21-29.

Ngakhale kuti Akristu anamasulidwa ku malamulo a m’pangano la Chilamulo, mfundo yakuti atumiki a Mulungu azipereka zinthu pothandizira kulambira koona siinasinthe. (Agalatiya 5:1) Kuwonjezera apo, Akristu a m’zaka za 100 zoyambirira ankasangalala kwambiri kupereka zinthu pofuna kuthandiza abale awo osoŵa. (Machitidwe 2:45, 46) Mtumwi Paulo anakumbutsa Akristu kuti ayenera kukhala owoloŵa manja kwa ena monga mmenenso Mulungu anawapatsira iwowo zinthu zabwino mooloŵa manja. Iye analemba kuti: “Lamulira iwo achuma m’nthaŵi ino ya pansi pano, kuti asadzikuze, kapena asayembekezere chuma chosadziŵika kukhala kwake, koma Mulungu, amene atipatsa ife zonse kochulukira, kuti tikondwere nazo; kuti achite zabwino, nachuluke ndi ntchito zabwino, nakondwere kugaŵira ena, nayanjane; nadzikundikire okha maziko okoma ku nyengo ikudzayi, kuti akagwire moyo weniweniwo.” (1 Timoteo 6:17-19; 2 Akorinto 9:11) Zoonadi, kuchokera pa zimene anaona m’moyo wake, Paulo anatha kuchitira umboni kuti mawu a Yesu otsatiraŵa ndi oona. Mawu ake ndi akuti: “Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.”​—Machitidwe 20:35.

Kupatsa Kwachikristu Masiku Ano

Masiku ano, atumiki a Yehova akupitiriza kugwiritsa ntchito chuma chawo pothandizana iwo eni komanso pothandiza pantchito ya Mulungu. Ngakhale atumiki amene si olemera, nawonso amapereka malinga n’kupata kwawo. “Kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” amaona kuti wapatsidwa udindo ndi Yehova woonetsetsa kuti ndalama zonsezi zikugwiritsidwa ntchito moyenera. (Mateyu 24:45) Ndalama zimathandiza kuyendetsera maofesi a nthambi, kumasulira ndi kusindikiza mabaibulo ndiponso mabuku ofotokoza Baibulo, kukonzera misonkhano ikuluikulu yachikristu, kuphunzitsira ndi kutumizira atumiki oyendayenda ndi amishonale, kukonzera chithandizo pakaoneka tsoka, komanso zimathandiza pantchito zina zambiri zofunika. Tiyeni tione imodzi mwa ntchito za ndalama zimenezi, yomwe ndi ntchito yokonzera malo olambiriramo.

Mboni za Yehova zimasonkhana kangapo pamlungu m’Nyumba zawo za Ufumu n’cholinga chophunzira zinthu zauzimu komanso kucheza ndi Akristu anzawo. Komabe, m’mayiko ambiri, nkhani ya zachuma imapangitsa kuti Mboni za m’mayikowo zisathe kupeza ndalama zomangira Nyumba za Ufumu popanda kupatsidwa thandizo poyamba. Chifukwa cha izi, m’chaka cha 1999, Mboni za Yehova zinayamba ntchito yothandiza kumanga Nyumba za Ufumu m’mayiko osauka pogwiritsira ntchito ndalama zochoka m’mayiko olemera. Kuwonjezera pamenepo, antchito odzipereka ambirimbiri alola kugwiritsira ntchito nthaŵi yawo komanso luso limene ali nalo pantchitoyi m’mayiko ameneŵa, ndipo nthaŵi zambiri amakagwira ntchitoyi m’madera akutali ndi tauni. Panthaŵi yomanga nyumbayo, Mboni za m’deralo zimaphunzira ntchito yomanga nyumba ndiponso kukonzanso nyumbayo ikawonongeka, ndipo Thumba la Nyumba za Ufumu limathandiza kugulira zipangizo ndi katundu wofunika pantchitoyo. Mboni zimene panopa zikugwiritsa ntchito nyumba zatsopanozi zimayamikira kwambiri chifukwa chakuti okhulupirira anzawo anapereka nthaŵi yawo komanso ndalama zawo. Mboni zimene zikugwiritsa ntchito nyumbayo nazonso zimapereka ndalama mwezi ndi mwezi zothandiza kukonzera Nyumba ya Ufumu yatsopanoyo ikawonongeka penapake ndiponso zoti zithandizire kubwezeretsa ndalama zomwe zinagwiritsidwa ntchito pomanga nyumbayo. Izi zimathandiza kuti pamangidwe Nyumba za Ufumu zinanso.

Nyumba za Ufumu zimamangidwa motsatira kamangidwe kanyumba ka m’dera limene zilimo komanso pogwiritsa ntchito zipangizo zopezeka m’deralo. Nyumbazi sizokometseredwa monyanyira, koma ndi zokongola, zoyenererana ndi ntchito yake, ndiponso anthu amakhalamo motakasuka. Pamene ntchito yomangayi inkayamba mu 1999, anakonza zoti ichitike m’mayiko 40 amene si olemera. Koma tsopano ntchitoyi yawonjezedwa kuti ichitike m’mayiko okwana 116 otere, ndipo ikukhudza pafupifupi theka la mipingo yonse ya Mboni za Yehova padziko lonse. Nyumba za Ufumu zoposa 9,000 zamangidwa m’zaka zisanu zapitazi, potsatira dongosolo limeneli. Tinganene kuti tsiku lililonse kunkamangidwa nyumba zatsopano zisanu. Komabe, m’mayiko okwana 116 ameneŵa, mukufunikirabe Nyumba za Ufumu zina zatsopano zokwana 14,500. Tikukhulupirira kuti chifukwa cha madalitso a Yehova ndiponso kudzipereka komanso kuwoloŵa manja kwa Mboni za padziko lonse, tikhala ndi ndalama zokwanira zogwirira ntchito imeneyi.​—Salmo 127:1.

Nyumba za Ufumu Zimathandiza Kuti Chiŵerengero Chikwere

Kodi Mboni ndiponso ntchito yolalikira za Ufumu m’dera lomwe mwamangidwa nyumbayo zimakhudzidwa motani ndi ntchito yaikulu imeneyi? M’madera ambiri, Nyumba ya Ufumu yatsopano ikatha kumangidwa, chiŵerengero cha anthu ofika pamisonkhano chimakwera kwambiri. Chitsanzo chosonyeza zimenezi chikupezeka mu lipoti ili lochokera ku Burundi: “Nyumba ya Ufumu ikangotha kumangidwa imadzadza nthaŵi yomweyo. Mwachitsanzo, Nyumba ya Ufumu ina inamangidwa mogwirizana ndi mpingo wa anthu okwana 100 amene anali kufika pamisonkhano. Nyumba ya Ufumu yatsopanoyi mungathe kukwana bwinobwino anthu 150. Koma panthaŵi yomwe amatsiriza kuimanga, pamisonkhanopo panali kufika anthu 250.”

N’chifukwa chiyani anthu amawonjezeka chonchi? Chifukwa chimodzi n’chakuti anthu nthaŵi zina amakayikira magulu a ofalitsa Ufumu amene alibe malo enieni a misonkhano, moti mwina amangosonkhanana pamtengo kapena m’munda. M’dziko lina, anthu amaganizira kuti ochita ziwawa zosonyeza kudana ndi mafuko ena amachokera m’timagulu ting’onoting’ono tachipembedzo totereti, ndipo mwalamulo misonkhano yonse yachipembedzo imayenera kuchitikira m’nyumba yopembedzeramo.

Kukhala ndi nyumba zawozawo za misonkhano kumathandizanso Mboni za Yehova kusonyeza anthu a m’dera lawo kuti Mbonizo si ophunzira a mbusa winawake. Ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Zimbabwe inalemba kuti: “M’mbuyomu abale kuno ankasonkhana m’makomo mwawo, ndipo anthu m’deralo ankatchula mpingowo ndi dzina la mwini khomolo. Motero abalewo ankawatchula kuti ndi atchalitchi cha Auje. Koma tsopano zonsezi zikusintha chifukwa anthu akuona zikwangwani zolembedwa bwino pa Nyumba ya Ufumu iliyonse zakuti, ‘Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova.’”

Anthu Opatsa Mosangalala

“Mulungu akonda wopereka mokondwerera,” analemba motero mtumwi Paulo. (2 Akorinto 9:7) Ndi zoona kuti zopereka zazikulu zimathandiza. Koma ndalama zambiri zoperekedwa kuti zithandizire pa ntchito ya Mboni za Yehova zimachokera m’mabokosi a zopereka za Nyumba ya Ufumu. Kaya zikhale zopereka zazikulu kapena zazing’ono, zonse n’zofunika ndipo sizinyalanyazidwa. Kumbukirani kuti Yesu anaona mkazi wamasiye wosauka uja akupereka timakobiri take tiŵiri. Angelo ndiponso Yehova anamuonanso mkaziyu. Sitidziŵa n’komwe dzina la mkaziyu, koma Yehova anaonetsetsa kuti zimene iye anachita mosaganizira kwambiri za iye yekha zilembedwe m’Baibulo ndi kukhalapo nthaŵi zonse.

Kuwonjezera pantchito yomanga Nyumba za Ufumu, zopereka zathu zimathandizanso pantchito zina zonse zokhudza ntchito yofunika kwambiri ya Ufumu. Kuthandizana mwa njira imeneyi kumatipatsa chifukwa chokhalira osangalala ndiponso kukhala ‘ochulukiranso kwa Mulungu mwa mayamiko ambiri.’ (2 Akorinto 9:12) Abale athu achikristu m’dziko la Benin anati: “Tsiku ndi tsiku anthu amapemphera kwa Yehova mapemphero oyamikira chithandizo cha ndalama chomwe alandira kuchokera kwa abale a padziko lonse.” Komanso, tonsefe amene timathandiza nawo pantchito ya Ufumu ndi ndalama timadalitsidwa chifukwa chopatsa.

[Bokosi/​Chithunzi pamasamba 22, 23]

Njira Zimene Ena Amaperekera

ZOPEREKA ZA NTCHITO YA PADZIKO LONSE

Ambiri amapatula, kapena kulinganiza, ndalama zimene amaika m’mabokosi a zopereka olembedwa kuti: “Zopereka za Ntchito ya Padziko Lonse​—Mateyu 24:14.”

Mwezi uliwonse mipingo imatumiza ndalama zimenezi ku ofesi ya Mboni za Yehova imene imayang’anira ntchito ya m’dziko lawo. Mungatumizenso mwachindunji ndalama zopereka modzifunira ku Accounting Office, Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania, P. O. Box 30749, Lilongwe 3, Malawi, kapena ku ofesi ya nthambi ya m’dziko lanu. Mukalemba macheke, musonyeze kuti alandire a “Watch Tower.” Mungaperekenso majuwelo kapena zinthu zina zamtengo wapatali. Tumizani pamodzi ndi kalata yachidule yofotokoza kuti zimenezo mwapereka monga mphatso yeniyeni.

MAKONZEDWE APADERA A ZOPEREKA

Ndalama zingaperekedwe pa makonzedwe apadera akuti, ngati woperekayo akuzifunanso, angam’bwezere zoperekazo. Kuti mudziŵe zambiri, lemberani ku Accounting Office pa adiresi imene tasonyeza pamwambapa.

KUPATSA KOLINGANIZA

Kuwonjezera pa mphatso zenizeni ndi ndalama zoperekedwa pa makonzedwe apadera, palinso njira zina zoperekera zinthu zopititsa patsogolo utumiki wa Ufumu padziko lonse. Zina mwa njirazi ndi izi:

Inshuwalansi: Watch Tower Society ingalembetsedwe kuti ndiyo idzapatsidwe phindu la inshuwalansi kapena penshoni.

Chuma ndi Ndalama Zoikizidwa: Chuma ndi ndalama zoikizidwa m’mabizinesi ena zingaperekedwe kukhala za Watch Tower Society monga mphatso yeniyeni.

Malo: Malo oti angagulitsidwe angaperekedwe monga mphatso yeniyeni kapena, ngati ali malo oti mukhoza kumangapo nyumba, mwa kusunga malowo amene mwiniwake angapitirizebe kukhalapo pamene ali ndi moyo. Lankhulani ndi ofesi ya nthambi ya m’dziko lanu musanakonze pangano la malo alionse.

Chuma Chamasiye: Chuma kapena ndalama zingakhale choloŵa cha Watch Tower Society kudzera m’pangano la amene adzatenga chuma chamasiye lochitidwa mwalamulo.

Ngati mukufuna kudziŵa zambiri za alionse mwa makonzedwe a kupatsa kolinganiza ameneŵa, lankhulani ndi a ku Accounting Office patelefoni kapena lemberani ku adiresi imene ili pansipa kapena ku ofesi ya Mboni za Yehova ya m’dziko lanu.

Accounting Office

Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania

P. O. Box 30749 Lilongwe 3

Malawi

Telefoni: 01762111.

[Zithunzi pamasamba 20, 21]

Malo akale ndi atsopano a misonkhano a Mboni za Yehova

M’dziko la Zambia

M’dziko la Central African Republic