Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

 Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Kodi Akristu amakuona bwanji kususuka?

Mawu a Mulungu amaletsa uchidakwa ndi kususuka ndipo amati izi sizololeka kwa atumiki a Mulungu. Motero, kwa Akristu palibe kusiyana pakati pa munthu wosusuka amene sakufuna kusintha ndi munthu amene ali ndi chizoloŵezi choledzera. Zidakwa ngakhalenso anthu osusuka sangakhale mumpingo wachikristu.

Lemba la Miyambo 23:20, 21 limati: “Usakhale mwa akumwaimwa vinyo, ndi ankhuli osusuka. Pakuti wakumwaimwa ndi wosusukayo adzasauka; ndipo kusinza kudzaveka munthu nsanza.” Pa Deuteronomo 21:20, (NW) timapezapo nkhani yonena za munthu “waliuma ndi wopanduka,” amene anayenera kuphedwa malinga ndi Chilamulo cha Mose. Malinga ndi vesili, makhalidwe aŵiri a munthu waliuma ndi wopandukayu anali ‘kususuka ndi uchidakwa.’ N’zoonekeratu kuti, kale ku Israyeli, anthu ofuna kutumikira Mulungu sankaloledwa kukhala osusuka.

Komano, kodi munthu wosusuka ndi munthu wotani, ndipo Malemba Achigiriki Achikristu amanenapo chiyani pankhaniyi? Munthu wosusuka amati ndi ‘munthu wodudukira kapena wolephera kuugwira mtima akaona zakudya.’ Motero, kususuka kumasonyezanso umbombo, ndipo Mawu a Mulungu amatiuza kuti “aumbombo” sadzaloŵa Ufumu wa Mulungu. (1 Akorinto 6:9, 10, NW; Afilipi 3:18, 19; 1 Petro 4:3) Komanso pamene mtumwi Paulo anachenjeza Akristu kuti apeŵe “ntchito za thupi,”  iye anatchulapo za “kuledzera, mchezo, ndi zina zotere.” (Agalatiya 5:19-21) Nthaŵi zambiri kudya mopitirira muyeso kumachitika chifukwa cha kuledzera ndiponso mchezo. Komanso, ponena kuti “ndi zina zotere,” mosakayikira Paulo anaphatikizapo kususuka. Monga mmene zimakhalira ndi “ntchito za thupi” zinazo, Mkristu amene watchuka ndi kususuka ndipo safuna kusintha khalidwe lake laumbombo ayenera kuchotsedwa mumpingo.​—1 Akorinto 5:11, 13. *

Ngakhale kuti Mawu a Mulungu sasiyanitsa chidakwa ndi munthu wosusuka, n’zosavuta kuzindikira chidakwa kusiyana ndi kuzindikira munthu wosusuka. Nthaŵi zambiri zizindikiro za uchidakwa n’zosavuta kuziona. Koma kuzindikira kuti munthu wafika pokhala wosusuka n’kovuta kwambiri chifukwa chakuti sizingatheke kum’zindikira mwa kungomuona. Motero, akulu mu mpingo amafunika kukhala osamala ndiponso ozindikira kwambiri pakakhala nkhani zokhudza kususuka.

Mwachitsanzo, kunenepa mopyola muyeso kungathe kukhala chizindikiro cha kususuka, koma sikuti ndi mmene zimakhalira nthaŵi zonse. Munthu angathe kunenepa kwambiri chifukwa cha matenda. Mwinanso zingakhale zotengera kwa makolo. Tiyeneranso kukumbukira kuti tikamanena kuti munthu ndi wonenepa mopyola muyeso timakhala tikunena za thupi lake, pamene tikanena za kususuka timakhala tikunena za maganizo ake. Kunenepa mopyola muyeso amati ndi “kuchuluka mafuta m’thupi,” pamene kususuka ndi “umbombo kapena kudya mosadziletsa.” Motero, kukula kwa thupi la munthu sichizindikiro cha kususuka. Chizindikiro chake ndi mmene munthuyo amaonera chakudya. Munthu angathe kukhala wathupi labwinobwino kapena wochepa thupi koma ali wosusuka. Komanso, mmene anthu a m’dera lina amaonera nkhani ya kunenepa moyenerera kapena kuumbika kwabwino kwa thupi zimasiyana kwambiri ndi mmene anthu a m’dera linanso angaonere nkhanizi.

Kodi zizindikiro za kususuka n’chiyani? Nthaŵi zambiri munthu wosusuka saatha kudziletsa, ndipo mwinanso amadya chakudya chambiri komanso mophangira mpaka kufika polephera kupuma bwino kapena kudwala kumene. Kulephera kudziletsa kumasonyeza kuti iye saganizira kwenikweni zoti akunyozetsa Yehova komanso zoti akuipitsa mbiri yabwino ya anthu Ake. (1 Akorinto 10:31) Komabe, munthu amene mwa apo ndi apo amadya kwambiri sangaonedwe kuti ndi “waumbombo.” (Aefeso 5:5, NW) Koma, potsatira mfundo ya pa Agalatiya 6:1, Mkristu woteroyo angafunikire kuthandizidwa. Paulo anati: “Abale, ngatinso munthu agwidwa nako kulakwa kwakuti, inu auzimu, mubweze wotereyo mu mzimu wa chifatso.”

Kodi n’chifukwa chiyani malangizo a m’Baibulo otilimbikitsa kupeŵa kudya kwambiri ali ofunika makamaka masiku ano? N’chifukwa chakuti, ponena za masiku athu ano makamaka, Yesu anachenjeza kuti: “Mudziyang’anire nokha, kuti kapena mitima yanu ingalemetsedwe ndi madyaidya ndi kuledzera, ndi zosamalira za moyo uno, ndi kuti tsiku ilo lingafikire inu modzidzimutsa ngati msampha.” (Luka 21:34) Kupeŵa kudya kwambiri ndi njira imodzi yofunika kwambiri yopeŵera moyo wotiwononga mwauzimu.

Akristu ayenera kukhala odziletsa. (1 Timoteo 3:2, 11) Motero, n’zosakayikitsa kuti Yehova angathandize anthu onse amene akuyesetsa kutsatira malangizo a m’Baibulo olimbikitsa kukhala odziletsa pankhani ya kudya ndi kumwa.​—Ahebri 4:16.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Onani “Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga” mu Nsanja ya Olonda yachingelezi ya May 1, 1986.