Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndani Angatsogolere Bwino Dziko Panopa?

Kodi Ndani Angatsogolere Bwino Dziko Panopa?

 Kodi Ndani Angatsogolere Bwino Dziko Panopa?

M’chaka cha 1940, nkhani ya utsogoleri inavuta koopsa m’nyumba ya malamulo ya ku Britain. David Lloyd George, bambo wa zaka 77, amene analipo pamakambitsirano a nkhaniyo, n’kuti atathandiza dziko la Britain kupambana pa nkhondo yoyamba ya padziko lonse ndipo poti anali atakhala zaka zambiri akuchita zandale ankadziŵa bwinobwino mmene akuluakulu aboma amagwirira ntchito. M’nyumba ya malamulo ya dzikolo, pa May 8, iye analankhula motere: “Dziko lino n’lokonzeka kulimbana ndi vuto lina lililonse, koma kuti litero likungofunika utsogoleri wabwino basi, likungofunika kuti boma lisonyeze bwinobwino zimene likufuna kuchita, ndiponso kuti anthu onse akhutitsidwe kuti atsogoleri a dziko lino akugwira ntchito yawo ndi mtima wonse.”

MAWU amene Lloyd George ananenaŵa amasonyezeratu kuti anthu amafuna kuti atsogoleri awo azikhala odziŵadi ntchito yawo ndiponso kuti aziyesetsa kukonza zinthu ndi mtima wawo wonse. Munthu wina wogwira ntchito yolimbikitsa anthu kuti akavote anati: “Anthu akamaponya voti yosankha munthu winawake kukhala pulezidenti, kwenikweni amakhala akuika moyo wawo, tsogolo lawo, komanso ana awo, m’manja mwake.” Kusenza udindo woterewu n’chintchito chadzaoneni. Kodi n’chifukwa chiyani zili choncho?

Dziko lathuli lili m’mavuto ochita kusoŵa poyambira kuwathetsa kwake. Mwachitsanzo, kodi ndi mtsogoleri uti amene wasonyeza kuti ndi wanzeru ndiponso wamphamvu kwambiri moti angathe kuchotseratu upandu ndiponso nkhondo? Kodi alipo mtsogoleri aliyense panopa amene ali wachuma kwambiri ndiponso wachifundo moti angathe kupatsa munthu aliyense chakudya, madzi abwino, ndiponso thandizo la zachipatala? Kodi ndani amene ali wodziŵa ndiponso wofunitsitsa kuteteza ndi kubwezeretsa mwakale zinthu zachilengedwe? Kodi ndani amene akudziŵa ndiponso amene ali ndi mphamvu zotha kuonetsetsa kuti anthu onse ali ndi moyo wautali komanso kuti n’ngosangalala?

Anthu Sangakwanitse Kuchita Ntchito Imeneyi

N’zoona kuti atsogoleri ena akwanitsa kuchita zinthu zinazake zabwino. Komabe, atsogoleri otereŵa angathe kulamulira kwa zaka zochepa chabe. Nangano iwoŵa akachoka pamabwera atsogoleri  otani? Mfumu Solomo wa dziko lakale la Israyeli, yemwe ndi m’modzi wa atsogoleri odziŵadi utsogoleri m’mbiri yonse ya anthu anadzifunsa funso limeneli. Ndiye anafika pa mfundo yakuti: “Ndipo ndinada ntchito zanga zonse ndinasauka nazo kunja kuno; pakuti ndidzam’siyira izo munthu wina amene adzanditsata. Ndipo ndani adziŵa ngati adzakhala wanzeru pena chitsiru? Koma adzalamulira ntchito zanga zonse ndinasauka nazo, ndi kuzigwira mwanzeru kunja kuno. Ichinso ndi chabe.”​—Mlaliki 2:18, 19.

Solomo sankadziŵa ngati amene adzaloŵe m’malo mwake adzapitirize ntchito yake yabwino kapena ngati adzawononge zonse zimene anachita. Kwa Solomo zomati mtsogoleri wina kuchoka wina n’kumuloŵa m’malo ankaziona kuti ‘n’zachabe.’ Mabaibulo ena amanena kuti kumeneku “n’kungotaya nthaŵi.”

Nthaŵi zina, anthu amachita zachiwawa pofuna kuti pabwere atsogoleri atsopano. Atsogoleri ena odziŵa bwino ntchito yawo aphedwapo adakali paulamuliro. Panthaŵi ina, Abraham Lincoln, yemwe anali pulezidenti wolemekezedwa kwambiri wa ku United States, anauza anthu kuti: “Ndasankhidwa kuti, kwakanthaŵi, ndikhale paudindo wofunika kwambiri, ndipo panopo ndapatsidwa mphamvu zimene, monga mukudziŵira, zitha m’kanthaŵi kochepa chabe.” Indedi, ulamuliro wake unali wakanthaŵi kochepa chabe. Ngakhale kuti anachita zinthu zambiri zothandiza ndiponso ankafunitsitsa kuthandiza kwambiri anthu, pulezidenti Lincoln analamulira dziko lake kwa zaka zinayi zokha basi. Atangoyamba chigawo chachiŵiri chaulamuliro wake, iye anaphedwa ndi munthu wina amene ankafuna kuti pabwere mtsogoleri wina.

Ngakhale atsogoleri abwino kwambiri sangadziŵe za tsogolo lawo motsimikiza. Motero, kodi muyenera kuika tsogolo lanu m’manja mwawo? Baibulo limati: “Musamakhulupirira zinduna, kapena mwana wa munthu, amene mulibe chipulumutso mwa iye. Mpweya wake uchoka, abwerera kumka ku nthaka yake; tsiku lomwelo zotsimikiza mtima zake zitayika.”​—Salmo 146:3, 4.

Ena zingawavute kuvomereza malangizo akuti tisamakhulupirire atsogoleri omwe ndi anthu anzathu. Komabe, dziŵani kuti Baibulo silinena kuti anthu sadzakhalapo ndi utsogoleri wabwino, komanso wokhalitsa. Yesaya 32:1 amati: “Taonani mfumu idzalamulira m’chilungamo, ndi akalonga adzalamulira m’chiweruzo.” Yehova Mulungu,  amene analenga anthu, wakhazikitsa “mfumu,” yomwe ndi mtsogoleri amene ayambe kulamulira zinthu zonse padziko pano posachedwapa. Kodi iyeyu ndani? Ulosi wa m’Baibulo umatithandiza kuti tim’dziŵe.

Amene Ali Woyenereradi Kukhala Mtsogoleri

Zaka masauzande aŵiri zapitazo, mngelo anauza Mariya, mtsikana wachiyuda, kuti: “Udzakhala ndi pakati, nudzabala mwana wamwamuna, nudzamutcha dzina lake Yesu. Iye adzakhala wamkulu, nadzatchedwa Mwana wa Wamkulukulu: ndipo Ambuye Mulungu adzam’patsa Iye mpando wachifumu wa Davide atate wake: ndipo Iye adzachita ufumu pa banja la Yakobo ku nthaŵi zonse; ndipo ufumu wake sudzatha.” (Luka 1:31-33) Inde, Yesu wa ku Nazarete ndiye Mfumu imene imatchulidwa m’maulosi a m’Baibulo.

Zojambulajambula zachipembedzo nthaŵi zambiri zimasonyeza Yesu ngati kamwana, nthaŵi zina akuoneka ngati munthu wosadya bwino, wonyentchera, kapenanso ngati munthu wokonda moyo wovutika amene amangoyang’anira zoipa zilizonse zimene zikum’gwera. Zithunzi zoterezi sizipangitsa anthu kuona kuti Yesu angakhaledi Mtsogoleri weniweni. Komano, Yesu Kristu weniweni amene amatchulidwa m’Baibulo, anali munthu wadzitho, wojintcha bwino wochita zinthu mwakhama ndiponso mosachita kum’pangira. Komanso anali ndi makhalidwe ena om’pangitsa kuti akhale mtsogoleri wabwino. (Luka 2:52) Nazi zina mwa zitsanzo za makhalidwe ake ena amene amaonekera kwambiri.

Yesu anali wokhulupirika kwambiri pa chilichonse. Anali munthu woona mtima ndi wowongoka mtima kwambiri mwakuti anauza adani ake poyera kuti anene ngati anamuonapo akuchita chinachake choipa chimene angamuimbe nacho mlandu. Adaniwo analephera kutero. (Yohane 8:46) Anthu ambiri oona mtima anakopeka n’kukhala om’tsatira chifukwa chakuti zinthu zomwe ankaphunzitsa sizinali zachiphamaso.​—Yohane 7:46; 8:28-30; 12:19

Yesu anadzipereka kwa Mulungu ndi mtima wonse. Iye anali wofunitsitsa kwambiri kumaliza bwinobwino ntchito imene Mulungu anam’patsa mwakuti panalibe aliyense, kaya munthu kapena chiwanda, amene akanamulepheretsa kutero. Iye sanabwerere m’mbuyo chifukwa choopa kuphedwa. (Luka 4:28-30) Sanafooke chifukwa cha kutopa kapenanso njala. (Yohane 4:5-16, 31-34) Ngakhale pamene anzake anam’thaŵa, iye sanasinthe cholinga chake.​—Mateyu 26:55, 56; Yohane 18:3-9.

Yesu ankaganizira anthu kwambiri. Anapatsa chakudya anthu anjala. (Yohane 6:10, 11) Analimbikitsa anthu othedwa nzeru. (Luka 7:11-15) Anachiritsa anthu osaona, osamva, ndiponso odwala. (Mateyu 12:22; Luka 8:43-48; Yohane 9:1-6) Analimbikitsa atumwi ake, omwe ankagwira ntchito mwakhama. (Yohane, chaputala 13 mpaka 17) Anasonyezadi kuti anali “Mbusa Wabwino” wosamalira bwino nkhosa zake.​—Yohane 10:11-14.

Yesu ankagwira ntchito mosanyinyirika. Anasambitsa mapazi a atumwi ake pofuna kuwaphunzitsa mfundo yofunika kwambiri. (Yohane 13:4-15) Ankayenda m’misewu yafumbi ya ku Israyeli polalikira uthenga wabwino. (Luka 8:1) Ngakhale pamene ankaganizira zoti akapume pamalo ena ‘apadera,’ analolera kuphunzitsa khamu la anthu amene anali kumufunafuna kuti apitirize kuwaphunzitsa. (Marko 6:30-34) Motero anapatsa Akristu onse chitsanzo cha kugwira ntchito molimbika.​—1 Yohane 2:6.

Yesu anamaliza ntchito yake n’kuchoka padziko pano. Chifukwa cha kukhulupirika kwake, Yehova anam’patsa mphoto ya ufumu ndiponso moyo wosafa. Ponena za Yesu amene panthaŵiyo anali ataukitsidwa, Baibulo limati: “Kristu anaukitsidwa kwa akufa, sadzafanso; imfa siichitanso ufumu pa iye.” (Aroma 6:9) Ndithudi, Yesu ndiye mtsogoleri wabwino koposa amene angatsogolere anthu. Yesu Kristu akadzangoyamba kulamulira chilichonse m’dzikoli, sipadzafunikanso kupatsa munthu wina mphamvu zolamulira, ndipo sipadzafunikanso kusintha utsogoleri wake. Yesu sadzachotsedwa paudindo wake mochita kuphedwa, ndipo ntchito imene adzachite siidzawonongedwa chifukwa chakuti sipadzakhala munthu wina wodzaloŵa m’malo mwake. Koma kodi n’chiyani makamaka chimene adzawachitire anthu?

Zimene Mtsogoleri Watsopanoyu Adzachite

Salmo 72 limatiuza mwaulosi zinthu zina zokhudza mmene Mfumu yangwiro, ya moyo wosafa imeneyi idzalamulilire. Mu vesi 7 ndi 8 timaŵerenga kuti: “Masiku ake wolungama adzakhazikika; ndi mtendere wochuluka, kufikira sipadzakhala  mwezi. Ndipo adzachita ufumu kuchokera kunyanja kufikira kunyanja, ndi kuchokera ku Mtsinje kufikira malekezero a dziko lapansi.” Muulamuliro wake wabwinowu, anthu okhala padziko lapansi adzakhala otetezeka nthaŵi zonse mpaka kalekale. Iye adzawononga zida zonse zimene zilipozi ndipo adzachotsa ngakhale chikhumbo chofuna nkhondo chenichenicho. Anthu amene panopo amavutitsa anzawo ngati mmene imachitira mikango yolusa kapena anthu amene amavutitsa anzawo ngati zimbalangondo zoipa mtima adzasinthiratu makhalidwe awo. (Yesaya 11:1-9) Mtendere udzakhala ponseponse.

Mavesi 12 mpaka 14 a Salmo 72 amapitiriza kunena kuti: “Adzapulumutsa waumphawi wofuulayo; ndi wozunzika amene alibe mthandizi. Adzachitira nsoni wosauka ndi waumphawi, nadzapulumutsa moyo wa aumphawi. Adzawombola moyo wawo ku chinyengo ndi chiwawa; ndipo mwazi wawo udzakhala wa mtengo [wapatali] pamaso pake.” Anthu osauka, aumphawi ndiponso ozunzika adzakhala osangalala pamodzi ndi anthu ena onse, adzayanjanitsidwa ndi ulamuliro wa Mfumu Yesu Kristu. Moyo wawo udzakhala wosangalala osati wa zowawa ndi zopweteketsa mutu.​—Yesaya 35:10.

Vesi 16 limalonjeza kuti: “M’dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka pamwamba pa mapiri.” Anthu ochuluka padziko pano amavutika ndi njala nthaŵi zonse. Ndale ndiponso dyera n’zimene nthaŵi zambiri zimachititsa kuti chakudya chisagaŵidwe mokomera anthu onse. Motero anthu ambirimbiri, makamaka ana amafa ndi njala. Koma muulamuliro wa Yesu Kristu, vuto limeneli lidzatheratu. Dziko lidzakhala ndi zakudya zochuluka ndiponso zokoma. Anthu onse adzakhala ndi chakudya chokwanira.

Kodi inuyo mungakonde kudzadalitsidwa nawo mu utsogoleri wabwino umenewu? Ngati mungakonde kutero, tikukulimbikitsani kuti muphunzire za mtsogoleri ameneyu amene posachedwapa adzayamba kulamulira dziko lonse. Mboni za Yehova, zingasangalale kwambiri kukuthandizani kuchita zimenezi. Simudzagwiritsidwa fuŵa lamoto chifukwa Yehova Mulungu mwini amanena za mwana wake kuti: “Ine ndadzoza mfumu yanga pa Ziyoni, phiri langa loyera.”​—Salmo 2:6.

[Bokosi patsamba 5]

KUCHOKA PAMPANDO MOSAYEMBEKEZEKA

Nthaŵi zambiri mtsogoleri amadziŵa kuti anthu ake angamulemekeze ndiponso kumuthandiza ngati paulamuliro wake, anthuwo akukhala mwamtendere ndiponso mwabata. Komano pazifukwa zina anthu aja akangosiya kumukhulupirira, posakhalitsa angathe kuika mtsogoleri wina pampando wake uja. Nazi zitsanzo zina za zinthu zimene zachititsapo atsogoleri ena amphamvu kuchoka pampando mosayembekezeka.

Moyo Wovutika. Pofika kumapeto kwa zaka za m’ma 1700, anthu ambiri a ku France moyo wawo unali wovutika chifukwa cha kukwera kwa misonkho ndiponso kuchepa kwa chakudya. Zimenezi zinachititsa kuti anthu onse m’dzikolo agalukire Ufumu umene unkawalamulira, motero m’chaka cha 1793 Mfumu Louis XVI inanyongedwa.

Nkhondo. Nkhondo yoyamba ya padziko lonse inathetsa ulamuliro wa atsogoleri ena amphamvu kwambiri m’mbiri ya anthu. Mwachitsanzo, chifukwa cha nkhondoyi, m’chaka cha 1917 chakudya chinasoŵa kwambiri mumzinda wa St. Petersburg, ku Russia, motero anthu anaukira Ufumu wawo m’mwezi wa February. Kuukira kumeneku kunachititsa kuti Mfumu Nicholas II ichotsedwe pampando, ndiye ulamuliro wa Chikomyunizimu unayambika. M’mwezi wa November 1918, dziko la Germany linafuna kuti agwirizane zamtendere, koma mayiko omwe ankamenyana ndi dzikoli ananena kuti sasiya kumenyana nalo mpaka utsogoleri wake utasintha. Motero, Mfumu ya ku Germany Wilhelm II anakakamizika kuthaŵira ku Netherlands.

Kufuna kuyesa mitundu ina ya boma. M’chaka cha 1989 ulamuliro wa Chikomyunizimu ku Russia unayamba kutha mphamvu. Maboma amene ankaoneka kuti ndi olimba kwambiri anayamba kugwa chifukwa anthu awo anayamba kudana ndi Chikomyunizimu n’kuyamba kukhazikitsa maboma a mitundu ina.

[Zithunzi patsamba 7]

Yesu anapatsa chakudya anthu anjala, anachiritsa odwala, ndipo anapereka chitsanzo chabwino kwambiri kwa Akristu onse

[Mawu a Chithunzi patsamba 4]

Lloyd George: Photo by Kurt Hutton/​Picture Post/​Getty Images