Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Muyenera Kukhulupirira Kuti Dziko Lapansi Lidzakhala Paradaiso?

Kodi Muyenera Kukhulupirira Kuti Dziko Lapansi Lidzakhala Paradaiso?

Kodi Muyenera Kukhulupirira Kuti Dziko Lapansi Lidzakhala Paradaiso?

NDI anthu ochepa okha amene amakhulupirira kuti nthaŵi ina dziko lapansili lidzakhala paradaiso. Ambiri amaganiza kuti silidzapitiriza kukhalapo. Malinga ndi zomwe linanena buku lakuti The Sacred Earth, la Brian Leigh Molyneaux, dziko lapansili linakhalapo kanthu kenakake kataphulika zaka mamiliyoni ambiri zapitazo. Ndipo ngati anthu saliwononga, anthu ambiri amakhulupirira kuti dzikoli pamodzi ndi zakuthambo zonse pamapeto pake “zidzawonongeka mwa kuphatikananso pamodzi n’kuyaka moto.”

Mngelezi wina wolemba ndakatulo wa zaka za m’ma 1600, John Milton, analibe maganizo odetsa nkhaŵa ngati ameneŵa. M’ndakatulo yake yofotokoza zakale yakuti Paradise Lost, iye analemba kuti Mulungu analenga dziko lapansi kuti likhale malo a paradaiso kuti anthu akhalemo. Paradaiso woyambirirayo anatayika. Komabe, Milton ankakhulupirira kuti paradaisoyu adzabwezeretsedwa, kuti tsiku lina Yesu Kristu pokhala mpulumutsi “adzafupa anthu ake okhulupirika, ndi kuwalandira kumalo achisangalalo . . . Kumwamba kapena Padziko Lapansi.” Milton ananena ndi mtima wonse kuti: “Chifukwa chakuti panthaŵiyo Dziko Lapansi lonseli lidzakhala Paradaiso.”

Kodi Paradaiso Adzakhala Kumwamba Kapena Padziko Lapansi?

Anthu ambiri opembedza ali ndi maganizo a Milton akuti pamapeto a zonse iwo adzalandira chipukuta misozi chifukwa cha mavuto aakulu omwe akukumana nawo pansi pano. Komano mphoto imeneyi adzalandirira kuti? Kodi kudzakhala “Kumwamba kapena Padziko Lapansi”? Kwa anthu ena, dziko lapansili silibwera n’komwe m’maganizo mwawo. Amati anthu ‘adzasangalala’ pokhapokha atachoka padziko lapansi n’kukakhala kumalo a mizimu kumwamba.

M’buku lakuti Heaven​—A History, C. McDannell ndi B. Lang, omwe analemba bukuli, ananena kuti katswiri wina wamaphunziro a zaumulungu wa zaka za m’ma 100, Irenaeus, ankakhulupirira kuti moyo m’paradaiso wobwezeretsedwa “sudzakakhala kumalo enaake kumwamba, koma padziko lapansi.” Malinga ndi bukuli, ngakhale kuti atsogoleri achipembedzo monga John Calvin ndi Martin Luther ankayembekezera kupita kumwamba, iwo ankakhulupiriranso kuti “Mulungu adzakonzanso dziko lapansi.” Anthu a zipembedzo zina nawonso akhala akukhulupirira zimenezi. McDannell ndi Lang ananenanso kuti anthu ena achiyuda ankakhulupirira kuti panthaŵi yomwe Mulungu adzafune, mavuto onse omwe anthu akukumana nawo “adzachotsedwa ndipo anthu adzakhala mosangalala padziko lapansi.” Malinga ndi chikhulupiriro chakale cha Aperisiya, “dziko lapansi lidzabwezeretsedwa mmene linalili pachiyambi ndipo anthu adzakhalanso mwamtendere,” limatero buku lakuti The Encyclopaedia of Middle Eastern Mythology and Religion.

N’chifukwa chiyani anthu sakuyembekezeranso kuti dzikoli lidzakhala paradaiso? Kodi moyo wathu padziko lapansi pano ndi wongoyembekezera chabe? Kodi moyo wathuwu ndi woti ungokhala “wachidule, komanso nthaŵi zambiri wamavuto” paulendo wopita kumalo a mizimu, monga momwe ankakhulupirira wafilosofi wachiyuda wa m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino, Philo? Kapena sizimene Mulungu ankalingalira pamene ankalenga dziko lapansi n’kuikapo anthu m’malo aparadaiso? Kodi anthu angapeze chimwemwe chenicheni mwauzimu ndi kusangalala padziko lapansi pompano? Bwanji osapenda zomwe Baibulo limanena pankhaniyi? Mukhoza kuyamba kuona, monga momwe anthu mamiliyoni angapo akuonera, kuti m’pomvekadi kukhulupirira kuti dziko lapansili lidzakhalanso paradaiso.

[Chithunzi patsamba 3]

Wolemba ndakatulo John Milton ankakhulupirira kuti Paradaiso adzapezedwanso

[Mawu a Chithunzi patsamba 2]

COVER: Earth: U.S. Fish & Wildlife Service, Washington, D.C./​NASA

[Mawu a Chithunzi patsamba 3]

Dziko: U.S. Fish & Wildlife Service, Washington, D.C./​NASA; John Milton: Leslie’s