Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

M’pomveka Kukhulupirira Kuti Dzikoli Lidzakhala Paradaiso

M’pomveka Kukhulupirira Kuti Dzikoli Lidzakhala Paradaiso

 M’pomveka Kukhulupirira Kuti Dzikoli Lidzakhala Paradaiso

KUYAMBIRA kale, anthu ambiri akhala akukhulupirira kuti pamapeto a zonse iwo adzachoka padziko lapansi pano n’kupita kumwamba. Ena amaganiza kuti Mlengi wathu sanalingalirepo zoti tikhale padziko pano kosatha. Anthu odzimana kwambiri zinthu ndiye achita kuposa pamenepo. Ambiri mwa iwo amati dzikoli pamodzi ndi zinthu zake zonse n’zoipa, ndipo zimalepheretsa munthu kukhala wosangalala mwauzimu komanso kuyandikana ndi Mulungu.

Anthu amaganizo ameneŵa mwinamwake sadziŵa zomwe Mulungu ananena pankhani ya dziko lapansi la paradaiso kapena amazinyalanyaza mwadala. Ndipotu, masiku ano ambiri alibe chidwi chofuna kuona zinthu zokhudza nkhaniyi zomwe Mulungu anauzira anthu kuti alembe m’Mawu ake, Baibulo. (2 Timoteo 3:16, 17) Koma kodi sichinthu chanzeru kudalira Mawu a Mulungu m’malo mokhulupirira zoganiza za anthu? (Aroma 3:4) Ndipotu n’kofunika kwambiri kuti tizitero, popeza Baibulo limatichenjeza kuti chamoyo china champhamvu kwambiri chomwe sichioneka chachititsa anthu khungu nwauzimu ndipo tsopano ‘chikunyenga dziko lonse.’​—Chivumbulutso 12:9; 2 Akorinto 4:4.

N’chifukwa Chiyani Pali Chisokonezo Chonchi?

Ziphunzitso zosiyanasiyana ponena za moyo ndi imfa zasokoneza anthu kwambiri pankhani ya cholinga cha Mulungu polenga dziko lapansi. Ambiri amakhulupirira kuti anthufe tili ndi munthu wa mzimu m’matupi mwathu amene amakhalapobe ndi moyo munthu akafa. Ena amakhulupirira kuti munthu wa mzimu wosaonekayo wa munthu aliyense analipo kale thupi la munthuyo lisanakhalepo. Malinga n’kunena kwa buku lina, wafilosofi wachigiriki, Plato ankaganiza kuti munthu wa mzimuyo “amam’tsekera m’thupi pomulanga chifukwa cha zochimwa zake pamene anali kumwamba.” Mofanana ndi malingaliro ameneŵa, katswiri wina wamaphunziro a zaumulungu wa zaka za m’ma 200, Origen ananena kuti “anthu a mzimu a m’matupi athuŵa anachimwa [kumwamba] asanagwirizanitsidwe ndi matupiŵa” ndipo “anatsekeredwa ukaidi [m’matupiŵa padziko lapansi pano] monga chilango cha machimo awo.” Ndipo anthu ambiri amakhulupirira kuti dzikoli ndi malo oyeserapo anthu paulendo wawo wa kumwamba.

Palinso malingaliro osiyanasiyana onena za zomwe zimachitika munthu akafa. Malinga ndi zimene linanena buku lakuti History of Western Philosophy, Aigupto ankaganiza kuti “mizimu ya anthu akufa imatsikira kumidima.” Pambuyo pake afilosofi anayamba kutsutsa zimenezi n’kumati mizimu ya anthu akufa sinatsikire kumidima koma inapita kumwamba kumalo a mizimu. Anthu amanena kuti wafilosofi wachigiriki, Socrates ankakhulupirira kuti panthaŵi yakufa, mzimu wa munthu “umapita kumalo osaoneka . . . ndipo umakakhala kumeneko ndi milungu nthaŵi yonse yamoyo wake.”

Kodi Baibulo Limati Chiyani?

Mawu ouziridwa a Mulungu, Baibulo, sanenako m’pamodzi pomwe kuti anthu ali ndi mizimu yomwe siifa. Taŵerengani nokha nkhani ya pa Genesis 2:7. Imati: “Yehova Mulungu anaumba munthu ndi dothi lapansi, nauzira mpweya wa moyo m’mphuno mwake; munthuyo nakhala wamoyo.” Izi n’zomveka ndiponso sizosokoneza m’pang’ono pomwe. Mulungu atalenga munthu woyambayo, Adamu, sanaike m’thupi mwake munthu wosaoneka wa mzimu.

 Polenga dziko lapansi ndiponso anthu, Yehova sankafuna kuti anthu azifa. Cholinga cha Mulungu chinali chakuti anthu akhale kosatha padziko lapansi la Paradaiso. Adamu anafa chifukwa chakuti sanamvere lamulo la Mulungu basi. (Genesis 2:8, 15-17; 3:1-6; Yesaya 45:18) Munthu woyambayo atafa, kodi anapita kumalo enaake a mizimu? Ayi! Iye, Adamu, anabwerera kufumbi lopanda moyo, komwe anachokera.​—Genesis 3:17-19.

Tonsefe tinalandira choloŵa cha uchimo ndi imfa kuchoka kwa kholo lathu Adamu. (Aroma 5:12) Imfa imeneyi ndiyo kusakhalaponso, monga momwe zinachitikira kwa Adamu. (Salmo 146:3, 4) Ndipotu, m’mabuku onse 66, Baibulo silisonyezapo kuti chinachake chosatha kufa chimakhalabe ndi moyo munthu akafa. Mosiyana kwambiri ndi zimenezo, Malemba amanena momveka bwino kuti moyo wa munthu umatheratu iye akafa.​—Mlaliki 9:5, 10.

Kodi Zinthu za M’dzikoli Zinalengedwa Zoipa?

Nanga bwanji za mfundo yakuti zinthu za m’dziko kuphatikizapo dzikoli, n’zoipa? Ameneŵa ndiwo anali maganizo a Amanike, chipembedzo chomwe chinayambira ku Persia m’zaka za m’ma 200, m’Nyengo Yathu Ino, ndi munthu wina dzina lake Mani. Buku lakuti The New Encyclopædia Britannica limati: “Chimanike chinayamba chifukwa cha mazunzo omwe anthu amabadwa nawo.” Mani ankakhulupirira kuti kukhala munthu “n’kwachilendo, kovuta, ndiponso koipa kwambiri.” Ankakhulupiriranso kuti njira yokha yosiyanirana ndi ‘mazunzoŵa’ inali yoti mzimu usiyane ndi thupi, n’kuchoka padziko lapansi, ndi kukakhala kudziko la mizimu.

Mosiyana ndi zimenezi, Baibulo limatiuza kuti kwa Mulungu “zonse zimene adazipanga” polenga dziko lapansi ndiponso munthu zinali “zabwino ndithu.” (Genesis 1:31) Nthaŵi imeneyo panalibe chopinga chilichonse pakati pa anthu ndi Mulungu. Adamu ndi Hava anali paubwenzi wolimba ndi Yehova, monga momwe zinalili pakati pa munthu wangwiro, Yesu Kristu ndi Atate wake wakumwamba.​—Mateyu 3:17.

Makolo athu oyamba, Adamu ndi Hava, akadapanda kuchimwa, akanakhala paubwenzi wolimba ndi Yehova Mulungu kwamuyaya padziko lapansi la paradaiso. Moyo wawo anauyambira m’Paradaiso, chifukwa Malemba amatiuza kuti: “Yehova Mulungu anabzala m’munda ku Edene chakum’maŵa; momwemo ndipo adaika munthu adamuumbayo.” (Genesis 2:8)  Hava anam’lengera m’munda wa paradaisowu. Adamu ndi Hava akanapanda kuchimwa, iwo ndi ana awo angwiro akanagwirira ntchito pamodzi mosangalala mpaka dziko lonse litakhala paradaiso. (Genesis 2:21; 3:23, 24) Paradaiso wa padziko lapansi akanakhala malo okhalapo anthu kwamuyaya.

N’chifukwa Chiyani Ena Amapita Kumwamba?

Mwina munganene kuti, ‘Komatu Baibulo limanena za anthu opita kumwamba, kodi sichoncho?’ Inde limanena. Adamu atachimwa, Yehova anakonza zokhazikitsa Ufumu wakumwamba womwe ena mwa mbadwa za Adamu ‘adzachite ufumu padziko’ pamodzi ndi Yesu Kristu. (Chivumbulutso 5:10; Aroma 8:17) Odzachita ufumuwo anali anthu oti adzaukitsidwa kukakhala ndi moyo wosafa kumwamba. Onse pamodzi ndi 144,000, ndipo oyambirira mwa anthu ameneŵa anali ophunzira okhulupirika a Yesu a m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino.​—Luka 12:32; 1 Akorinto 15:42-44; Chivumbulutso 14:1-5.

Komano sikuti chinali cholinga cha Mulungu poyambapo kuti anthu olungama adzachoke padziko kupita kumwamba. Ndipo, Yesu ali padziko lapansi, anati: “Kulibe munthu anakwera Kumwamba, koma Iye wotsikayo kuchokera Kumwamba, ndiye Mwana wa munthu.” (Yohane 3:13) Kudzera mwa “Mwana wa munthu,” Yesu Kristu, Mulungu anapereka dipo lomwe likupangitsa kuti anthu okhulupirira nsembe ya Yesu adzapeze moyo wosatha. (Aroma 5:8) Koma kodi miyandamiyanda ya anthu oterowo idzakhala kuti kosatha?

Cholinga Choyambirira cha Mulungu Chidzakwaniritsidwa

Ngakhale kuti Mulungu anakonza zotenga anthu ena kuti akalamulire pamodzi ndi Yesu Kristu mu Ufumu wakumwamba, zimenezi sizikutanthauza kuti anthu onse abwino amapita kumwamba. Yehova analenga dziko kuti likhale Paradaiso wokhalamo anthu. Posachedwapa, Mulungu adzakwaniritsa cholinga chimenechi.​—Mateyu 6:9, 10.

Mu ulamuliro wa Yesu Kristu ndi anzake olamulira nawo kumwamba, padziko lonse lapansi padzakhala mtendere ndi chimwemwe. (Salmo 37:9-11) Anthu amene Mulungu akuwakumbukira adzaukitsidwa kwa akufa n’kukhala ndi thanzi labwino. (Machitidwe 24:15) Chifukwa cha kukhulupirika kwawo kwa Mulungu, anthu omvera adzapatsidwa chomwe makolo athu oyamba anataya, kukhala anthu angwiro ndiponso kosatha m’paradaiso padziko lapansi.​—Chivumbulutso 21:3, 4.

Yehova Mulungu salephera kuchita zomwe wakonza kuti achite. Kudzera mwa mneneri wake Yesaya, iye anati: “Monga mvula imagwa pansi ndi matalala, kuchokera kumwamba yosabwerera komweko, koma ikhamiza nthaka ndi kuibalitsa, ndi kuiphukitsa, ndi kuipatsitsa mbewu kwa wobzala, ndi chakudya kwa wakudya; momwemo adzakhala mawu anga amene aturuka m’kamwa mwanga, sadzabwerera kwa Ine chabe, koma adzachita chimene ndifuna, ndipo adzakula mmene ndinawatumizira.”​—Yesaya 55:10, 11.

M’buku la m’Baibulo la Yesaya, timaona chithunzithunzi cha mmene moyo udzakhalire m’Paradaiso padziko lapansi. Palibe wokhala m’Paradaiso adzanene kuti, “Ine ndidwala.” (Yesaya 33:24) Nyama sizidzaopseza anthu. (Yesaya 11:6-9) Anthu adzamanga nyumba zabwino ndi kukhalamo ndipo adzabzala mbewu n’kudya ndi kukhuta. (Yesaya 65:21-25) Komanso, Mulungu ‘adzameza imfa ku nthaŵi yonse; ndipo Ambuye Mulungu adzapukuta misozi pa nkhope zonse.’​—Yesaya 25:8.

Posachedwapa anthu omvera adzakhala m’malo abwino oterowo. ‘Adzamasulidwa ku ukapolo wa chivundi, ndi kuloŵa ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu.’ (Aroma 8:21) Zidzakhalatu zosangalatsa kwambiri kukhala kosatha m’Paradaiso wolonjezedwa wa padziko lapansi! (Luka 23:43) Mungadzakhale nawo m’Paradaiso ameneyu ngati panopo mukutsatira zinthu zolondola zopezeka m’Malemba ndi kukhulupirira Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu. Ndipo mungatsimikizedi kuti m’pomveka kukhulupirira kuti dziko lapansi lidzakhala paradaiso.

[Chithunzi patsamba 5]

Adamu ndi Hava analengedwa kuti akhale kosatha m’dziko lapansi la paradaiso

 [Zithunzi patsamba 7]

M’Paradaiso padziko lapansi . . .

adzamanga nyumba

adzawoka minda yamphesa

adzadalitsidwa ndi Yehova

[Mawu a Chithunzi patsamba 4]

U.S. Fish & Wildlife Service, Washington, D.C./​NASA