Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Lalikirani ndi Cholinga Chopanga Ophunzira

Lalikirani ndi Cholinga Chopanga Ophunzira

 Lalikirani ndi Cholinga Chopanga Ophunzira

‘Pamene anamumva [Apolo], Priskila ndi Akula anam’tenga, nam’fotokozera njira ya Mulungu mosamalitsa.’​—MACHITIDWE 18:26.

1. Ngakhale kuti anali ndi “mzimu wachangu,” kodi Apolo anafunika chiyani?

PRISKILA ndi Akula, banja lachikristu la m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino, anamvera Apolo akulankhula m’sunagoge mu mzinda wa Efeso. Popeza Apolo anali wodziŵa kulankhula ndiponso anali ndi luso lokopa, anali kuchititsa chidwi omvera ake. Iye anali ndi “mzimu wachangu,” ndipo anali “kuphunzitsa mosamalira zinthu za Yesu.” Komabe, zinali kuonekeratu kuti Apolo ‘ankadziŵa ubatizo wa Yohane wokha.’ Zimene Apolo analalikira pankhani ya Kristu zinali zoona ndithu. Vuto linali lakuti sanali kudziŵa zonse. Apolo anafunika kuwonjezera zimene anali kudziŵa zokhudza ntchito ya Yesu Kristu pokwaniritsa cholinga cha Yehova.​—Machitidwe 18:24-26.

2. Kodi ndi ntchito yovuta iti imene Priskila ndi Akula analolera kuigwira?

 2 Mofulumira, Priskila ndi Akula anadzipereka kuthandiza Apolo kuti akhale munthu wotsatira “zinthu zonse” zimene Kristu analamula. (Mateyu 28:19, 20) Nkhaniyo imati anamutenga Apolo “nam’fotokozera njira ya Mulungu mosamalitsa.” Komabe panali zifukwa zina zokhudza Apolo zimene zikanapangitsa Akristu ena kulephera kum’phunzitsa. Zifukwa zotani? Ndipo kodi tingaphunzire chiyani pa kuyesetsa kwa Priskila ndi Akula kukambirana Malemba ndi Apolo? Kodi kupenda nkhani yakale imeneyi kungatithandize bwanji kuika maganizo pa kuyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba?

Ganizirani Kwambiri Anthu

3. N’chifukwa chiyani mbiri ya Apolo sinalepheretse Priskila ndi Akula kumuphunzitsa?

3 Popeza Apolo anali mbadwa yachiyuda, mosakayikira anakulira mu mzinda wa Alesandriya. Panthaŵi imeneyo mzindawu unali likulu la Igupto ndiponso kuchimake kwa maphunziro apamwamba, wotchuka chifukwa kunali laibulale yaikulu. Mu mzindawu munali Ayuda ambiri, komanso akatswiri amaphunziro. N’chifukwa chake, Baibulo lachigiriki la Malemba Achihebri lodziŵika ndi dzina lakuti Septuagint linapangidwa kumeneko. M’pake kuti Apolo anali “wamphamvu m’malembo [“wodziŵa Malemba kwambiri,” NW].” Akula ndi Priskila anali opanga mahema. Kodi iwo anachita mantha chifukwa chakuti Apolo anali wodziŵa kulankhula? Ayi. Chifukwa chakuti anali kumukonda anaganizira za iye, vuto lake, ndiponso momwe angamuthandizire.

4. Kodi n’kuti ndipo ndi motani mmene Apolo analandirira thandizo limene anali kufunika?

4 Kaya Apolo anali wodziŵa kulankhula bwanji, anafunika kumulangiza. Zimene amafunika kumuthandiza sizinali kupezeka ku yunivesite ina iliyonse koma kwa anzake a mu mpingo wachikristu. Mwa kulangizidwa, Apolo akanapindula ndi mfundo zom’thandiza kudziŵa zolondola kwambiri ponena za zimene Mulungu wakonza pankhani ya chipulumutso. Priskila ndi Akula “anam’tenga, nam’fotokozera njira ya Mulungu mosamalitsa.”

5. Kodi mungati chiyani ponena za moyo wauzimu wa Priskila ndi Akula?

5 Priskila ndi Akula anali olimba mwauzimu ndiponso anali ndi maziko olimba m’chikhulupiriro. Mosakayikira, anali ‘okonzeka nthaŵi zonse kuchita chodzikanira pa yense wakufunsa chifukwa cha chiyembekezo chinali mwa iwo,’ kaya munthuyo anali wolemera, wosauka, katswiri wamaphunziro, kapena kapolo. (1 Petro 3:15) Akula ndi mkazi wake ankatha ‘kulunjika nawo bwino mawu a choonadi.’ (2 Timoteo 2:15) Mwachionekere, anali kuphunzira Malemba mosamala kwambiri. Apolo analimbikitsidwa kwambiri ndi malangizo a ‘m’mawu a Mulungu amene ali amoyo, ndi ochitachita,’ okhudza mtima.​—Ahebri 4:12.

6. Kodi tikudziŵa bwanji kuti Apolo anayamikira thandizo limene analandira?

6 Apolo anayamikira chitsanzo cha aphunzitsi ake ndipo anakhala waluso kwambiri popanga ophunzira. Zimene anadziŵazo anazigwiritsa ntchito mokwanira polengeza uthenga wabwino, makamaka kwa Ayuda. Apolo anathandiza kwambiri kukopa Ayuda pankhani ya Kristu. ‘Popeza anali wamphamvu m’malembo,’ amatha kuwatsimikizira kuti aneneri onse akale anali kudikira mwatcheru kubwera kwa Kristu. (Machitidwe 18:24) Nkhaniyo imanenanso kuti Apolo kenako anapita ku Akaya, kumene “anathangata ndithu iwo akukhulupira mwa chisomo; pakuti ndi mphamvu anatsutsa Ayuda, pamaso pa anthu, nasonyeza mwa malembo kuti Yesu ndiye Kristu.”​—Machitidwe 18:27, 28.

Tengerani Chitsanzo cha Aphunzitsi Ena

7. Kodi zinatani kuti Akula ndi Priskila akhale aphunzitsi aluso?

7 Kodi Akula ndi Priskila anakhala bwanji aphunzitsi aluso a Mawu a Mulungu? Kuwonjezera pa kuphunzira mwakhama ndiponso kupezeka pamisonkhano, kucheza kwambiri ndi mtumwi Paulo kuyenera kuti kunawathandiza zedi. Kwa chaka chimodzi ndi theka, Paulo anakhala kunyumba kwa Priskila ndi Akula ku Korinto. Anagwirira limodzi ntchito yopanga  ndi kukonzanso mahema. (Machitidwe 18:2, 3) Tangolingalirani nkhani zakuya za m’Malemba zimene ayenera kuti ankakambirana. Ndithudi kucheza kwawo ndi Paulo kunawonjezera zimene anali kudziŵa mwauzimu. “Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru,” imatero Miyambo 13:20. Kucheza ndi anthu abwino kunawathandiza kwambiri pa zochita zawo zauzimu.​—1 Akorinto 15:33.

8. Kodi Priskila ndi Akula anaphunzira chiyani poona Paulo ali mu utumiki?

8 Priskila ndi Akula atamuona Paulo akulengeza Ufumu, anaona mmene mphunzitsi wabwino ayenera kukhalira. Nkhani ya m’buku la Machitidwe imanena kuti Paulo “anafotokozera m’sunagoge [ku Korinto] masabata onse, nakopa Ayuda ndi Ahelene.” Kenako, ali ndi Sila ndi Timoteo, Paulo “anapsinjidwa [“anatanganidwa kwambiri,” NW] ndi mawu, nachitira umboni kwa Ayuda kuti Yesu ndiye Kristu.” Paulo ataona kuti anthu a m’sunagoge analibe chidwi kwenikweni, iye anachoka kumene ankakonda kulalikirako kupita kumalo abwino kwambiri, nyumba yoyandikana ndi sunagoge ndipo Priskila ndi Akula anamuona iye akuchita zimenezi. Kumeneko Paulo anathandiza Krispo, “mkulu wa sunagoge,” kukhala wophunzira. Mwachionekere, Priskila ndi Akula anaona kuti kusintha kwa munthu ameneyu kukhala wophunzira kunathandiza kwambiri deralo kukhala lobala zipatso. Nkhaniyo imati: “Krispo . . . anakhulupirira Ambuye, ndi apabanja ake onse; ndipo Akorinto ambiri anamva, nakhulupira, nabatizidwa.”​—Machitidwe 18:4-8.

9. Kodi Priskila ndi Akula anachita chiyani ndi chitsanzo cha Paulo?

9 Olengeza Ufumu ena monga Priskila ndi Akula, anatengera zimene Paulo anali kuchita mu utumiki wakumunda. Mtumwiyo analimbikitsa Akristu ena kuti: “Khalani onditsanza ine, monga inenso nditsanza Kristu.” (1 Akorinto 11:1) Potsatira chitsanzo cha Paulo, Priskila ndi Akula anathandiza Apolo kudziŵa molondola kwambiri ziphunzitso zachikristu. Kenako, Apolo nayenso anathandiza ena. Mosakayikira Priskila ndi Akula anathandiza kupanga ophunzira ku Roma, Korinto, ndi Efeso.​—Machitidwe 18:1, 2, 18, 19; Aroma 16:3-5.

10. Kodi mwaphunzira chiyani m’Machitidwe chaputala 18 chimene chikuthandizeni mu ntchito yopanga ophunzira?

10 Kodi tingaphunzire chiyani popenda Machitidwe chaputala 18? Chabwino, monga momwe Akula ndi Priskila anaphunzirira kwa Paulo, tingakulitse luso lathu lopanga ophunzira potsanzira chitsanzo cha aphunzitsi abwino a Mawu a Mulungu. Tingacheze ndi amene ‘amatanganidwa kwambiri ndi mawu’ ndiponso amene ‘amachitira umboni mokwanira’ kwa ena. (Machitidwe 18:5, Kingdom Interlinear Translation) Tingaone momwe amawafikira anthu pamtima pogwiritsa ntchito luso lokopa anthu pophunzitsa. Luso limeneli lingatithandize kupanga ophunzira. Munthu akamaphunzira nafe Baibulo, tingamuuze kuti aitane  anthu ena a m’banja lake kapena amene wayandikana nawo nyumba kumakhala nawo pa phunzirolo. Kapena tingamuuze kuti atiuze ngati pali ena amene tingaphunzire nawo Baibulo.​—Machitidwe 18:6-8.

Konzani Mpata Wopanga Ophunzira

11. Kodi tingawapeze kuti ophunzira atsopano?

11 Paulo ndi Akristu anzake anafuna kupanga ophunzira polalikira ku nyumba ndi nyumba, kumsika, ndi pamene ali paulendo​—inde, kulikonse. Monga wogwira ntchito ya Ufumu wachangu wofuna kupanga ophunzira, kodi mungawonjezere zimene mumachita mu utumiki wanu wakumunda? Kodi mungagwiritse ntchito mokwanira mpata womwe mwapeza kuti mufunefune oyenerera ndi kuwalalikira? Kodi ndi njira zina ziti zimene ofalitsa anzathu a uthenga wabwino apezera ophunzira? Choyamba tiyeni tione mbali yolalikira patelefoni.

12-14. Fotokozani chokumana nacho chanu kapena china chimene chili m’ndimezi posonyeza phindu la ulaliki wa patelefoni.

12 Mkristu wina amene tim’patse dzina lakuti Maria ali kulalikira ku nyumba ndi nyumba ku Brazil, anapereka thirakiti kwa mtsikana wina amene anali kutuluka m’nyumba ya pamdadada winawake. Pogwiritsa ntchito mutu wa thirakitilo monga poyambira nkhani, Maria anafunsa kuti, “Kodi mukufuna kudziŵa zambiri za Baibulo?” Mtsikanayo anayankha kuti: “Ndikufuna n’tadziŵa. Koma vuto n’lakuti ndine mphunzitsi, ndipo kuphunzitsa kumandithera nthaŵi yanga yonse.” Maria anam’fotokozera kuti akhoza kumakambirana nkhani za m’Baibulo patelefoni. Mtsikana uja anam’patsa Maria nambala yake ya telefoni, ndipo tsiku limenelo usiku, anayambitsa phunziro patelefoni pogwiritsa ntchito bulosha lakuti Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? *

13 Mtumiki wina wanthaŵi zonse wa ku Ethiopia akuchita ulaliki wa patelefoni, anadabwa kuti pamene anali kulankhula ndi mwamuna wina anali kumvanso phokoso chapansipansi. Mwamuna uja anamupempha kuti aimbenso nthaŵi ina. Mlongoyo ataimbanso, mwamuna uja anapepesa ndipo ananena kuti nthaŵi imene anaimba telefoni poyamba paja, iye ndi mkazi wake anali akukangana kwambiri. Mlongo uja anagwiritsa ntchito mawu ameneŵa monga mpata wonena malangizo anzeru amene Baibulo limapereka othetsera mavuto a m’banja. Anamuuza mwamuna uja kuti buku la Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova lathandiza mabanja ambiri. Patapita masiku angapo chim’patsireni buku lija, mlongo uja anamuimbiranso telefoni mwamuna uja. Mwamuna uja anati: “Buku limeneli lapulumutsa ukwati wanga!” Ndiponso, anasonkhanitsa pamodzi banja lake kuti aliuze mfundo zabwino zimene anaŵerenga m’bukulo. Anayambitsa phunziro la Baibulo lapanyumba, ndipo posapita nthaŵi mwamuna uja anayamba kupezeka pa misonkhano yachikristu nthaŵi zonse.

14 Wolengeza Ufumu ku Denmark amene anayambitsa phunziro la Baibulo polalikira patelefoni anati: “Woyang’anira utumiki anandilimbikitsa kuti ndizichita ulaliki wa patelefoni. Poyamba ndinkachita mantha, n’kumati:  ‘Imeneyi si mbali yanga.’ Komabe, tsiku lina ndinalimba mtima ndipo ndinayamba kuimba telefoni ku nyumba yoyamba. Sonja anayankha, ndipo titakambirana mwachidule, anavomera kulandira mabuku ofotokoza za m’Baibulo. Tsiku lina madzulo tinakambirana nkhani ya chilengedwe, ndipo anafuna kuŵerenga buku lakuti Life​—How Did It Get Here? By Evolution or by Creation. * Ndinamuuza kuti zingakhale bwino titakumana pamaso m’pamaso ndi kukambirana nkhaniyo. Iye anavomera. Nditapita kwawo, Sonja anali wokonzeka kuphunzira ndipo kuyambira nthaŵi imeneyo takhala tikuphunzira mlungu uliwonse.” Mlongo wathu wachikristuyo akuti: “Kwa zaka zambiri ndinkapemphera kuti ndipeze phunziro la Baibulo, koma sindinkayembekezera kulipeza polalikira patelefoni.”

15, 16. Kodi ndi zokumana nazo ziti zimene munganene zosonyeza phindu la kukhala wokonzeka kugwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana zoyambitsira maphunziro a Baibulo?

15 Anthu ambiri zinthu zikuwayendera bwino chifukwa chogwiritsa ntchito mfundo yolalikira anthu kulikonse kumene ali. Mkazi wina wachikristu ku United States anaimitsa galimoto yake pafupi ndi galimoto yamatola pamalo oimikapo galimoto. Mayi amene anali m’galimoto yamatolayo atamuona, mlongo uja anayamba kumufotokozera zimene timachita mu ntchito yathu yophunzitsa Baibulo. Mayiyo anamvetsera, n’kutsika m’galimoto muja, n’kupita pagalimoto ya mlongo uja. Iye anati: “Ndasangalala kuti munaima kuti mulankhule nane. Ndakhala nthaŵi yaitali ndisanapezeko mabuku anu ofotokoza za m’Baibulo. Komanso, ndikufuna kuyambiranso kuphunzira Baibulo. Kodi muziphunzira nane?” Chotero mlongo wathuyu anakonza mpata wabwino wouza ena uthenga wabwino.

16 Mlongo wina ku United States atapita ku nyumba yosungirako anthu okalamba ndi odwala anakumana ndi zotsatirazi: Analankhula ndi woyang’anira zinthu zina pamalowo n’kumuuza kuti akufuna kuthandiza mwauzimu anthu okhala pamalowo. Mlongo wathuyo anafotokozanso kuti angasangalale kumachititsa phunziro la Baibulo laulere mlungu uliwonse ndi anthu amene akufuna kuphunzira. Woyang’anirayo anamulola mlongoyo kupita m’zipinda za anthu osiyanasiyana pamalopo. Posapita nthaŵi, anali kuchititsa phunziro la Baibulo katatu pamlungu ndi anthu okwanira 26, mmodzi mwa iwo amakwanitsa kupezeka pa misonkhano yathu nthaŵi zonse.

17. Kodi ndi njira iti imene nthaŵi zambiri imakhala yabwino poyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba?

17 Olengeza Ufumu ena apeza zotsatira zabwino mwa kupempha anthu mwachidunji kuphunzira nawo Baibulo. Tsiku lina m’maŵa mpingo wina wa ofalitsa 105 unayesetsa kwambiri kupempha mwininyumba aliyense amene apeza kuti aziphunzira naye Baibulo. Ofalitsa 86 analoŵa mu utumiki wakumunda tsiku limenelo, ndipo atatha maola aŵiri mu ntchito yolalikira, anapeza kuti anayambitsa maphunziro osachepera 15.

Pitirizani Kufunafuna Oyenerera

18, 19. Kodi ndi malangizo ofunika ati a Yesu amene tiyenera kuwakumbukira, ndipo kuti tichite zimenezi tiyenera kutsimikiza mtima kuchita chiyani?

18 Monga wolengeza Ufumu, mungafune kuyesa mfundo zimene zatchulidwa m’nkhani ino. N’zoona kuti ndi bwino kulingalira miyambo ya m’dera lanu posankha njira yolalikirira. Koposa zonse, tiyeni tizikumbukira malangizo a  Yesu ofunafuna anthu oyenerera ndi kuthandiza anthu amenewo kukhala ophunzira.​—Mateyu 10:11; 28:19.

19 Kuti zimenezi zitheke, tiyeni ‘tilunjike nawo bwino mawu a choonadi.’ Tingachite zimenezi mwa kugwiritsa ntchito kwambiri Malemba okha basi pokopa ena. Zimenezi zidzatithandiza kuwafika pamtima anthu achidwi ndi kuwalimbikitsa kuchitapo kanthu. Pamene tipemphera ndi kudalira Yehova, tingagwire nawo ntchito yothandiza ena kukhala ophunzira a Yesu Kristu. Ndipo ntchito imeneyi ndi yopindulitsa kwambiri. Chotero tiyeni ‘tiyesetse kukhala ovomerezeka pamaso pa Mulungu,’ nthaŵi zonse tilemekeze Yehova monga olengeza Ufumu achangu, amene amalalikira ndi cholinga chopanga ophunzira.​—2 Timoteo 2:15, NW.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 12 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 14 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

Kodi Mukukumbukira?

• N’chifukwa chiyani Apolo anafunika kumufotokozera bwino kwambiri njira ya Mulungu?

• Kodi Priskila ndi Akula anaphunzira bwanji kwa mtumwi Paulo?

• Kodi m’Machitidwe chaputala 18, mwaphunziramo chiyani ponena za ntchito yopanga ophunzira?

• Kodi mungakonze bwanji mpata wopanga ophunzira?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 18]

Priskila ndi Akula ‘anam’fotokozera [Apolo] njira ya Mulungu mosamalitsa’

[Chithunzi patsamba 20]

Apolo anakhala waluso popanga ophunzira

[Chithunzi patsamba 21]

Paulo analalikira kulikonse kumene anapita

[Zithunzi patsamba 23]

Konzani mpata wolalikira