Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Ndi Chikhulupiriro, Baraki Anagonjetsa Gulu Lankhondo Lamphamvu

Ndi Chikhulupiriro, Baraki Anagonjetsa Gulu Lankhondo Lamphamvu

 Ndi Chikhulupiriro, Baraki Anagonjetsa Gulu Lankhondo Lamphamvu

YEREKEZERANI kuti mwayang’anizana ndi gulu la asilikali olusa kwambiri. Zida zawo ndi zamakono kwambiri, ndipo ali chire kuzigwiritsa ntchito. Malinga ndi mmene alili, inuyo ndiponso asilikali anzanu ndinu woti simungaimitsane nawo.

Izi n’zimene Baraki, Debora, ndi Aisrayeli anzawo okwana 10,000 anakumana nazo m’masiku a oweruza a Israyeli. Adani awo anali Akanani otsogoleredwa ndi Sisera, mkulu wa asilikali. Zina mwa zida zawo zankhondo zinali magaleta omwe kumawilo kwake kunali zikwakwa zoopsa kwambiri zachitsulo. Anakumanira pa Phiri la Tabori ndi ku mtsinje wa Kisoni. Zomwe zinachitika kumeneko zimasonyeza kuti Baraki anali munthu wachitsanzo chabwino cha chikhulupiriro. Taonani zomwe zinachitika kuti pakhale nkhondoyi.

Aisrayeli Afuulira Yehova

Buku la Oweruza limafotokoza za kusiya mobwerezabwereza kulambira koona komwe Aisrayeli ankachita ndiponso zotsatirapo zoopsa za zochita zawozo. Nthaŵi iliyonse, Aisrayeli akapempha Mulungu moonadi kuti awachitire chifundo, iye ankasankha mpulumutsi, n’kuwapulumutsa, kenako Aisrayeliwo n’kupandukanso. Ndendende ndi zimenezi, “ana a Israyeli anaonjeza kuchita choipa pamaso pa Yehova, atafa Ehudi,” woweruza amene anawapulumutsa kuti asaponderezedwe ndi Amoabu. Ndipotu “anasankha milungu yatsopano.” Chinatsatirapo n’chiyani? “Yehova anawagulitsa m’dzanja la Yabini mfumu ya Kanani, wochita ufumu ku Hazori; kazembe wake wa nkhondo ndiye Sisera . . . Ndipo ana a Israyeli anafuula kwa Yehova; pakuti [Sisera] anali nawo magareta achitsulo mazana asanu ndi anayi; napsinja ana a Israyeli kolimba zaka makumi aŵiri.”​—Oweruza 4:1-3; 5:8.

Pankhani ya mmene moyo unalili mu Israyeli, Malemba amati: “[Masiku amenewo] maulendo adalekeka ndi apanjira anayenda mopazapaza. Miraga idalekeka.” (Oweruza 5:6, 7) Anthu ankaopa achifwamba oyenda m’magaleta. “Anthu mu Israyeli ankakhala mwamantha, ndipo onse analibiretu nkhongono komanso ankasoŵa pogwira,” anatero katswiri wina wamaphunziro. Motero monga momwe ankachitira m’mbuyo mwake, Aisrayeliwo, omwe analibe nkhongono, anafuulira Yehova kuti awathandize.

Yehova Asankha Mtsogoleri

Kuponderezedwa ndi Akanani kunakhala vuto la Israyeli yense. Mulungu anagwiritsa ntchito mneneri wamkazi Debora kuuza anthu chiweruzo chake ndiponso malangizo ake. Motero Yehova anapatsa mayiyu mwayi wokhala mayi wophiphiritsa wa Israyeli.​—Oweruza 4:4; 5:7.

Debora anaitanitsa Baraki n’kumuuza kuti: “Kodi Yehova Mulungu wa Israyeli sanalamulira ndi kuti, Muka, nulunjike ku phiri la Tabori, nuwatenge, apite nawe anthu zikwi khumi a ana a Nafitali ndi ana a Zebuloni? Ndipo ndidzam’koka Sisera, kazembe wa nkhondo ya Yabini, akudzere  ku mtsinje wa Kisoni, ndi magareta ake, ndi aunyinji ake; ndipo ndidzam’pereka m’dzanja lako.” (Oweruza 4:6, 7) Ndi mawu oti ‘kodi Yehova Mulungu sanalamulira?’ Debora anasonyezeratu kuti alibe mphamvu iliyonse pa Baraki. Iye anangokhala njira yom’dziŵitsira lamulo la Mulungu. Kodi Baraki anati chiyani?

“Ukamuka nane, ndidzamuka; ukapanda kumuka nane, sindimuka,” anatero Baraki. (Oweruza 4:8) N’chifukwa chiyani Baraki sanangovomera kamodzi n’kamodzi ntchito yomwe Mulungu anam’patsayi? Kodi anali ndi mantha? Kodi sankakhulupirira malonjezo a Mulungu? Ayi, sikuti Baraki anakana ntchitoyi, kapenanso kuti sanamvere Yehova. M’malomwake, kuyankha kwake kukusonyeza kuti iye sankadziona woyenerera kuchita yekha lamulo la Mulungu. Kukhalapo kwa woimira Mulungu kukanam’tsimikizira kuti Mulungu am’tsogolera komanso iye ndi anthu ake akanalimbikitsidwa. Motero, m’malo mosonyeza kuchita mantha, zimene Baraki ananena zinali umboni woti anali ndi chikhulupiriro cholimba.

Zomwe Baraki anachitazi zikufanana ndi zija zomwe Mose, Gideoni, ndi Yeremiya anachita. Amuna ameneŵa nawonso ankadzikayikira kuti angachite zomwe Mulungu wawauza. Koma sikuti iwo anaonedwa monga anthu achikhulupiriro chochepa chifukwa cha zimenezi. (Eksodo 3:11–4:17; 33:12-17; Oweruza 6:11-22, 36-40; Yeremiya 1:4-10) Nanga tinganenenji pa zimene Debora anachita? Sanayerekeze n’komwe kutenga ulamuliro. M’malomwake anakhalabe mtumiki wodzichepetsa wa Yehova. Anauza Baraki kuti: “Kumuka ndidzamuka nawe.” (Oweruza 4:9) Analolera kuchoka kunyumba, malo otetezedwa kwambiri, n’kukakhala ndi Baraki pankhondo yomwe inali pafupi. Nayenso Debora ndi chitsanzo cha munthu wachikhulupiriro ndi wolimba mtima.

Atsatira Baraki ndi Chikhulupiriro

Pamalo omwe asilikali a Israyeli anakumanirana panali paphiri loonekera bwino lotchedwa Tabori. Anasankha malo abwino kwambiri. Anali malo amene nthaŵi zonse mafuko a Nafitali ndi Zebuloni, omwe ankakhala chakufupi, ankachitirapo misonkhano yawo. Ndiye malinga ndi mmene Mulungu anawauzira, amuna odzipereka okwana zikwi khumi, pamodzi ndi Debora, anatsatira Baraki kupita paphiripo.

Onse amene anali ndi Baraki anafunikira kukhala ndi chikhulupiriro. Yehova anali atalonjeza Baraki kuti adzagonjetsa Akanani, koma kodi Aisrayeli anali ndi zida zotani? Oweruza 5:8 amati: ‘Chikopa kapena nthungo sizidaoneke mwa zikwi makumi anayi a Israyeli.’ Motero Aisrayeli analibe zida zokwanira. Ngakhale kuti zinali choncho, nthungo ndi zikopa sizikanafanana m’pang’ono pomwe ndi magaleta ankhondo okhala ndi zikwakwa. Atamva kuti Baraki wapita kuphiri la Tabori, Sisera mwamsangamsanga anasonkhanitsira magaleta ake onse pamodzi ndi asilikali ake kumtsinje wa Kisoni. (Oweruza 4:12, 13) Zomwe iye sanazindikire ndi zoti akukamenyana ndi Mulungu Wamphamvuyonse.

Baraki Agonjetsa Ankhondo a Sisera

Nthaŵi ya nkhondoyo itakwana, Debora anauza Baraki kuti: “Nyamuka; pakuti ili ndi tsikuli Yehova wapereka Sisera m’dzanja lako; sanatuluka kodi Yehova pamaso pako?” Baraki ndi asilikali ake anafunika kuchoka pamwamba pa phiri la Tabori n’kutsikira kuchigwa, komano kuchigwako n’kumene magaleta a Sisera angagwire ntchito bwino kwambiri. Mukanakhala nawo pa asilikali a Baraki, kodi mukanamva bwanji? Pokumbukira kuti malangizowo achoka kwa Yehova, kodi simukananyinyirika? Baraki ndi anthu ake zikwi khumi anamvera. “Ndipo  Ambuye anawononga Sisera, ndi magareta onse ndi gulu lankhondo lonse, ndi lupanga lakuthwa pamaso pa Baraki.”​—Oweruza 4:14, 15.

Ndi thandizo la Yehova, Baraki anagonjetsa ankhondo a Sisera. Nkhani yosimba za nkhondoyi sifotokoza zonse zomwe zinachitika. Komabe, nyimbo ya Baraki ndi Debora yosangalalira kuti apambana imati, ‘thambo ndi mitambo zinakha madzi.’ Mwachionekere, mvula yamkuntho inapangitsa kuti magaleta a Sisera atitimire m’matope, zomwe zinapatsa mwayi Baraki. Motero chida chankhondo champhamvu cha Akanani sichinagwire ntchito. Pankhani ya mitembo ya amuna a Sisera, nyimboyo imati: ‘Mtsinje wa Kisoni unaikokolola.’​—Oweruza 5:4, 21.

Kodi zimenezi n’zoona? Mtsinje wa Kisoni ndi khwawa lomwe nthaŵi zambiri siliyenda madzi ambiri. Kaŵirikaŵiri, mitsinje yotere imadzaza mwadzidzi n’kuyamba kuthamanga kwambiri kukagwa mvula yamkuntho kapena mvumbi ndipo imakhala yoopsa. Pankhondo yoyamba ya padziko lonse, mvula ya mphindi 15 zokha m’dera lomweli, lomwe nthaka yake ndi yamakande, akuti inasokoneza ulendo wa asilikali apakavalo. Nkhani ya nkhondo yomwe inalipo pakati pa Napoleon ndi Ateke yomwe anamenyera pa Phiri la Tabori pa April 16, 1799, imati “pamene Ateke ankathaŵa, ambiri anamira powoloka mbali ina ya chigwachi chomwe chinasefukira madzi a m’Kisoni.”

Wolemba mbiri wachiyuda, Flavius Josephus anati ankhondo a Sisera ndi Baraki atatsala pang’ono kukumana, “panafika namondwe wamkulu wochoka kumwamba, anafika ndi mvula yambiri ndiponso matalala adzaoneni, ndipo kunawomba mphepo yomwe inapangitsa kuti mvulayo iziwawomba kumaso Akanani, n’kuwachititsa chidima, moti mivi ndi zoponyera miyala zawo sizinawathandize.”

Oweruza 5:20 amati: “Nyenyezi zinathira nkhondo yochokera kumwamba, m’mipita mwawo zinathirana ndi Sisera.” Kodi nyenyezi zinam’thira nkhondo motani Sisera? Ena amaona mawu ameneŵa kuti amafotokoza za thandizo la Mulungu. Ena amaganiza za thandizo la angelo, kugwa kwa miyala kuchokera kumwamba, kapena maulosi amene analephera kukwaniritsidwa omwe Sisera ankadalira chifukwa chokhulupirira nyenyezi. Poti Baibulo silifotokoza mmene nyenyezi zinamenyera nkhondoyi, m’pomveka kuwatenga mawuŵa kuti akutanthauza kuti Mulungu anawamenyera nkhondo asilikali a Israyeli mwanjira inayake. Mulimonse mmene zinalilimo, Aisrayeli anapezerapo mwayi pa zimenezi. “Baraki anatsata magareta . . . ndi gulu lonse lankhondo la Sisera linagwa ndi lupanga lakuthwa, sanatsala munthu ndi mmodzi yense.” (Oweruza 4:16) N’chiyani chinachitikira Sisera, mkulu wa asilikali?

Wopondereza Agwera “M’dzanja la Mkazi”

Baibulo limati: “Koma Sisera [anaisiya nkhondo ndipo] anathaŵira choyenda pansi ku hema wa Yaeli mkazi wa Heberi Mkeni; pakuti panali mtendere pakati pa Yabini mfumu ya Hazori, ndi nyumba ya Heberi Mkeni.” Yaeli anapempha Sisera, yemwe anali atatopa, kuti aloŵe m’hema wake, nam’patsa mkaka kuti amwe, ndi kum’fundika, moti anagona. Kenako Yaeli “anatenga chichiri cha hema, natenga nyundo m’dzanja lake,” zinthu zomwe munthu wokhala m’mahema amagwiritsa ntchito kaŵirikaŵiri. “Nam’dzera monyang’ama, nakhomera chichiri chiloŵe m’litsipa mwake; nichinapyoza  kuloŵa m’nthaka; popeza anali mtulo tofa nato ndi kulema; nafa.”​—Oweruza 4:17-21.

Kenako Yaeli anatuluka kukachingamira Baraki ndi kumuuza kuti: “Idza kuno, ndidzakuonetsa munthu um’funayo.” Nkhaniyo imanenanso kuti: “Potero anam’dzera, ndipo taonani, Sisera wagwa, wafa, ndi chichiri m’litsipa mwake.” Zimenezi ziyenera kuti zinalimbitsa kwambiri chikhulupiriro cha Baraki! Poyambirira, Debora, mneneri wamkazi anamuuza kuti: “Ulendo umukawo, sudzachita nawo ulemu; pakuti Yehova adzagulitsa Sisera m’dzanja la mkazi.”​—Oweruza 4:9, 22.

Kodi tinganene kuti Yaeli anachita chinyengo? Yehova sanazione choncho. “Akhale wodalitsika woposa akazi a m’hema,” imatero nyimbo ya Baraki ndi Debora yosangalalira kuti apambana. Nyimboyi imatithandiza kusakhala ndi malingaliro olakwika pa imfa ya Sisera. Amayi ake akuwafotokoza kuti akuyembekezera kwambiri kubwerako kwa Sisera kuchoka kunkhondoyo. Iwo akufunsa kuti: “Achedweranji galeta wake?” ‘Akazi anzawo omveka anzeru’ akuyesa kuwalimbitsa mtima powauza kuti akugaŵa katundu yemwe apeza pankhondo, nsalu zokongola kwambiri zamawangamawanga ndiponso kugaŵa atsikana kwa amuna. Akaziwo akufunsa kuti: “Sanagaŵa zofunkha? Namwali, anamwali aŵiri kwa munthu aliyense. Chofunkha cha nsalu zamawangamawanga kwa Sisera . . . Nsalu zamawangamawanga, za maluŵa konsekonse, kwa chofunkha cha khosi lake.”​—Oweruza 5:24, 28-30.

Zomwe Tikuphunzirapo

Nkhani ya Baraki imatiphunzitsa zinthu zofunika kwambiri. Mosakayikira, onse osaganizira Yehova m’miyoyo yawo adzakumana ndi mavuto ndiponso adzagwira fuwa lamoto. Olapa ndi kubwerera kwa Mulungu ndi kum’khulupirira angathe kumasulidwa ku zinthu zamitundumitundu zowapanikiza. Komanso kodi sitiyenera kukhala omvera? Ngakhale pamene zofuna za Mulungu zikusemphana ndi maganizo a munthu, tingakhale ndi chikhulupiriro chakuti malangizo ake ngopindulitsa kwambiri nthaŵi zonse. (Yesaya 48:17, 18) Baraki ‘anapitikitsa magulu a nkhondo achilendo’ chifukwa choti ankakhulupirira Yehova ndiponso anamvera malangizo ake basi.​—Ahebri 11:32-34.

Mawu ogwira mtima otseka nyimbo ya Debora ndi Baraki ngakuti: “Adani anu onse, Yehova, atayike momwemo. Koma iwo akukonda inu akhale ngati dzuŵa lotuluka mu mphamvu yake.” (Oweruza 5:31) N’zomwe zidzachitike Yehova akadzawononga dziko loipa la Satanali!

[Chithunzi patsamba 29]

Yehova anagwiritsa ntchito Debora kuti aitane Baraki

[Chithunzi patsamba 31]

Mtsinje wa Kisoni utasefukira kumagombe ake

[Mawu a Chithunzi]

Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.

[Chithunzi patsamba 31]

Phiri la Tabori