Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Kodi munthu amene akufuna kubatizidwa koma ali ndi chilema chachikulu kapena thanzi lake silili bwino zimene zingachititse kumizidwa kukhala kovuta angafunikirebe kum’miza thupi lonse m’madzi?

Liwu lakuti “kubatiza” lachokera ku liwu lachigriki lakuti baʹpto, limene limatanthauza “kusunsa.” (Yohane 13:26) M’Baibulo, liwu lakuti “kubatiza” n’lofanana ndi “kumiza.” Baibulo la The Emphasised Bible la Rotherham, pofotokoza za ubatizo wa mdindo wa ku Etiopia amene anabatizidwa ndi Filipo, limati: “Onse anapita kumadzi, Filipo ndi mdindoyo,​—ndipo anam’miza.” (Machitidwe 8:38) Motero, munthu amene akubatizidwa amamizidwa m’madzi.​—Mateyu 3:16; Marko 1:10.

Yesu analangiza ophunzira ake kuti: “Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo.” (Mateyu 28:19, 20) Potsatira langizo limeneli, Mboni za Yehova zimabatiza m’maiŵe, m’nyanja, m’mitsinje, kapena malo ena kumene kuli madzi okwanira kumiza thupi lonse. Popeza Malemba amanena kuti munthu afunika kubatizidwa mwa kum’miza thupi lonse, anthu alibe mphamvu zopatula munthu wina pa ubatizo wotero. Motero, munthu ayenerabe kubatizidwa ngakhale kuti pangafunikire kutsatira njira zina zachilendo chifukwa cha vuto lake. Mwachitsanzo, ubatizo wochitira m’bafa lalikulu wathandiza kwambiri anthu okalamba kapena omwe sanali kupeza bwino. Madzi a m’bafalo angafunditsidwe, munthu wofuna kubatizidwayo n’kumuika pang’onopang’ono m’madziwo ndipo akawazoloŵera, ubatizo weniweni ungachitike.

Ngakhale anthu azilema zazikulu abatizidwa. Mwachitsanzo, anthu amene anawachita opaleshoni ya kholingo ndipo chifukwa cha opaleshoniyo ali ndi bowo losatsekeka pam’mero abatizidwapo, kapenanso anthu amene amagwiritsa ntchito makina popuma. Komabe, pochita maubatizo otereŵa pamafunikira kukonzekera bwinobwino. Ndi bwino kuti pakhale nesi wodziŵa bwino ntchito yake kapena dokotala, ngati alipo. Komabe, ngati anthu asamala kapena kutsatira njira zotetezera, munthu aliyense angabatizidwe. Motero, m’pofunika kuchita zonse zotheka kuti munthu abatizidwe m’madzi ngati mwiniyo akufuna ndi mtima wonse ndiponso ngati avomera kuti atero ngakhale kuti pakhoza kuchitika zovuta zina pom’batizapo.