Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kupeza Choonadi pa Malo Osayembekezeka

Kupeza Choonadi pa Malo Osayembekezeka

 Olengeza Ufumu Akusimba

Kupeza Choonadi pa Malo Osayembekezeka

MULUNGU akufuna kuti “anthu onse apulumuke, nafike pozindikira choonadi.” (1 Timoteo 2:3, 4) Kuti izi zitheke, Mboni za Yehova zasindikiza ndiponso kufalitsa mabaibulo ndi mabuku ophunzirira Baibulo miyandamiyanda. Nthaŵi zina, mabuku ameneŵa athandiza anthu oona mtima kuphunzira choonadi mosayembekezeka. Pankhani imeneyi, olengeza Ufumu mumzinda wa Freetown ku Sierra Leone akusimba zotsatirazi.

Osman anali mwana wachiŵiri m’banja la ana asanu ndi anayi. Popeza anakulira m’banja la chipembedzo, iye nthaŵi zonse ankapita kukalambira pamodzi ndi bambo ake. Komabe Osman ankavutika maganizo kwambiri ndi zomwe chipembedzo chake chinkaphunzitsa pankhani ya helo. Sankamvetsa kuti zimatheka bwanji Mulungu wachifundo kumazunza anthu oipa mwa kuwatentha pa moto. Zonse zomwe Osman anamuuza pofuna kuti amvetse chiphunzitso cha moto wa helo sizinamugwire mtima.

Tsiku lina Osman ali ndi zaka makumi aŵiri, anaona buku la bluu litakwiririka mbali imodzi pazinyalala. Popeza ankakonda mabuku kwambiri, iye analitola, n’kulipukuta ndipo anaona mutu wake wakuti​—Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya. *

‘Ichinso ndiye choonadi chiti?’ anadzifunsa motero Osman. Pofuna kudziŵa zambiri, Osman anatenga bukulo kupita nalo kunyumba n’kukaliŵerenga lonse mwamsanga. Analitu wokondwa kwambiri kudziŵa kuti Mulungu ali ndi dzina ndipo dzinalo ndi Yehova. (Salmo 83:18) Osman anadziŵanso kuti khalidwe lalikulu la Mulungu ndilo chikondi ndiponso kuti ngakhale mfundo yoti Iye amalanga anthu pa moto imamunyansa kwambiri. (Yeremiya 32:35; 1 Yohane 4:8) Kenako, Osman anaŵerenga kuti Yehova posachedwapa adzabweretsa dziko lapansi la paradaiso limene anthu adzakhalemo kosatha. (Salmo 37:29; Chivumbulutso 21:3, 4) Choonadi chabwinotu kwambiri chimenechi kuchokera kwa Mulungu wachifundo ndiponso wachikondi. Osman ndi mtima wonse, anathokoza Yehova kwambiri chifukwa chomulola kupeza choonadi pa malo osayembekezeka.

Patapita masiku angapo, anzake a Osman anamuthandiza kupeza Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova ndipo anapezeka pamsonkhano kwanthaŵi yake yoyamba. Ali komweko, anapempha Mboni ina kuti iziphunzira naye Baibulo. Ngakhale kuti a m’banja lake anali kum’tsutsa, Osman anapitirizabe kukula mwauzimu mpaka anabatizidwa. (Mateyu 10:36) Tsopano ndi mkulu mumpingo. N’zochititsatu chidwi kwambiri kuti zonsezi zinatheka chifukwa chopeza buku lofotokoza Baibulo kudzala.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova mu 1968.