Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Kodi kudzoza “Malo Opatulikitsa” komwe Danieli 9:24 analosera, kunachitika liti?

Danieli 9:24-27 ndi ulosi wonena za kuonekera kwa Kristu​—‘Kalonga Wodzozedwayo.’ Ulosi wa kudzozedwa kwa “Malo Opatulikitsa,” sukutanthauza kudzozedwa kwa chipinda Chopatulikitsa cha m’kachisi wa ku Yerusalemu. Mmalo mwake, mawu akuti “Malo Opatulikitsa” akunena za malo opatulika a Mulungu kumwamba​—Malo Opatulikitsa m’kachisi wamkulu wauzimu wa Yehova kumwamba. *​—Ahebri 8:1-5; 9:2-10, 23.

Kodi kachisi wa Mulungu wauzimu anayamba liti kugwira ntchito? Chabwino, talingalirani zomwe zinachitika paubatizo wa Yesu mu 29 C.E. Kuyambira pamenepo mpaka m’tsogolo, Yesu anakwaniritsa mawu a pa Salmo 40:6-8. Pambuyo pake, mtumwi Paulo anasonyeza kuti Yesu anapemphera kwa Mulungu kuti: “Nsembe ndi chopereka simunazifuna, koma thupi munandikonzera Ine.” (Ahebri 10:5) Yesu anadziŵa kuti Mulungu ‘sanafune’ kuti nsembe za nyama zipitirize kuperekedwa pa kachisi ku Yerusalemu. Koma mmalo mwake, Yehova anakonzera Yesu thupi langwiro kuti alipereke nsembe. Pofotokoza kufunitsitsa kochokera mu mtima, Yesu anapitiriza kuti: “Taonani, ndafika, (Pamutu pake pa buku palembedwa za Ine) kudzachita chifuniro chanu, Mulungu.” (Ahebri 10:7) Kodi Yehova anamuyankha motani? Uthenga wabwino wa Mateyu umati: “Yesu, pamene anabatizidwa, pomwepo anatuluka m’madzi: ndipo onani, miyamba inam’tsegukira iye, ndipo anapenya Mzimu wa Mulungu wakutsika ngati nkhunda nudza nutera pa iye; ndipo onani, mawu akuchokera kumiyamba akuti, Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa iyeyu ndikondwera.”​—Mateyu 3:16, 17.

Pamene Yehova Mulungu anavomereza thupi la Yesu kuti liperekedwe nsembe, zinatanthauza kuti guwa la nsembe lalikulu kuposa la m’kachisi wa ku Yerusalemu, lakhazikitsidwa. Ili linali guwa la “chifuniro” cha Mulungu, kapena kuti dongosolo la kulandira nsembe ya moyo waumunthu wa Yesu. (Ahebri 10:10) Kudzoza Yesu ndi mzimu woyera, kunatanthauza kuti tsopano Mulungu wakhazikitsa dongosolo lonse la kachisi wauzimu. * Choncho paubatizo wa Yesu, malo a kumwamba a Mulungu anadzozedwa, kapena kuti kupatulidwa, monga “Malo Opatulikitsa” m’dongosolo la kachisi wamkulu wauzimu.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Nkhani yofotokoza mbali zosiyanasiyana za kachisi wauzimu wa Mulungu, ili mu Nsanja ya Olonda ya July 1, 1996 masamba 14 mpaka 19.

^ ndime 5 Nkhaniyi inafotokozedwa patsamba 195 m’buku lakuti Samalani Ulosi wa Danieli!

[Chithunzi patsamba 27]

Malo Opatulikitsa” anadzozedwa pamene Yesu anabatizidwa