Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Nkhani Yosautsa ya Kuvutika kwa Anthu

Nkhani Yosautsa ya Kuvutika kwa Anthu

 Nkhani Yosautsa ya Kuvutika kwa Anthu

“TINALAKWANJI MULUNGU TINALAKWANJI?” Umenewo unali mutu wankhani patsamba loyamba la nyuzipepala ina yotchuka kwambiri chitachitika chivomezi chomwe chinawononga kwambiri ku Asia Minor. Chithunzi chomwe chinali patsamba lomwelo chinasonyeza bambo akusolola mwana wake wamkazi wovulala m’nyumba yawo yomwe inagwa.

Nkhondo, chilala, miliri, ndiponso masoka achilengedwe zachititsa mavuto adzaoneni, misozi yosalekeza, ndi imfa zosaŵerengeka. Kuwonjezera apo, palinso vuto la kugwirira chigololo, uchidyamakanda, ndi zoipa zina. Taganizirani za anthu ambirimbiri amene amavulala ndi kufa pangozi. Ndipo ena miyandamiyanda akuvutika chifukwa cha matenda, ukalamba, ndi imfa za okondedwa awo.

Zaka za m’ma 1900 ndizo zakhala zamavuto adzaoneni kuposa zaka zonse m’mbuyomu. Kungoyambira mu 1914 mpaka 1918, nkhondo yoyamba ya padziko lonse inapha asilikali pafupifupi mamiliyoni khumi. Olemba mbiri ena amanena kuti nkhondoyo inapha anthu wamba oposa pamenepa. M’nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse, asilikali ndiponso anthu wamba pafupifupi 50 miliyoni kuphatikizapo amayi, ana, ndi okalamba miyandamiyanda anaphedwa. M’zaka zonse za m’ma 1900 zapitazi, anthu ambiri akhala akuphedwa mwachisawawa, kuvutika ndi nkhondo zapachiŵeniŵeni, chiwawa, njala, ndi umphaŵi. Buku lotchedwa Historical Atlas of the Twentieth Century limanena kuti, anthu pafupifupi 180 miliyoni anafa chifukwa cha “zinthu zoipazi.”

Fuluwenza yachispanya ya m’chaka cha 1918 mpaka 1919, inapha anthu 20 miliyoni. Zaka makumi aŵiri zapitazi, anthu pafupifupi 19 miliyoni afa ndi matenda a AIDS ndipo ena 35 miliyoni ali ndi kachilombo koyambitsa matendaŵa. Ana miyandamiyanda akutsala amasiye chifukwa chakuti makolo awo anamwalira ndi AIDS. Ndipo ana osaŵerengeka akumwalira ndi AIDS yomwe amayi awo anawapatsira asanabadwe.

Ana akuvutikanso m’njira zina. Poona zomwe bungwe loona za ana padziko lonse la United Nations Children’s Fund (UNICEF) linanena kumapeto kwa 1995, nyuzipepala ya ku England yotchedwa Manchester Guardian Weekly inati: “Nkhondo zomwe zachitika m’zaka khumi zapitazi zapha ana mamiliyoni aŵiri ndi kulumaza ena pakati pa mamiliyoni anayi kapena asanu. Ana 12 miliyoni analibe nyumba zokhalamo, ndipo ena opitirira miliyoni imodzi ndi amasiye kapena anawalekanitsa ndi makolo awo. Komanso ena mamiliyoni khumi zinawasokoneza maganizo.” Kuwonjezera apo, anthu pafupifupi 40 mpaka 50 miliyoni padziko lonse amachotsa mimba pa chaka.

Kodi M’tsogolo Muli Zotani?

Anthu ambiri amaona kuti chinachake choopsa chidzachitika m’tsogolo. Kagulu kena ka asayansi kananena kuti: “Zochita za anthu . . . zidzasintha dzikoli kwakuti  silidzathanso kuchirikiza moyo m’njira yomwe tikudziŵa.” Powonjezera iwo anati: “Ngakhale panopa, munthu mmodzi mwa anthu asanu alionse ali paumphaŵi wadzaoneni wochita kusoŵa ndi chakudya chomwe, ndipo mmodzi mwa anthu khumi alionse akudwala matenda osoŵa zakudya m’thupi.” Asayansi anagwiritsa ntchito zochitikazi “kuchenjezera anthu onse pa zomwe zili m’tsogolo.” Iwo anati: “Ngati tikufuna kuti tsoka lalikulu lisagwere mtundu wa anthu komanso kuti dziko lathuli lisawonongeke kotheratu, kusintha kwakukulu kokhudza udindo wathu wosamalira dzikoli ndi zamoyo zake n’kofunika kwambiri.”

N’chifukwa chiyani Mulungu walola kuvutika ndi kuipa kotereku? Kodi wakonza motani njira zothetsera mavutoŵa? Ndipo adzawathetsa liti?

[Mawu a Chithunzi patsamba 3]

Chithunzi cha njinga ya olumala chili pamwambapa: UN/​DPI Photo 186410C chojambulidwa ndi P.S. Sudhakaran; mwana wosoŵa zakudya ali pakatiyo: WHO/​OXFAM; bambo wowonda kwambiri ali m’munsiyo: FAO photo/​B. Imevbore