Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Kodi Akristu oona ayenera kuchiona motani chizoloŵezi chofala chopatsana ulere mapulogalamu ogulitsa a pakompyuta?

Ena angadzikhululukire mwa kutchula mawu a Yesu akuti: “Munalandira kwaulere, patsani kwaulere.” Koma kumeneku kungakhale kulakwitsa. Yesu sanali kunena za kupatsa ena makope aulere a mabuku kapena mapulogalamu a pakompyuta amene eni ake owapanga analetsa kuwakopera, amenenso amakhudzidwa ndi malamulo ena a boma. Iye anali kunena za kupatsa mu utumiki. Yesu anauza atumwi amene anali kupita m’mizinda ndi m’midzi yosiyanasiyana kuti akalalikire za Ufumu, akachiritse odwala, ndi kutulutsa ziwanda. M’malo mofuna malipiro pa zimenezi, atumwiwo anayenera ‘kupatsa kwaulere.’​—Mateyu 10:7, 8.

Mmene makompyuta ayamba kuchuluka m’manyumba ndi m’makampani, anthu ambiri akufuna mapulogalamu a pakompyuta. Nthaŵi zambiri mapulogalamuwa amakhala ogulitsa. Zoonadi, anthu ena amalemba mapulogalamu aulere, ndipo amanenanso kuti wofuna atha kukopera ndi kugaŵiranso ena. Koma mapulogalamu ochuluka apakompyuta amakhala ogulitsa. Kaya ndi mapulogalamu okagwiritsa ntchito kunyumba kapena ndi ofunikira kuntchito, owafunawo ayenera kugula. Wina atatenga kapena kukopera mapulogalamu ena popanda malipiro, umenewo ndi mlandu, monga momwenso zilili ndi kukopera mabuku athunthu ambiri, ngakhale kuti zinthu zokopedwazo angazipereke kwa ena mwaulere.

Mapulogalamu ochuluka apakompyuta (kuphatikizapo maseŵera apakompyuta) amafuna laisensi, ndipo mwiniwake kapena amene akuwagwiritsa ntchito ayenera kutsatira mfundo za laisensiyo. Malaisensi ochuluka otere amaneneratu kuti pulogalamuyo ndi ya munthu mmodzi basi. Nthaŵi zambiri zimatanthauza kuti ingaikidwe pakompyuta imodzi yokha, kaya ndi kunyumba kapena kuntchito kapena kusukulu. Malaisensi ena amalola mwiniwakeyo kusunga kope linanso lapadera, koma asapangire anthu ena makope. Ngati mwiniwakeyo akufuna kupatsa wina pulogalamu yonse (kuphatikizapo laisensi yake ndi malangizo ake), angathe kutero. Komano ndiye kuti iyeyo alibenso ulamuliro woigwiritsa ntchito. Pali malaisensi mitundumitundu, chotero munthu amene akugula kapena kupatsidwa pulogalamu ayenera kufufuza kuti laisensi yake ikuti chiyani.

Mayiko ambiri ali ndi malamulo oletsa kukopera zinthu zomwe munthu anapanga ndi luso lake monga mapulogalamu a pakompyuta, ndipo amaonetsetsa kuti anthu akuwatsatira. Mwachitsanzo, pa January 14, 2000, nyuzipepala ya New York Times inanena kuti “apolisi a ku Germany ndi a ku Denmark agwira anthu a gulu lina lalikulu lochita zaukatangale ndi mapulogalamu ndi maseŵera a pakompyuta” mwa kukopera ndi kugaŵira anthu ena, ngakhalenso kuwagulitsa pa Intaneti.

Kodi mpingo wachikristu ukuima pati pankhani imeneyi? Yesu anati: “Perekani zake za Kaisara kwa Kaisara, ndi zake za Mulungu kwa Mulungu.” (Marko 12:17) Zimenezi zimafuna kuti Akristu azilabadira malamulo a dziko lawo omwe sawombana ndi lamulo la Mulungu. Ponena za maboma, mtumwi Paulo analemba kuti: “Anthu onse amvere maulamuliro aakulu . . . Iye amene atsutsana nawo ulamuliro, akaniza choikika ndi Mulungu; ndipo iwo akukaniza, adzadzitengera kulanga.”​—Aroma 13:1, 2.

Akulu mumpingo wachikristu sanaikidwe kuti aziona zimene zili pamakompyuta a ena, ngati kuti anapatsidwa mphamvu zofotokozera ena malamulo oteteza mapulogalamu a pakompyuta ndi kuonetsetsa kuti anthu akuwatsatira. Koma iwo amakhulupirira ndipo amaphunzitsa kuti Akristu sayenera kutenga chinthu ngati si chawo ndipo ayenera kuyesetsa kutsatira malamulo. Zimenezi zimateteza Akristu kuti asalangidwe monga oswa malamulo, ndipo zimawathandiza kukhala ndi chikumbumtima chabwino kwa Mulungu. Paulo analemba kuti: “Chifukwa chake, kuyenera kuti mukhale omvera, si chifukwa cha mkwiyo wokha, komanso chifukwa cha chikumbumtima.” (Aroma 13:5) Paulo ananenanso chifuno cha Akristu oona ndi mawu akuti: “Takopeka mtima kuti tili nacho chikumbumtima chokoma m’zonse, pofuna kukhala nawo makhalidwe abwino.”​—Ahebri 13:18.

[Bokosi patsamba 29]

Makampani ndi masukulu ena amagula mapulogalamu amene malaisensi awo amatchula chiŵerengero cha anthu amene akuloledwa kuwagwiritsa ntchito. Mu 1995, mipingo ya Mboni za Yehova m’mayiko ena inakambirana nkhani imene inali ndi uphungu uwu:

“Makampani ambiri amene amapanga ndi kugulitsa mapulogalamu a kompyuta amaletsa kukopera popanda chilolezo ndipo amapereka laisensi yolongosola mmene mapulogalamuwo angawagwiritsire ntchito. Kaŵirikaŵiri laisensiyo imanena kuti mwiniwake sayenera kupatsa ena makope a pulogalamuyo; ndipotu lamulo la padziko lonse lokhudza kukopera zinthu zopangidwa ndi ena limaletsanso zimenezo. . . . Makampani ena aakulu amagulitsa makompyuta okhala ndi mapulogalamu ndi malaisensi ake. Komabe, ogulitsa makompyuta ena samapereka malaisensi chifukwa chakuti mapulogalamu amene amaikamo amakhala akatangale, kutanthauza kuti wogulayo amaswa lamulolo mwa kugwiritsira ntchito mapulogalamuwo. Mogwirizana ndi zimenezi, Akristu ayenera kupeŵa kuika kapena kutenga pa makompyuta zinthu zoletsedwa kuzikopera (monga momwe zofalitsa za Sosaite zilili) ndi zimene amazikopera popanda chilolezo cha eni ake.”