Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mipukutu ya ku Nyanja Yakufa—N’chifukwa Chiyani Muyenera Kuchita Nayo Chidwi?

Mipukutu ya ku Nyanja Yakufa—N’chifukwa Chiyani Muyenera Kuchita Nayo Chidwi?

 Mipukutu ya ku Nyanja Yakufa​—N’chifukwa Chiyani Muyenera Kuchita Nayo Chidwi?

Asanapeze Mipukutu ya ku Nyanja Yakufa, zolembedwa zakale kwambiri za Malemba Achihebri zinali za m’zaka za m’ma 800 ndi m’ma 900 C.E. Kodi zolembedwa zimenezi zinalidi zodalirika kuti zikupereka Mawu a Mulungu monga momwedi ayenera kukhalira? Tikufunsa choncho chifukwa chakuti Malemba Achihebri anamalizidwa kulembedwa zaka 1000 zolembedwazo zisanakhalepo. Pulofesa Julio Trebolle Barrera, wa m’gulu la akonzi a Mipukutu ya ku Nyanja Yakufa ochokera m’mayiko osiyanasiyana anati: “Mpukutu wa Yesaya [wotengedwa ku Qumran] ukusonyeza umboni wosatsutsika wakuti malemba a m’Baibulo alembedwa mokhulupirika ndi mosamala kwambiri ndi okopera malemba achiyuda pazaka zoposa sauzande imodzi.”

MPUKUTU umene Barrera akunena uli ndi buku lonse la Yesaya. Pakali pano, pakati pa zolembedwa pamanja za Baibulo zoposa 200 zomwe anazipeza ku Qumran, papezeka zigawo za buku lina lililonse la m’Malemba Achihebri kusiyapo buku la Estere. Mosiyana ndi mpukutu wa Yesaya, mipukutu ya mabuku ochuluka imangopezeka zidutswa zake, zomwe zili ndi malemba ochepa kwambiri a mabukuwo. Mabuku a m’Baibulo amene anali otchuka kwambiri ku Qumran anali Masalmo (makope 36), Deuteronomo (makope 29), ndi Yesaya (makope 21). Amenewanso ndiwo mabuku ogwidwa mawu kwambiri m’Malemba Achigiriki Achikristu.

Ngakhale kuti mipukutuyo ikusonyeza kuti Baibulo silinasinthe kwambiri, ikusonyezanso kuti panali mabaibulo achihebri olembedwa mosiyanasiyana amene Ayuda anali kugwiritsa ntchito m’nthaŵi ya Kachisi Wachiŵiri. Mawu a m’mipukutu ina ndi osiyana ndi malemba a Amasorete m’kalembedwe kake. Mipukutu ina ikufanana kwambiri ndi Septuagint yachigiriki. Kumbuyoku, akatswiri anali kuganiza kuti mawu a mu Septuagint osiyana ndi mabaibulo ena anali olakwika kapena kuti wotembenuza anawonjezamo malingaliro ake. Tsopano mipukutuyo ikusonyeza kuti nthaŵi zambiri kusiyana kotereku kulipo chifukwa cha kusiyanasiyana kwa malemba achihebri. Chimenechi chingakhale chifukwa chimene mwina ndi mwina Akristu oyambirira anagwira mawu Malemba Achihebri koma mogwiritsa ntchito mawu osiyana ndi a m’malemba a Amasorete.​—Eksodo 1:5; Machitidwe 7:14.

Chotero, chuma chimenechi cha mipukutu ndi zidutswa za mabuku a m’Baibulo n’zofunika zedi pofuna kufufuza mmene malemba a m’Baibulo lachihebri akhala akuwakopera. Mipukutu ya ku Nyanja Yakufa yasonyeza kuti Septuagint ndi Pentatuke yachisamariya n’zothandiza pofuna kuyerekeza mawu. Yakhala chiŵiya chowonjezeka chimene otembenuza Baibulo angagwiritse ntchito poona zimene angawongolere m’malemba a Amasorete. M’malo ochuluka ndithu, ikugwirizana ndi zosankha za Komiti Yotembenuza Baibulo la New World Bible Translation pobwezeretsa dzina la Yehova m’malo momwe linachotsedwa m’malemba a Amasorete.

Mipukutu yonena za malamulo ndi zikhulupiriro za anthu a ku Qumran ikusonyeza bwino lomwe kuti panthaŵi ya Yesu sikunali Chiyuda cha  mtundu umodzi wokha. Anthu a ku Qumran anali ndi miyambo yosiyana ndi ya Afarisi ndi Asaduki. Kusiyana kumeneko kuyenera kuti n’kumene kunachititsa kuti anthu a ku Qumran ameneŵa akakhale kwawokha kuchipululu. Molakwa, anali kudziona kuti ndiwo akukwaniritsa Yesaya 40:3 amene amanena za mawu ofuula m’chipululu olungamitsa njira ya Yehova. Zidutswa za mipukutu zingapo zimanena za Mesiya amene olemba ake a mipukutuyo anaona kuti wayandikira. Zimenezi n’zochititsa chidwi chifukwa cha mawu a Luka akuti “anthu anali kuyembekezera” kudza kwa Mesiya.​—Luka 3:15.

M’njira ina, Mipukutu ya ku Nyanja Yakufa ikutithandiza kumvetsa mmene moyo wa Ayuda unalili panthaŵi imene Yesu anali kulalikira. Ingagwiritsidwe ntchito pofufuza Chihebri chakale ndi malemba a m’Baibulo moyerekeza ndi zolembedwa zake. Koma mawu a Mipukutu ya ku Nyanja Yakufa yochuluka n’ngofunikabe kuwapenda. Chotero, pangakhalebe mfundo zinanso zimene zidzadziŵika. Inde, chinthu chofunika kwambiri chimene ofukula za m’mabwinja apeza m’zaka za m’ma 1900 chikupitirizabe kuchititsa chidwi akatswiri ndi ophunzira Baibulo pamene zaka za m’ma 2000 zikupita.

[Mawu a Chithunzi patsamba 7]

Malo ofukulidwa ku Qumran: Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.; cholembedwa: Chilolezo cha Shrine of the Book, Israel Museum, Jerusalem