Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mipukutu ya ku Nyanja Yakufa—Kodi Zoona Zake N’zotani?

Mipukutu ya ku Nyanja Yakufa—Kodi Zoona Zake N’zotani?

 Mipukutu ya ku Nyanja Yakufa​—Kodi Zoona Zake N’zotani?

Zaka zoposa 50 zapitazo, mbusa wina wachibeduwini anaponya mwala m’phanga umene unapangitsa kuti kupezeke chimene ena akuti ndicho chinthu chofunika kwambiri chimene ofufuza za m’mabwinja apeza m’zaka za m’ma 1900. Mbeduwini ameneyo anamva mwalawo kuti waswa mtsuko wadothi. Atapita kukaona, anapeza yoyambirira mwa mipukutu imene yatchedwa kuti Mipukutu ya ku Nyanja Yakufa.

MIPUKUTU imeneyi yakopa chidwi cha anthu ndiponso yakhala phata la kusamvana pakati pa akatswiri ndi pakati pa ofalitsa nkhani zosiyanasiyana. Anthu sakuimvetsa bwino nkhani ya mipukutuyi ndipo ena akuuzidwa zonama. Pali mphekesera yakuti ena akubisa mipukutu ina yofunika, ati chifukwa ili ndi nkhani zimene zingawonongetse kwambiri chikhulupiriro cha Akristu ndi Ayuda omwe. Komano n’chifukwa chiyani mipukutuyi ili yofunika kwenikweni? Pambuyo pa zaka zoposa 50, kodi n’kutheka kudziŵa zoona zake?

Kodi Mipukutu ya ku Nyanja Yakufa N’chiyani?

Mipukutu ya ku Nyanja Yakufa ndizo zolembedwa pamanja zachiyuda zamakedzana, ndipo zochuluka zinalembedwa m’Chihebri, zina m’Chialamu, komanso zochepa m’Chigiriki. Yochuluka ya mipukutuyi ndiponso zidutswa zake zinalembedwa zaka zoposa 2,000 zapitazo, Yesu asanabadwe. Pakati pa mipukutu yoyambirira yomwe anaipeza kwa Abeduwini panali zolembedwa pamanja zazitali zisanu ndi ziŵiri zowonongeka mosiyanasiyana malinga ndi nthaŵi imene zakhala. Pamene anafufuza m’mapanga owonjezeka, anapezamo mipukutu inanso ndi zidutswa za mipukutu zokwanira masauzande ambiri. Pakati pa zaka za 1947 ndi 1956, anapeza mapanga 11 onse pamodzi momwe munali mipukutu pafupi ndi ku Qumran, m’mphepete mwa Nyanja Yakufa.

 Mipukutu yonseyo ndi zidutswa zake akazilongosola bwino, zikupanga zolembedwa pamanja pafupifupi 800. Zopitirira pang’ono 200 ndizo makope a zigawo za Baibulo lachihebri. Zolembedwa pamanja zinanso n’zokhudzana ndi zolembedwa zachiyuda zakale zosakhala za m’Baibulo, za Apocrypha ndi za Pseudepigrapha zomwe.  *

Mipukutu ina imene inachititsa chidwi kwambiri akatswiri inali ya zolembedwa zomwe kale sizinali kudziŵika. Zimenezi zimaphatikizapo nkhani zomasulira mfundo za m’chilamulo cha Ayuda, malamulo a anthu omwe ankakhala ku Qumran, ndakatulo ndi mapemphero ogwiritsa ntchito polambira, pamodzinso ndi nkhani za kutha kwa dziko zosonyeza malingaliro awo ponena za kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Baibulo ndi masiku otsiriza. Palinso zolembedwa zomasulira mabuku a m’Baibulo m’njira yawoyawo, chiyambi chakale zedi cha zolembedwa zamakono zomasulira malemba a m’Baibulo vesi ndi vesi.

Analemba Mipukutu ya ku Nyanja Yakufa Ndani?

Njira zosiyanasiyana zofufuzira nthaŵi pamene mipukutuyo inalembedwa zikusonyeza kuti iyo inakopedwa kapena kulembedwa pakati pa zaka za zana lachitatu B.C.E. ndi zaka za zana loyamba C.E. Akatswiri ena anenapo kuti Ayuda ochokera ku Yerusalemu kachisi asanawonongedwe mu 70 C.E. ndiwo anabisa mipukutuyo m’mapangamo. Koma akatswiri ochuluka openda mipukutuyo akuona kuti lingaliro limeneli silikugwirizana ndi nkhani za m’mipukutuyo. Mipukutu yochuluka ikusonyeza malingaliro ndi miyambo yosiyana kwambiri ndi malingaliro a atsogoleri achipembedzo a ku Yerusalemu. Mipukutu imeneyi ikusonyeza kuti eni ake ankakhulupirira kuti Mulungu anakana ansembe ndi utumiki wa pa kachisi ku Yerusalemu ndi kuti iye anali kuona kulambira kwa gulu lawolo m’chipululu monga koloŵa m’malo mwa utumiki wa pakachisi. N’zokayikitsa kuti akuluakulu a pakachisi a ku Yerusalemu ndiwo akanabisa mtokoma wokhala ndi mipukutu ina yoteroyo.

Ngakhale kuti ku Qumran kuyenera kuti kunali gulu la okopa zolembedwa, zikuoneka kuti mipukutu yambiri inachokera kumalo ena ndipo inabwera ku Qumran ndi okhulupirira. M’njira ina, Mipukutu ya ku Nyanja Yakufa ndi laibulale yaikulu kwambiri. Monga momwe zimakhalira ndi laibulale iliyonse, pangakhale mabuku olongosola mfundo zambiri zosiyanasiyana, ndipo sikuti mabuku onsewo amasonyeza malingaliro achipembedzo a owaŵerenga. Komabe, nkhani zimene zikupezeka kuti zili m’makope ochuluka ziyenera kuti zikusonyeza zomwe gululo linkachita komanso zikhulupiriro zawo.

Kodi Aesene Ndiwo Anali Kukhala ku Qumran?

Ngati mipukutu imeneyi inali laibulale ya ku Qumran, kodi ndani ankakhala kumeneko? Pulofesa Eleazar Sukenik, amene anapeza mipukutu itatu mu 1947, yomwe anakaisungira ku yunivesite yotchedwa Hebrew ku Yerusalemu, ndiye anali woyamba kunena kuti mipukutu imeneyi iyenera kuti inali ya Aesene.

Aesene anali gulu lachiyuda limene Josephus, Philo wa ku Alexandria, ndi Pliny Wamkulu, olemba nkhani a m’zaka za zana loyamba analitchulapo. Sitikudziŵa kuti Aesene anachokera kuti kwenikweni, koma akuoneka kuti anayamba kuonekera panthaŵi yamavuto pambuyo pa kupanduka kwa Amakabe m’zaka za zana lachiŵiri B.C.E. * Josephus anawatchula chapanthaŵi imeneyo polongosola mmene malingaliro awo achipembedzo anasiyanirana ndi a Afarisi ndi Asaduki. Pliny anatchula kumene mudzi wa Aesene unali pafupi ndi Nyanja Yakufa pakati pa Yeriko ndi Engedi.

Pulofesa James VanderKam, katswiri wa Mipukutu ya ku Nyanja Yakufa, akunena kuti mwina “Aesene amene anali kukhala ku Qumran anali mbali yaing’ono chabe ya gulu lalikulu la Aesene,” omwe Josephus anati analipo ngati masauzande anayi. Ngakhale kuti mwina ndi mwina sizikugwirizana kwenikweni, chithunzi chimene zolembedwa za ku  Qumran zikupereka chikuoneka kuti chikugwirizana kwambiri ndi Aesene kusiyana ndi gulu lina lililonse lachiyuda la panthaŵiyo.

Ena anena kuti Chikristu chinayambira ku Qumran. Komabe, pali zinthu zambiri zosiyana kotheratu pakati pa malingaliro achipembedzo a anthu a ku Qumran ndi Akristu oyambirira. Zolembedwa za ku Qumran zikusonyeza kuti anthuwo anali ndi malamulo okhwima zedi a Sabata ndiponso anali okondetsetsa miyambo ya kudziyeretsa. (Mateyu 15:1-20; Luka 6:1-11) N’chimodzimodzinso ndi kudzipatula kwa Aesene kukakhala kwaokha, kukhulupirira kwawo chikonzero cha Mulungu ndi kusafa kwa moyo, ndiponso kugogomeza kwawo umbeta ndi zikhulupiriro zoti amakhala pamodzi ndi angelo polambira. Zimenezi zikusonyeza kuti sanali kutsatira ziphunzitso za Yesu ndi za Akristu oyambirira.​—Mateyu 5:14-16; Yohane 11:23, 24; Akolose 2:18; 1 Timoteo 4:1-3.

Palibe Chinsinsi, Palibe Mipukutu Yobisika

Pazaka zotsatira, Mipukutu ya ku Nyanja Yakufa itapezeka, mabuku osiyanasiyana analembedwa amene analongosola zimene apeza m’mipukutuyo panthaŵiyo kuti akatswiri padziko lonse lapansi aŵerenge. Koma panali mavuto ambiri ndi zidutswa masauzande ambiri za m’phanga lina, lotchedwa Phanga 4. Zimenezi zinali m’manja mwa kagulu kakang’ono ka akatswiri ochokera m’mayiko osiyanasiyana omwe anali kugwirira ntchito yawo kum’mawa kwa mzinda wa Yerusalemu (chigawo chomwe panthaŵiyo chinali m’dziko la Yordano) pa Palestine Archaeological Museum. Pagulu la akatswirili panalibe Myuda kapena Mwisrayeli aliyense.

Gululo silinafune wina aliyense kuona nawo mipukutuyo lisanafalitse zimene linapeza pakufufuza kwakeko. Akatswiriwo sanali kupitirira chiŵerengero chinachake. Wina m’gululo akamwalira, anali kuwonjezerapo katswiri watsopano mmodzi yekha kuti aloŵe m’malo mwake. Ntchito yakeyo inali kufunika akatswiri ochuluka, ndiponso nthaŵi zina, panali kufunikiranso luso lalikulu pa Chihebri ndi Chialamu chakale. James VanderKam anati: “Zidutswa masauzande ambirimbiri zinali zochulukitsitsa moti akatswiri asanu ndi atatu okha sakanatha, ngakhale atakhala aluso chotani.”

Pambuyo pa Nkhondo ya Masiku Asanu ndi Limodzi mu 1967, chigawo cha kum’mawa cha mzinda wa Yerusalemu chinatengedwa ndi dziko la Israyeli, koma mfundo za gulu lija lofufuza mipukutu sizinasinthe. Mmene ena anaona kuti akuchedwa kwambiri kuti afalitse mipukutu ya m’Phanga 4 ija, patadutsa zaka makumi angapo, akatswiri angapo anadandaula. Mu 1977, Pulofesa Geza Vermes wa ku Yunivesite ya Oxford anati m’zaka zonse za m’ma 1900 imeneyo inali nkhani yochititsa manyazi koposa m’nkhani zamaphunziro. Ndiye panabuka mphekesera zonena kuti Tchalitchi cha Katolika chikubisa dala mipukutuyo, kubisa nkhani za m’mipukutuyo zimene zingawonongetse Chikristu.

Pomalizira pake, mu 1980 gululo analikulitsa n’kukhala la akatswiri 20. Kenako, mu 1990, motsogoleredwa ndi mkonzi wake wamkulu watsopano, Emanuel Tov, wa pa Yunivesite ya Hebrew mu Yerusalemu, gululo linawonjezekabe n’kukhala akatswiri oposa 50. Anaika ndandanda yofalitsira mabuku onse a mipukutu yotsalayo.

Chinthu chosaiŵalika chinachitika mosayembekezeka mu 1991. Choyamba buku lakuti A Preliminary Edition of the Unpublished Dead Sea Scrolls (Buku Loyamba la Mipukutu ya ku Nyanja Yakufa Yosafalitsidwa) linafalitsidwa. Limeneli analilemba mwa kugwiritsa ntchito makompyuta ndipo maziko ake anali kope la mpambo wa mawu la akatswiriwo. Kenako, Laibulale ya Huntington ku San Marino, California, inalengeza kuti katswiri aliyense atha kum’patsa zithunzi zawo zonse za mipukutu ija. Posapita nthaŵi, buku lakuti A Facsimile Edition of the Dead Sea Scrolls (Buku la Mipukutu ya ku Nyanja Yakufa) litafalitsidwa, zithunzi za mipukutu yomwe poyamba inali yosafalitsidwa zinayamba kupezeka mosavuta.

Chotero, m’zaka khumi zapitazi, akatswiri akhala omasuka kufufuza Mipukutu yonse ya ku Nyanja Yakufa. Kufufuzako kwasonyeza kuti panalibe chinsinsi chilichonse; panalibe mipukutu yobisika. Pamene mabuku omalizira a mipukutuyo afalitsidwa m’pamene kufufuza kwenikweni kukuyambika tsopano. Kwabadwa mbadwo watsopano wa akatswiri a mipukutu. Koma kodi kufufuza kumeneku kuli ndi tanthauzo lotani kwa ophunzira Baibulo?

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 Zolembedwa za Apocrypha (kutanthauza “zobisika”) ndiponso Pseudepigrapha (kutanthauza “zolembedwa zonamizira kulembedwa ndi anthu ena”) n’zolembedwa zachiyuda zoyambira m’zaka za zana lachitatu B.C.E. mpaka m’zaka za zana loyamba C.E. Tchalitchi cha Roma Katolika chimavomereza zolembedwa za Apocrypha kukhala mbali ya mabuku ouziridwa a m’Baibulo, koma Ayuda ndi Apulotesitanti sawavomereza mabuku ameneŵa. Zolembedwa za Pseudepigrapha nthaŵi zambiri zimakhala ngati kuti zikupitiriza nkhani za m’Baibulo, zolembedwa m’dzina la munthu wina wa m’Baibulo wodziŵika bwino.

^ ndime 13 Onani nkhani yakuti “Kodi Amakabe Anali Ayani?” mu Nsanja ya Olonda ya November 15, 1998, masamba 21-4.

[Chithunzi patsamba 3]

Awa ndi ena mwa mapanga amene anapezamo mipukutu yamakedzana pafupi ndi Nyanja Yakufa

[Mawu a Chithunzi patsamba 3]

Chidutswa cha mpukutu: Masamba 3, 4, ndi 6: Chilolezo cha Israel Antiquities Authority

[Mawu a Chithunzi patsamba 5]

Mwachilolezo cha Shrine of the Book, Israel Museum, Jerusalem