Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Nzeru Ikufuula—Kodi Inuyo Mukuimva?

Nzeru Ikufuula—Kodi Inuyo Mukuimva?

“Nzerutu ikungokhalira kufuula, ndipo kuzindikira kukungokhalira kutulutsa mawu. Imaima pamwamba pa zitunda, m’mbali mwa njira ndi pamphambano za misewu. Imafuula mokweza . . . polowera kuzipata.”MIYAMBO 8:1-3.

NZERU ndi yofunika kwambiri. Popanda kuchita zinthu mwanzeru, munthu angamangokhalira kupalamula. Koma kodi nzeru yeniyeni tingaipeze kuti? Munthu amene analemba buku la Miyambo ankaganizira za nzeru zopanda malire za Mlengi wathu. Ndipotu nzeru zimenezi ndi zoti aliyense angathe kuzidziwa, chifukwa zimapezeka m’buku lapadera kwambiri, lomwe ndi Baibulo. Taganizirani mfundo zotsatirazi.

  • Buku lina linanena kuti: “Baibulo ndi buku lomwe lafalitsidwa komanso kumasuliridwa kambirimbiri m’zinenero zambiri kuposa buku lililonse.” (The World Book Encyclopedia) Baibulo lonse kapena mbali yake likupezeka m’zinenero pafupifupi 2,600. Izi zikusonyeza kuti anthu 90 pa 100 alionse angathe kukhala nalo m’chinenero chawo. Pamenepatu tingati nzeru ikufuula.

  • Koma nzeru ‘imafuula mokweza’ m’njira inanso. Lemba la Mateyu 24:14 limati: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto [a dziko loipali] adzafika.”

Tingati “uthenga wabwino” umenewo ndi nzeru yeniyeni, chifukwa umatiuza za njira yanzeru imene Mulungu wakonza yodzathetsera mavuto a anthu. Mulungu adzagwiritsa ntchito Ufumu wake kuthetsa mavuto onse a anthu. Ufumu umenewu ndi boma lokhazikitsidwa ndi Mulungu, ndipo lidzalamulira dziko lonse lapansi. Izi zikusonyeza kuti padziko lonse padzakhala boma limodzi lokha. (Danieli 2:44; 7:13, 14) N’chifukwa chake Yesu Khristu anapemphera kuti: “Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chimodzimodzinso pansi pano.”—Mateyu 6:9, 10.

A Mboni za Yehova amalengeza za Ufumu wa Mulunguwu m’mayiko okwana 239, ndipo amaona kuti kugwira nawo ntchito imeneyi ndi mwayi waukulu zedi. Apatu tingatidi nzeru yeniyeni yochokera kwa Mulungu ‘ikufuula mokweza.’ Kodi inuyo mukuimva?