KUCHEZA NDI | GUILLERMO PEREZ
Yemwe Anali Dokotala wa Opaleshoni Akufotokoza za Chikhulupiriro Chake
Dr. Guillermo Perez, yemwe anali dokotala wamkulu wa opaleshoni pachipatala china ku South Africa, anapuma pa ntchito yake. Kwa zaka zambiri ankakhulupirira kuti zinthu zamoyo zinakhalako zokha. Koma kenako anayamba kukhulupirira kuti mmene thupi la munthu limagwirira ntchito zimasonyeza kuti linachita kulengedwa ndi Mulungu. Mtolankhani wa Galamukani! anacheza naye kuti adziwe za chikhulupiriro chake.
N’chifukwa chiyani poyamba munkakhulupirira kuti zamoyo zinakhalako zokha?
Ngakhale kuti ndinakulira m’banja lakatolika, ndinkakayikira zinthu zina zomwe ndinamva zokhudza Mulungu. Mwachitsanzo, zinkandivuta kukhulupirira Mulungu chifukwa ndinamva kuti amawotcha anthu kumoto. Choncho nditaphunzira kuyunivesite kuti zamoyo sizinalengedwe ndi Mulungu, koma zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina, ndinayamba kukhulupirira zimenezi poganiza kuti zili ndi umboni. Komanso kutchalitchi kwathu sankatsutsa mfundo yoti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina, kungoti ankati Mulungu ndiye anachititsa zimenezi.
Kodi n’chiyani chinachititsa kuti muyambe kuchita chidwi ndi Baibulo?
Mkazi wanga, Susana, anayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova. Iwo anamusonyeza kuchokera m’Baibulo kuti Mulungu sawotcha anthu oipa kumoto. * Komanso anamusonyeza vesi limene limanena zoti Mulungu walonjeza kuti adzasandutsa dziko lapansili kukhala paradaiso ndipo anthufe tizidzakhala mmenemo mosangalala. * Tinaona kuti mfundo zimenezi n’zomveka kusiyana ndi zimene tinkaphunzira kutchalitchi kwathu zija. Mu 1989, wa Mboni wina dzina lake Nick, anayamba kundiphunzitsa Baibulo. Tsiku lina tikukambirana zokhudza mmene thupi la munthu limagwirira ntchito, ndinadabwa ndi mawu omveka bwino opezeka m’Baibulo palemba la Aheberi 3:4. Vesili limati: “Nyumba iliyonse inamangidwa ndi winawake, koma amene anapanga zinthu zonse ndi Mulungu.”
Kodi zimene munaphunzira zokhudza thupi la munthu zinakuthandizani kuvomereza kuti zinthu zinachita kulengedwa?
Ee. Mmene thupi la munthu limadzichiritsira lokha, zimasonyeza kuti linapangidwa modabwitsa. Mwachitsanzo, munthu akavulala, kuti balalo lipole pamachitika masiteji 4 ndipo siteji iliyonse imayamba, ina isanamalize. Kudziwa zimenezi kunandithandiza kuzindikira kuti thupi lathuli linapangidwa m’njira yoti lizitha kudzichiritsa lokha.
Tifotokozereni bwinobwino zimene zimachitika munthu akavulala
Munthu akavulala, pakangotha masekondi ochepa, siteji yoyamba imayamba. Siteji imeneyi imathandiza kuti magazi asiye kutuluka. Zimene zimachitika ndi zogometsa kwambiri komanso zimachitika mwadongosolo. Timabowo ta mitsempha ta pamalo ovulalawo timachepa ndipo izi n’zimene zimathandiza kuti magazi asiye kutuluka. Komanso ndiwonjezerepo kuti, mmene thupi lathu limagwirira ntchito, tingaziyerekezere ndi pulambala wodziwa bwino ntchito yake. Mitsempha ikaduka, thupi limatha kutseka lokha podukapo kuti magazi asiye kutuluka.
Nanga pa siteji yachiwiri chimachitika n’chiyani?
Pakangotha maola ochepa, magazi amasiya kutuluka ndipo pamalopo pamayamba kutupa. Kuti zimenezi zitheke pamachitika zinthu zingapo zodabwitsa. Choyamba timabowo ta mitsempha tomwe tinachepa kuti magazi asamatuluke tija, timayamba kukula n’cholinga choti magazi ambiri afike pamalo ovulalawo. Kenako thupi limatulutsa timadzi tokhala ndi mapuloteni ndipo iti n’timene timachititsa kuti pamalopo patupe. Timadziti n’tofunika kwambiri chifukwa timathandiza kupha majeremusi pabalapo, kupateteza kuti pasalowe matenda komanso kuchotsa tinyama tomwe tawonongeka. Kuti zonsezi zitheke pamapangika maselo enaake ambirimbiri komanso zinthu zimene zimakhala m’maselo. Zina zimene zimachitika pa siteji imeneyi, ndi zimene zimachititsa kuti siteji yachitatu iyambe, ndipo ikangoyamba siteji yachiwiriyi imathera pompo.
Kodi chimachitika n’chiyani pa siteji yachitatuyi?
Pakatha masiku angapo kuchokera pamene munthu wavulala, thupi limayamba kupoletsa balalo. Chimenechi ndiye chimakhala chiyambi cha siteji yachitatu ndipo zambiri zothandiza kuti bala lipole zimachitika pakatha milungu iwiri. Maselo amene amapanga timaulusi tomwe timakhala ngati masititchi pabalapo, amayamba kuchulukana ndipo amafalikira pabala ponsepo. Komanso timitsempha ting’onoting’ono timatuluka pamalopo n’kuyamba kukula ndipo timathandiza kuchotsa zoipa n’kubweretsa zofunikira. Kenako maselo enaake amapangidwa ndipo maselo amenewa amathandiza kuti povulalapo pagwirane n’kubwerera m’chimake.
Koma ndiyetu pamachitika zambiri. Ndiye pamatenga nthawi yaitali bwanji kuti bala lipoleretu?
Siteji yomalizayi, yomwe ndi imene imathandiza kuti bala lipoleretu, imatenga miyezi yambiri. Ngati munthu wathyoka fupa, pamafunika kuti libwerere m’chimake. Kuti zimenezi zitheke, timaulusi tomwe timakhala ngati masititchi tija timayamba kulimba pang’onopan’gono kenako n’kuthandiza kuti fupa lija likhale mmene linalili poyamba. Zonsezi zimasonyeza kuti mmene thupi lathuli limadzichiritsira lokha munthu akavulala, n’zogometsa kwambiri.
Kodi mungatipatse chitsanzo chomwe chinakuchititsani chidwi kwambiri pa nkhani ya mmene thupi limadzichiritsira lokha?
Ndimagoma kwambiri ndikaganizira mmene thupi limadzichiritsira lokha
Ee. Ndikukumbukira kuti ndinathandizapo mtsikana wina wazaka 16 amene anavulala pa ngozi ya galimoto. Mtsikanayu anavulala kwambiri moti kapamba wake anawonongeka zedi ndipo magazi ankatsikira m’mimba. Likanakhala kale, bwenzi titamuchita opaleshoni kuti tikonze kapena kuchotsa kapambayo. Koma masiku ano madokotala amaona kuti njira yabwino yochizira ndi kulola kuti thupi lidzichize lokha. Choncho ndinangom’patsa mankhwala opha ululu, oteteza ku tizilombo toyambitsa matenda komanso othandiza kubwezeretsa madzi ndi magazi amene anataya. Patatha milungu ingapo, tinamujambula ndipo tinapeza kuti kapamba wake uja ali bwino. Ndimagoma kwambiri ndikaganizira mmene thupi limadzichiritsira lokha. Ndipo zimenezi zimandichititsa kukhulupirira kwambiri kuti anthufe tinalengedwa ndi Mulungu.
N’chiyani chinakuchititsani chidwi kuti mukopeke ndi a Mboni za Yehova?
Ndinaona kuti a Mboni ndi anthu ansangala komanso ankayankha mafunso anga onse pogwiritsa ntchito Baibulo. Ndinachitanso chidwi kuona kuti amauza anthu ena zomwe amakhulupirira molimba mtima komanso amathandiza ena kudziwa zoona zokhudza Mulungu.
Kodi kukhala wa Mboni za Yehova kunakuthandizani pa ntchito yanu monga dokotala?
Ee. Nthawi zambiri pa ntchito yathu timathandiza anthu odwalika kapena ovulala kwambiri. Zimenezi zimachititsa kuti uyambe kuvutika maganizo chifukwa nthawi zonse umaona anthu omvetsa chisoni. Choncho ndimaona kuti kukhala wa Mboni za Yehova kunandithandiza kuti ndisamavutike maganizo kwambiri chifukwa cha zimenezi. Komanso ngati wodwala angakonde, ndinkamuuza za zimene Mlengi walonjeza zoti posachedwa adzathetsa matenda ndi mavuto onse, * adzabwezeretsa dzikoli kukhala paradaiso ndiponso palibe aliyense amene adzanene kuti, “ndikudwala.” *