GALAMUKANI! November 2013 | Makhalidwe Abwino Angakuthandizeni Kuti Muzisangalala
Mfundo zimene timayendera zimakhudza zinthu zimene timaona kuti ndi zofunika kwambiri, mmene timachitira zinthu ndi anthu ena komanso malangizo amene timapereka kwa ana athu. Werengani magaziniyi kuti muone mfundo za makhalidwe abwino zimene zingatithandize kuti tizisangalala.
Zochitika Padzikoli
Nkhani zake ndi monga: Msonkho wa tchalitchi ku Germany, zimene ubongo umachita munthu akayamikiridwa, komanso kuchuluka kwa anthu amene “sali m’chipembedzo chilichonse.”
MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA
Kukambirana ndi Mwana Wanu Nkhani Yotumizirana Zinthu Zolaula Pafoni
Musachite kudikira kuti mpaka mwana wanu akumane ndi vuto linalake chifukwa chakuti sanagwiritse ntchito bwino foni yake. Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zimene mungachite kuti mukambirane ndi mwana wanu kuopsa kotumizirana zinthu zolaula.
NKHANI YAPACHIKUTO
Makhalidwe Abwino Angakuthandizeni Kuti Muzisangalala
Anthu ambiri amayendera mfundo yoti: ‘Palibe vuto ndi kuchita chilichonse chomwe mtima wako ukufuna, bola ngati iweyo ukuona kuti n’choyenera.’ Koma kodi ndi nzeru kutsatira mfundo imeneyi? Werengani nkhaniyi kuti muone makhalidwe ena a m’Baibulo amene angakuthandizeni.
KUCHEZA NDI ANTHU
Katswiri Woimba Piyano Akufotokoza za Chikhulupiriro Chake
Nyimbo ndi zimene zinathandiza munthu ameneyu, yemwe poyamba sankakhulupirira Mulungu, kuti akhulupirire zoti kuli Mlengi. Kodi n’chiyani chinamuthandiza kukhulupirira kuti Baibulo n’lochokera kwa Mulungu?
Kupirira Mavuto Amene Azimayi Amakumana Nawo Akamasiya Kusamba
Ngati inuyo komanso mwamuna wanu mutamvetsa zimene zimachitika munthu akamasiya kusamba, mudzatha kupirira mosavuta mavuto omwe amachitika.
ZIMENE BAIBULO LIMANENA
Banja
Werengani nkhaniyi kuti muone mmene kutsatira maudindo amene Mulungu anapereka kwa mwamuna ndi mkazi kungathandizire anthu apabanja kuti azisangalala.
Kodi Mumachita “Phwando Nthawi Zonse”?
Werengani nkhaniyi kuti muone zimene zingakuthandizeni kukhala wosangalala pamene mukukumana ndi mavuto.
Zina zimene zili pawebusaiti
Kodi Ndimangokhalira Kuganizira za Maonekedwe Anga?
Kodi mungatani kuti muzisangalala ndi mmene mumaonekera?
Kodi Ndingatani Ngati Ndikudwala Matenda Aakulu?—Gawo 1
Achinyamata 4 akufotokoza zimene zikuwathandiza kupirira matenda awo kuti asamangokhalira kudandaula.
N’chifukwa Chiyani Ndimadzivulaza?
Achinyamata ena ali ndi vuto lodzivulaza mwadala. Ngati muli ndi khalidwe limeneli, kodi mungatani kuti mulisiye?
Yosefe Anapulumutsa Anthu Ambiri
Koperani nkhaniyi kuti muwerenge zokhudza Yosefe, amene Mulungu anamugwiritsira ntchito kupulumutsa mtundu wonse.