Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Germany

M’chaka cha 2012 khoti lina lalikulu ku Germany linagamula kuti anthu a m’dzikolo saziloledwa kumachita zinthu zina ndi tchalitchi chawo chakale ngati analengeza kuti asiya tchalitchicho. Matchalitchi ambiri a m’dzikolo amalandira msonkho kuchokera kwa mamembala ake. Chifukwa cha zimene khoti linagamulazi, anthu omwe ananena kuti asiya tchalitchi cha Katolika ndipo anasiya kupereka msonkho, koma amachitabe zinthu ngati Akatolika, saziloledwa kuchita nawo mwambo wokumbukira imfa ya Yesu kapena mwambo wolapa machimo. Anthu amenewa sangapatsidwenso udindo uliwonse m’boma, mwinanso maliro awo sangayendetsedwe ndi mpingo.

Dziko Lonse

Kafukufuku yemwe anachitika pa zipembedzo za padziko lonse wasonyeza kuti anthu amene amanena kuti “sali m’chipembedzo chilichonse,” alipo 1.1 biliyoni. Anapezanso kuti anthu amene amati ndi Akhristu alipo 2.2 biliyoni, Asilamu alipo 1.6 biliyoni. Ndipo Ahindu alipo 1 biliyoni.

Japan

Asayansi a ku Japan apeza kuti “munthu akayamikiridwa, mbali ya ubongo imene imapangitsa kuti munthu azisangalala imayamba kugwira ntchito.” Zimene apezazi zikugwirizana ndi zomwe anthu amanena zoti kuyamikira ndi njira yabwino yomulimbikitsira munthu pa zimene akuchita.

Bolivia

Kumapeto kwa chaka cha 2012 boma la Bolivia linapanga kalembera wa dziko lonse. Kuti kalembelayu akhale wolondola, boma linalamula kuti aliyense asachoke pakhomo pa tsiku la kalembelayo. Linalamulanso kuti magalimoto a anthu wamba asayende, aliyense asatuluke kapena kulowa m’dzikolo komanso kuti aliyense asamwe mowa pa tsikulo.

Italy

Pa kafukufuku wina amene anachitika ku Italy, anapeza kuti anthu a m’dzikolo amasewera ndi ana awo kwa mphindi pafupifupi 15 tsiku lililonse. Magazini ina inati: “Munthu mmodzi mwa anthu 5 aliwonse, amaona kuti kusewera ndi ana kumathandiza anawo kuti aphunzire zinthu.” (La Repubblica) Munthu wina wopanga zoseweretsa ana, dzina lake Andrea Angiolino, ananena kuti makolo akamasewera ndi ana awo, anawo amayamba kuganiza bwino komanso amaphunzira “kumvera malamulo.”