GALAMUKANI! September 2013 | Kodi Halowini Ndi Chiyani?

Anthu ambiri amachita mwambo wa Halowini ngakhale kuti sadziwa mmene unayambira. Werengani nkhani kuti mudziwe kuopsa kochita nawo zikondwerero zomwe simukudziwa mmene zinayambira.

Zochitika Padzikoli

Muli nkhani monga izi: Madzi oundana a ku Arctic akusungunuka, anthu akupha njovu ku Congo kuti apeze minyanga yake, zinthu zambiri zikufa m’madzi pamalo otchedwa Great Barrier Reef komanso mabakiteliya omwe apezeka mu mkaka wa m’mawere.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Kugonana Musanakwatirane

Werenga nkhaniyi kuti mudziwe zimene Baibulo limanena zokhudza anthu amene amagonana kapena amene amachita zinthu zina zokhudza kugonana asanakwatirane.

NKHANI YAPACHIKUTO

Kodi Halowini N’chiyani?

Werengani nkhaniyi kuti mudziwe mmene mwambo wa Halowini komanso miyambo ina inayambira.

MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA

Kodi Mungatani Kuti Muzikhululukirana?

N’chifukwa chiyani kukhululukirana sikophweka? Werengani nkhani kuti muone mmene Baibulo lingakuthandizireni.

KUCHEZA NDI ANTHU

Katswiri wa Impso Akufotokoza za Chikhulupiriro Chake

N’chiyani chinachititsa dokotala wina, yemwenso sankakhulupirira kuti kuli Mulungu, kuyamba kuganizira za Mulungu komanso cholinga cha moyo? N’chiyani chinamuthandiza kusintha maganizo?

TIONE ZAKALE

Zheng He

Kodi Zheng He anali ndani? Werengani nkhaniyi kuti mudziwe za maulendo ake komanso mmene maulendowa anathandizira anthu a m’mayiko ena kudziwa zambiri za dziko la China.

KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Nthenga za Mbalame Zochititsa Chidwi Kwambiri

Kodi akatswiri ofufuza nyama za m’madzi apeza zotani zokhudza nthenga za mbalame zimenezi?

Zina zimene zili pawebusaiti

Kodi Ndizitani Ngati Ena Akundichitira Zachipongwe?

Werengani nkhaniyi kuti mudziwe tanthauzo la kuchitiridwa zachipongwe komanso zimene mungachite ngati mutachitiridwa zachipongwezo.

Kodi Ndiyenera Kudziwa Zotani Zokhudza Mameseji a Pafoni?

Mameseji a pafoni akhoza kuononga ubwenzi wanu ndi anzanu komanso mbiri yanu. Werengani kuti mudziwe mmene zimenezi zingachitikire

Kodi Ndingatani Ngati Ndikudwala Matenda Aakulu?​—Gawo 1

Achinyamata 4 akufotokoza zimene zikuwathandiza kupirira matenda awo kuti asamangokhalira kudandaula.

Kodi Mungatani Kuti Anzanu Asiye Kukuvutitsani?

Onerani vidiyoyi kuti mudziwe chifukwa chake anthu amavutitsa anzawo komanso zimene mungachite kuti asiye kukuvutitsani.

Yosefe Ali ku Iguputo

Kodi mungasangalatse bwanji Mulungu ngakhale pamene anthu ena sakuona? Werengani nkhani ya m’Baibuloyi kuti muone chitsanzo cha Yosefe.