Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Nthenga za Mbalame Zochititsa Chidwi Kwambiri

Nthenga za Mbalame Zochititsa Chidwi Kwambiri

KUMADERA ozizira kuli mbalame zina zomwe zimathamanga kwambiri. Mbalamezi zimasambira mothamanga ndipo zimadumpha kuchokera m’madzi kukaima pa madzi oundana. Kodi mbalamezi zimatha bwanji kuchita zimenezi?

Nthenga za mbalame zochititsa chidwi

Taganizirani izi: Nthenga za mbalamezi zimasunga mpweya zomwe zimathandiza kuti mbalamezi zisamazizidwe komanso kuti zizisambira mofulumira kwambiri. Akatswiri ofufuza nyama za m’madzi amanena kuti mpweya wa mu nthengazi ukamatuluka umathandiza kuti thupi lonse la mbalameyo lisamavutike kuyenda m’madzi ndipo zimenezi zimathandiza kuti izisambira mofulumira kwambiri.

Akatswiri opanga sitima za m’madzi akhala akuphunzira za mbalameyi n’cholinga choti apange sitima yoti izitulutsa mpweya kuti izithamanga kwambiri. Komabe akuona kuti kuchita zimenezi kungakhale kovuta chifukwa “n’zosatheka kupanga nthenga zofanana ndi za mbalameyi.”

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti mbalamezi zikhale ndi nthenga zodabwitsa chonchi?