Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Kugonana Musanakwatirane

Kugonana Musanakwatirane

Kodi n’kulakwa kugonana musanakwatirane?

“Mulungu akufuna kuti  . . . [muzipewa] dama.”—1 Atesalonika 4:3.

ZIMENE ANTHU AMANENA

M’zikhalidwe zina anthu amaloledwa kugonana asanakwatirane bola ngati agwirizana. M’mayiko ena, anthu amaona kuti n’zosalakwika kuti achinyamata osakwatirana azigonana kapena kusonyezana chikondi m’njira yolakwika.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Baibulo limagwiritsa ntchito mawu oti “dama,” likamanena za kugonana kwa anthu omwe ndi osakwatirana. Mulungu amafuna kuti anthu amene amamulambira ‘azipewa dama.’ (1 Atesalonika 4:3) Dama lili m’gulu la machimo akuluakulu monga chigololo, kukhulupirira mizimu, uchidakwa, kulambira mafano, kupha komanso kuba.—1 Akorinto 6:9, 10; Chivumbulutso 21:8.

N’CHIFUKWA CHIYANI MUYENERA KUDZIWA ZIMENEZI?

Chifukwa chimodzi n’chakuti Baibulo limatichenjeza kuti, “Mulungu adzaweruza adama.” (Aheberi 13:4) Koma chofunika kwambiri n’chakuti tikamamvera lamulo la Mulungu loti tizipewa dama, timasonyeza kuti timakonda Yehova Mulungu. (1 Yohane 5:3) Ndipo iye amadalitsa anthu amene amamvera malamulo ake.—Yesaya 48:18.

 Kodi n’kulakwa kuti anthu osakwatirana azisonyezana chikondi m’njira yolakwika?

“Dama ndi chonyansa chamtundu uliwonse kapena umbombo zisatchulidwe n’komwe pakati panu.”—Aefeso 5:3.

ZIMENE ANTHU AMANENA

Anthu ambiri amaona kuti ngati anthu awiri osakwatirana sakugonana, palibe vuto lililonse ngati atamasonyezana chikondi m’njira ina iliyonse.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Ponena za makhalidwe oipa okhudza kugonana, Baibulo silimangonena za dama lokha, koma limatchulanso za “zonyansa” komanso ‘khalidwe lotayirira.’ (2 Akorinto 12:21) Zimenezi zikusonyeza kuti, ngakhale anthu asagonane, pali njira zambirimbiri zosonyezerana chikondi zimene Mulungu amadana nazo ngati zachitidwa ndi anthu amene sanakwatirane.

Mfundo yaikulu ya m’Baibulo pa nkhaniyi ndi yoti anthu okwatirana okha ndi amene ali ndi ufulu wogonana. Baibulo limasonyezanso kuti kukhala ndi “chilakolako chosalamulirika cha kugonana” n’kosayenera. (1 Atesalonika 4:5) Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Taganizirani chitsanzo ichi: Mkazi wasankha kuti asagonane ndi chibwenzi chake mpaka adzakwatirane. Komabe amasonyezana chikondi m’njira yolakwika ndi chibwenzi chakecho. Zimenezi zingasonyeze kuti onsewo akulakalaka kapena akufunitsitsa zinthu zimene si zawo. Choncho, tinganene kuti ali ndi “chilakolako chosalamulirika cha kugonana” ndipo Baibulo limaletsa khalidwe limeneli.—Aefeso 5:3-5.

Kodi mungapewe bwanji dama?

“Thawani dama.”1 Akorinto 6:18.

ZIMENE MUYENERA KUDZIWA

Baibulo limasonyeza kuti amene amagonana asanakwatirane amasokoneza ubwenzi wawo ndi Mulungu.—Akolose 3:5, 6.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Baibulo limatichenjeza kuti: “Thawani dama.” (1 Akorinto 6:18) Mawu amenewa akutanthauza kuti munthu ayenera kuyesetsa kupewa chilichonse chomwe chingamukope kuti achite dama. (Miyambo 22:3) Mwachitsanzo, kuti munthu asachite dama ayenera kupewa kucheza ndi anthu amene satsatira malamulo a Mulungu pa nkhani ya kugonana. N’chifukwa chake Baibulo limati: “Munthu woyenda ndi anthu anzeru adzakhala wanzeru, koma wochita zinthu ndi anthu opusa adzapeza mavuto.”—Miyambo 13:20.

Kuganizira kwambiri zinthu zolakwika kungapangitsenso kuti munthu achite dama. (Aroma 8:5, 6) Choncho, ndi bwino kupewa nyimbo, mafilimu, mabuku, magazini kapena china chilichonse chimene chimalimbikitsa dama, chifukwa Mulungu amadana nalo.—Salimo 101:3.