GALAMUKANI! April 2013 | N’zotheka Kuthetsa Nkhanza za M’banja

Baibulo lathandiza anthu ena kusiya khalidwe lachiwawa n’kukhala anthu achifundo komanso aulemu.

Zochitika Padzikoli

Nkhani zake ndi monga: Munthu woyamba kuikidwa chibwano chachitsulo ndi zomera za ku Antarctica zikhoza kutheratu.

MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA

Kodi Mungapewe Bwanji Kulankhula Mawu Achipongwe?

Kodi mungatani ngati banja lanu lasokonekera chifukwa choti inuyo ndi mkazi kapena mwamuna wanu mumakonda kulankhulana mawu achipongwe?

KUCHEZA NDI ANTHU

“Sindimakayikiranso Zoti Mulungu Analenga Zamoyo”

Werengani nkhaniyi kuti mudziwe chifukwa chake wasayansi wina anasintha maganizo pa nkhani yoti asintha maganizo ake pa nkhani yoti zamoyo zinachita kusanduka, zinthu zonse zinachita kulengedwa komanso pa nkhani ya Baibulo.

NKHANI YAPACHIKUTO

N’zotheka Kuthetsa Nkhanza za M’banja

Kodi malangizo a m’Baibulo angathandize bwanji mwamuna ndi mkazi kuti asiye khalidwe la nkhanza?

ANTHU NDI MAYIKO

Dziko la Indonesia

Werengani kuti mudziwe za chikhalidwe ndi miyambo ya anthu ochezeka, oleza mtima komanso okonda kuchereza alendo.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Thanzi Lathu

Werengani kuti mudziwe zimene limanena pa nkhani ya matenda komanso chithandizo cha mankhwala.

Mukhoza Kulowa pa Webusaiti Yathu Mosavuta

Kachidindo ka QR kokhala ndi manambala osaoneka kayamba kupezeka m’magazini ya Galamukani! kuti muzitha kulowa pa webusaiti yathu mosavuta komanso mofulumira.

Zina zimene zili pawebusaiti

Kodi Ndingatani Anthu Ena Akamandivutitsa?

Anthu ambiri amene akuvutitsidwa amaona kuti palibe chimene angachite. Nkhaniyi ikufotokoza zimene mungachite kuti anthu asiye kukuvutitsani.

Yakobo, Esau, ndi Mphodza

Dziwani za Yakobo ndi Esau. Koperani chithunzichi, sindikizani, kenako chichekenireni.