Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

United States

Mkati mwa mlungu woyambira October 29, 2012, zinthu monga kuphana ndi zachiwawa zinachepa kwambiri mumzinda wa New York City, poyerekezera ndi mmene zinalili m’chaka cha 2011 nthawi ngati yomweyi. Chimene chinachititsa zimenezi ndi mphepo ya mkuntho yotchedwa Hurricane Sandy yomwe inawononga kwambiri madera a m’mphepete mwa nyanja kum’mawa kwa United States. Mphepo yamkunthoyi inachititsa kuti m’madera amenewa kukhale kopanda magetsi. Mneneri wapolisi mumzinda wa New York, dzina lake Paul Browne, ananena kuti: “Nthawi zambiri kukachitika ngozi zachilengedwe kapena zinthu zoopsa [zangati zimene zinachitika pa September 11, 2001], kuphana komanso zachiwawa zimachepa kwambiri.” Komabe umbava unachuluka kwambiri chifukwa chakuti anthu ankapita kukaba zinthu m’nyumba ndi m’mashopu. A Browne ananena kuti: “Zimenezi n’zosadabwitsa chifukwa nthawi ngati imeneyi kumakhala mdima.”

Antarctica

Asayansi akuda nkhawa kuti zomera za ku Antarctica zikhoza kutha n’kulowedwa m’malo ndi zomera zina zochokera m’madera ena. Akukhulupirira kuti alendo ambiri amene amabwera m’derali amabweretsa njere za zomerazi mosadziwa. Njerezi zimakhala zitamatirira ku nsapato kapena zikwama zawo. Panopa akuti m’chigawo chakumadzulo kwa derali kwayamba kupezeka zomera zamitundu yosiyanasiyana zochokera m’madera ena.

Netherlands

Gogo wina wazaka 83 wakhala munthu woyamba kuikidwa chibwano chachitsulo chomwe anachipanga pogwiritsa ntchito makina otchedwa 3-D laser printer. Gogoyu anali ndi matenda a m’mafupa koma panopa anachira moti amatha kudya, kupuma komanso kulankhula bwinobwino. Popanga chibwanocho, makina amenewa anasakaniza tizitsulo tosiyanasiyana n’kutisanjikizasanjikiza mpaka kupanga chibwano. Kenako madokotala anapanga opaleshoni yomuikirira gogoyo chibwanocho.

Germany

Patangotha chaka chimodzi boma la Germany litaletsa kusuta fodya m’malo ena omwe mumapezeka anthu ambiri, chiwerengero cha anthu amene amagonekedwa m’chipatala chifukwa cha kumva kupweteka pachifuwa, chatsika ndi 13.3 peresenti, pomwe chiwerengero cha anthu odwala matenda a mtima chatsika ndi 8.6 peresenti.