Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kugwirizanitsa Sayansi ndi Chipembedzo

Kugwirizanitsa Sayansi ndi Chipembedzo

Kugwirizanitsa Sayansi ndi Chipembedzo

“Zomaona kuti sayansi ndi chipembedzo ndi zinthu zosagwirizana zinatha tsopano.”Inatero nyuzipepala ya The Daily Telegraph, ya ku London, pa May 26, 1999.

NJIRA zothandiza kwambiri zokhudza sayansi ndiponso chipembedzo zimakhala ndi cholinga chofuna kupeza zoona. Sayansi inatulukira kuti dzikoli lili ndi dongosolo lodabwitsa, kuti chilengedwechi chimasonyezadi kuti panagona nzeru zakuya kuti chikhale mmene chililimu. Chipembedzo choona chimathandiza anthu kumvetsetsa zimene asayansiŵa atulukira pophunzitsa anthu kuti nzeru za Mlengi n’zimene zinatheketsa kuti pakhale zonsezi zimene timaona m’dzikoli.

“Ine ndimaona kuti ndimamvetsetsa kwambiri sayansi chifukwa chopembedza,” anatero Francis Collins, wasayansi ya tizilombo tosaoneka ndi maso. Iye anapitiriza kunena kuti: “Ndikatulukira chinachake chokhudza maselo achibadwa cha anthu, ndimagwidwa nthumanzi ndikaganizira za chinsinsi cha moyo, ndipo chamumtima ndimangoti, ‘Shaa, Mulungu yekha ndiye ankadziŵa zimenezi.’ N’zosangalatsa kwambiri komanso thupi lonseli limangothawathawa, ndipo zimenezi zimandithandiza kulemekeza Mulungu ndiponso kuti sayansi izindikhutiritsa kwambiri.”

Kodi n’chiyani chimene chingathandize munthu kuti agwirizanitse sayansi ndi chipembedzo?

Kufufuza Kosatha

Dziŵani kuti pali malire: Sizikudziŵika n’komwe ngati m’tsogolo muno tidzadziŵe mayankho onse a mafunso ozunguza okhudza za chilengedwe chathu chachikulu mopanda malire, za mlengalenga, ndiponso za nthaŵi. Wasayansi wina yoona zamoyo Lewis Thomas ananena kuti: “Kufufuza kumeneku sikudzatha chifukwa chakuti anthufe timakhala ndi mafunso ambirimbiri pa zinthu, timakonda kufufuza, kuunguzaunguza ndiponso kuyesa kuonaona kuti tidziŵe zinthu. Siidzafika nthaŵi yomwe tidzanene kuti nkhani imeneyi taimvetsadi. Sindikukhulupirira kuti panthaŵi inayake aliyense adzafika ponena kuti, ‘Ayi tsopano ndachimvetsa bwinobwino chilengedwe chonse.’ Sitidzachimvetsa mpaka kalekale.”

Nkhani ya choonadi cha chipembedzonso n’chimodzimodzi, sitifika poti zinthu zonse tazidziŵa bwinobwino. Wolemba Baibulo wina dzina lake Paulo ananena kuti: “Zimene tiona tsopano, timaziona ngati zithunzi chabe m’galasi, zosaoneka bwino kwenikweni . . . Tsopano ndimangodziŵa mopereŵera.”—1 Akorinto 13:12, Chipangano Chatsopano.

Komabe kudziŵa mopereŵera chabe mafunso okhudza sayansi ndi chipembedzo, sikuti kumatilepheretsa kuona zimene zili zoona malinga ndi mfundo zimene tikudziŵa. Sitifunikira kudziŵa mwatsatanetsatane zonse zokhudza dzuŵa kuti tisakayike mpang’ono pomwe kuti maŵa lidzatuluka.

Ganizirani mfundo zodziŵika bwino: Pofunafuna kumvetsa zinthu, tiyenera kutsata mfundo zomveka bwino. Tikamafufuza choonadi cha sayansi ndiponso chipembedzo m’posavuta kusocheretsedwa tikapanda kutsata umboni umene uli wotsimikizika kwambiri. Kunena zoona, palibe munthu amene angalimbane n’kuti afufuze zonse zimene asayansi apeza zimene zili m’mabuku asayansi amene amadzaza nyumba zikuluzikulu zosungirako mabuku. Koma Baibulo n’losavuta kufufuzamo ziphunzitso zauzimu zoyenera kuti tiziganizire. Baibulo ndi buku limene maumboni odziŵika bwino amatsimikizira kuti limanena zoona. *

Komabe, tikafuna kungodziŵa bwino zinthu zokhudza sayansi ndiponso chipembedzo, m’pofunika khama kwambiri kuti tithe kusiyanitsa zoona ndi zongoganizira, zochitikadi ndi zonama. Wolemba Baibulo, Paulo analangiza kuti, tiyenera kulewa “zokamba zopanda pake ndi zotsutsana za ichi chitchedwa chizindikiritso konama.” (1 Timoteo 6:20) Pofuna kugwirizanitsa sayansi ndi Baibulo, tiyenera kuganizira mfundo zenizeni n’kupeŵa mfundo zosatsimikizika ndi zongoganizira, ndipo tiyeneranso kuganizira kugwirizana kwa mfundozo.

Mwachitsanzo, pakuti timadziŵa kuti Baibulo likamanena kuti “tsiku” limatanthauza nthaŵi yaitali mosiyanasiyana, timaona kuti nkhani yakuti Mulungu analenga zinthu kwa masiku asanu ndi limodzi m’buku la Genesis siitsutsana ndi zimene asayansi anapeza zakuti dzikoli lakhalapo kwa zaka pafupifupi mabiliyoni anayi ndi theka. Baibulo limati Mulungu asanayambe kulenga zinthu zina, dzikoli n’kuti litakhalapo kale kwa nthaŵi inayake imene Baibulo silinatchule. (Onani bokosi lakuti “Kodi Masiku Amene Mulungu Analenga Zinthu Anali a Maola 24 Tsiku Lililonse?”) Ngakhale asayansi ataona kuti analakwitsa n’kutchula zaka zina pankhani ya kulengedwa kwa dziko lathuli, zimene Baibulo linanena n’zoona basi. Pankhani imeneyi, ndiponso pankhani zina zosiyanasiyana, m’malo motsutsana ndi Baibulo kwenikweni sayansi imatidziŵitsa zambiri zofunika kudziŵa zokhudza mmene dziko lathuli lilili panopo komanso mmene linalili m’mbuyomo.

Chikhulupiriro, osati kutengeka maganizo: Baibulo limatidziŵitsa za Mulungu ndiponso cholinga chake zimene sitingathe kuzidziŵa kuchokera m’buku lina lililonse. Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kulikhulupirira? Baibulolo limatiuza kuti tilione tokha ngati limanenadi zinthu molondola. Onani ngati limanena zoona pankhani ya zochitika za m’mbiri, ngati limanenadi zinthu zothandiza, ngati olemba ake anali anthu onena zinthu mwachilungamo, komanso ngati limaphunzitsadi zoona. Pofufuza m’Baibulo n’kuona kuti limalondola ngakhale pamene likusimba za sayansi ndiponso makamaka pa maulosi ake ambirimbiri amene akhala akukwaniritsidwa m’mbuyo monsemu mpaka m’nthaŵi yathu ino, munthu angathe kukhala ndi chikhulupiriro cholimba chakuti n’zoonadi Baibulo ndi Mawu a Mulungu. Kukhulupirira Baibulo si kutengeka maganizo koma ndi kukhulupirira poona umboni wakuti mawu amene ali m’Malemba n’ngolondola.

Musainyoze sayansi; komanso onani kuti chikhulupiriro n’chofunika: Mboni za Yehova zimapempha anthu asayansi ndiponso achipembedzo, amene amatha kumvetsera maganizo a ena, kuti zikambirane nawo mwanjira yoona mtima pofufuzira pamodzi choonadi kuchokera mu sayansi ndiponso chipembedzo. M’mipingo yawo Mboni zimathandiza anthu kuona bwinobwino kufunika kwa sayansi ndi zinthu zotsimikizika zimene yatulukira komanso kuona kufunika kwa chikhulupiriro chimene chimapezeka m’Baibulo mokha, buku limene limanena mosapita m’mbali n’kuperekanso umboni wambirimbiri kuti ilo ndilo Mawu a Mulungu. Mtumwi Paulo ananena kuti: “Pamene munalandira mawu a Mulungu, amene munamva kwa ife, munawalandira, osati monga mawu a anthu, koma, monga momwe alili ndithu, mawu a Mulungu.”—1 Atesalonika 2:13, NW.

N’zoonadi kuti monganso zilili ndi sayansi, mabodza ndiponso zochita zina zoipa zaloŵanso m’chipembedzo. Motero, pali chipembedzo choona ndiponso chipembedzo chabodza. N’chifukwa chake anthu ambiri asiya zipembedzo zotchuka, n’kuloŵa mumpingo wachikristu wa Mboni za Yehova. Akhumudwa poona kuti zipembedzo zawo zakale sizikufuna kusiya miyambo ya anthu ndiponso zikhulupiriro zachabechabe n’kutsatira choonadi chimene ena atulukira kapena chimene chavumbulidwa.

Kuphatikizanso pamenepo, Akristu oona amaona kuti moyo n’ngofunikadi, chifukwa chakuti anam’dziŵa kwambiri Mlengi, monga mmene am’tchulira m’Baibulo, komanso zimene ananena kuti adzachitira anthu ndiponso dziko lathu limene tikukhalamoli. Mboni za Yehova zimakhutira ndi mayankho ochokera m’Baibulo a mafunso monga akuti, Kodi n’chifukwa chiyani ife tilipo? Kodi tikuloŵera kuti? Zingakhale zosangalala kwambiri kukambirana nanu nkhani zimenezi.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 10 Onani buku lakuti Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Bokosi patsamba 10]

Kodi Masiku Amene Mulungu Analenga Zinthu Anali a Maola 24 Tsiku Lililonse?

Anthu ena amene amakhulupirira kuti zinthu zonse zolembedwa m’Baibulo n’zenizeni osati kuti zina n’zongophiphiritsira amanena kuti anthu asanakhaleko zamoyo zonse zimene zinalipo zinachita kulengedwa osati kuti zinachita kusanduka kuchokera kuzinthu zinazake. Iwo amanena motsindika kuti chilengedwe chonsechi chinalengedwa m’masiku asanu ndi limodzi, tsiku lililonse lokhala ndi maola 24 ndipo kuti izi zinachitika m’zaka 6,000 kapena 10,000 zapitazo. Koma potero, iwo amalimbikitsa chiphunzitso chosapezeka m’malemba chimene chapangitsa anthu ambiri kunyoza Baibulo.

Kodi mawu akuti tsiku m’Baibulo nthaŵi zonse amakamba za tsiku lenileni la maola 24? Lemba la Genesis 2:4 limanena za “tsiku lomwe Yehova Mulungu anapanga dziko lapansi ndi zakumwamba.” Tsiku limodzi limeneli limaimira masiku onse asanu ndi limodzi amene Mulungu analenga zinthu zotchulidwa mu Genesis chaputala 1. Baibulo likatchula mawu akuti tsiku limatanthauza nthaŵi, ndipo ingathe kukhala nthaŵi ya zaka 1000 kapena zaka zambirimbiri kuposa pamenepo. N’kutheka kunena kuti tsiku lililonse limene Baibulo limati Mulungu analenga zinthu linali la zaka masauzande ambirimbiri. Chinanso n’chakuti dzikoli linalipo kale Mulungu asanayambe kulenga zinthu m’masiku ameneŵa. (Genesis 1:1) Motero pamfundo imeneyi, zimene Baibulo limanena n’zogwirizana ndi zimene sayansi yoona imanena.—2 Petro 3:8.

Pothirira ndemanga nkhambakamwa yakuti masiku amene Mulungu analenga zinthu anali a maola 24, katswiri wina wasayansi ya tinthu tosaoneka ndi maso topezeka m’zamoyo, Francis Collins anati: “Chiphunzitso chimenechi chawonongetsa chikhulupiriro cha anthu ambiri kuposa chinthu china chilichonse m’nthaŵi yathu ino.”

[Bokosi patsamba 11]

Kodi Sayansi Yalanda Malo a Khalidwe Labwino?

Mpake kuti anthu ambiri okhulupirira sayansi anasiya kupembedza chifukwa chipembedzo chakhala chikulepheretsa sayansi kuti iyende bwino ndiponso chili ndi mbiri yoipa, n’chachinyengo komanso n’chankhanza. Pulofesa wina wa sayansi ya tizilombo tosaoneka ndi maso, John Postgate ananena kuti: “Zipembedzo za padzikoli . . . zabweretsa zinthu zoopsa monga kupereka nsembe anthu, kumenyana kwa Akristu ndi Asilamu, kupha anthu ambiri pazifukwa zosankhana mtundu kapena za kusiyana chipembedzo chawo ndiponso kuchita nkhanza zoopsa pofuna kutembenuza anthu. Masiku ano khalidwe loipa lachipembedzo limeneli lafika poopsa kwambiri. Chifukwa chakuti mosiyana ndi sayansi chipembedzo sichikulola kuti munthu ukhale wopanda mbali iliyonse.”

Poyerekeza khalidwe limeneli ndi zinthu zabwino zimene iye anati sayansi imachita monga kuthandiza anthu kuchita zinthu mwanzeru, mosayang’ana nkhope, ndiponso mosatengeka maganizo, Postgate ananena kuti “sayansi yalanda malo a khalidwe labwino.”

Kodi n’zoonadi kuti sayansi ndi yomwe yalanda malo a khalidwe labwino? Yankho la funsoli n’lakuti ayi. Postgate iye mwini anavomereza kuti “anthu okhulupirira sayansi nawo amachita nsanje, umbombo, kusankhana ndiponso njiru.” Ananenanso kuti “pali asayansi angapo ndithu amene aonetsa kuti angathe kupha anthu n’cholinga chofuna kufufuza zinthu, monga mmene anachitira asayansi ena ku Germany panthaŵi ya ulamuliro wachipani cha Nazi ndiponso ku ndende za ku Japan.” Ndipo pamene kampani yopanga magazini ya National Geographic inatumiza mtolankhani woti akafufuze chimene chinachitika kuti m’magaziniyi alembemo nkhani yabodza imene asayansi anatumiza yonena za zofukula zinazake zimene ankati n’zakale kwambiri, mtolankhaniyo anapeza kuti chinachitika n’chakuti “asayansiŵa ankasungirana tizinsinsi tawo topweteketsana, ankakulirana mitima, ankadzitukumula, ankakhulupirira zinthu zopanda umboni ngati zawasangalatsa, ankangopeka zinthu, kulakwitsa, kuchita makani, kusintha maonekedwe a zinthu, kujedana, kunamizana, ndi kupatsana ziphuphu.”

Ndiponsotu sayansi ndi imene yathandiza kuti anthu akhale ndi zida zoopsa zomapherana, monga zida za tizilombo toyambitsa matenda, gasi wakupha, mabomba ouluka okha, mabomba otha kuwakhotetsera kumene mukufuna ali kale m’mwamba, ndi mabomba a nyukiliya.

[Chithunzi pamasamba 8, 9]

Mlalang’amba wotchedwa Ant Nebula (Kapena kuti Menzel 3), umene anaujambula ndi makina oonera zinthu zakutali omwe ali mlengalenga otchedwa Hubble Space Telescope

[Mawu a Chithunzi]

NASA, ESA and The Hubble Heritage Team (STScI/AURA)

[Zithunzi patsamba 9]

Sayansi inatulukira kuti dzikoli lili ndi zinthu zambiri zosonyeza kuti zinapangidwa pogwiritsa ntchito nzeru zakuya

[Chithunzi patsamba 10]

Mboni za Yehova zimalemekeza sayansi komanso zimakhulupirira Baibulo