Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Imfa ya Yesu Inathandiza Kuti Akufa Adzaukitsidwe

Imfa ya Yesu Inathandiza Kuti Akufa Adzaukitsidwe

Pamwambo wa Chikumbutso, timakhala ndi mwayi woganizira madalitso amene tidzapeze mtsogolo chifukwa cha dipo. Ena mwa madalitso amenewa ndi kuuka kwa akufa. Yehova sankafuna kuti anthu azifa. N’chifukwa chake anthufe zimatipweteka kwambiri wachibale kapena mnzathu akamwalira. (1 Akor. 15:26) Yesu anamva chisoni kwambiri ataona ophunzira ake akulira chifukwa cha imfa ya Lazaro. (Yoh. 11:33-35) Yesu amachita zinthu mofanana ndi Atate wake. Choncho sitingakayikire kuti Yehova nayenso zimam’pweteka akamationa tikulira chifukwa cha imfa ya wachibale kapena mnzathu. (Yoh. 14:7) Yehova akufunitsitsa kudzaukitsa atumiki ake amene anamwalira. Ifenso tiziyembekezera mwachidwi kuti akufa adzauka.—Yobu 14:14, 15.

Yehova ndi wadongosolo ndipo m’pomveka kunena kuti adzachita zinthu mwadongosolo poukitsa akufa. (1 Akor. 14:33, 40) N’kutheka kuti pa nthawiyo tizidzakhala ndi mwambo wolandira anthu oukitsidwa. Kodi timaganizira za kuuka kwa akufa makamaka pa nthawi yomwe wachibale kapena mnzathu wamwalira? (2 Akor. 4:17, 18) Kodi timathokoza Yehova chifukwa chopereka dipo komanso chifukwa chotidziwitsa kuti akufa adzauka?—Akol. 3:15.

  • Kodi ndi achibale kapena anzanu ati amene mumafunitsitsa kudzaonana nawonso?

  • Kodi ndi anthu ati otchulidwa m’Baibulo amene mumafunitsitsa kudzacheza nawo?