1 Petulo 4:1-19

4  Choncho, pakuti Khristu anavutika m’thupi,+ nanunso dzikonzekeretseni ndi maganizo omwewo,+ chifukwa munthu amene wavutika m’thupi walekana nawo machimo,+  kuti pamene akukhala ndi moyo m’thupi ku nthawi yotsala ya moyo wake,+ asatsatenso zilakolako za anthu, koma chifuniro cha Mulungu.+  Pakuti nthawi+ imene yapitayi inali yokwanira kwa inu kuchita chifuniro cha anthu a m’dzikoli+ pamene munali kuchita zinthu zosonyeza khalidwe lotayirira,+ zilakolako zoipa, kumwa vinyo mopitirira muyezo,+ maphwando aphokoso, kumwa kwa mpikisano, ndi kupembedza mafano kosaloleka.+  Chifukwa chakuti simukupitiriza kuthamanga nawo limodzi m’chithaphwi cha makhalidwe oipa,+ anthu a m’dzikoli sakumvetsa, choncho amakunyozani.+  Koma anthu amenewa adzayankha mlandu kwa yemwe ali+ wokonzeka kuweruza amoyo ndi akufa.+  Ndipotu, pa chifukwa chimenechi uthenga wabwino unalengezedwanso kwa akufa,+ kuti aweruzidwe mwa thupi mogwirizana ndi kuona kwa anthu,+ koma akhale ndi moyo mwa mzimu+ mogwirizana ndi kuona kwa Mulungu.  Koma mapeto a zinthu zonse ayandikira.+ Choncho khalani oganiza bwino,+ ndipo khalani maso kuti musanyalanyaze kupemphera.+  Koposa zonse, khalani okondana kwambiri,+ pakuti chikondi chimakwirira machimo ochuluka.+  Muzicherezana popanda kudandaula.+ 10  Molingana ndi mphatso imene aliyense walandira, igwiritseni ntchito potumikirana monga oyang’anira abwino amene alandira kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu, kumene wakusonyeza m’njira zosiyanasiyana.+ 11  Ngati wina akulankhula, alankhule monga mwa mawu opatulika+ a Mulungu. Ngati wina akutumikira,+ atumikire modalira mphamvu imene Mulungu amapereka,+ kuti m’zinthu zonse Mulungu alemekezeke+ kudzera mwa Yesu Khristu. Ulemerero+ ndi mphamvu, ndi zake mpaka muyaya. Ame. 12  Okondedwa, musadabwe ndi moto umene ukuyaka pakati panu, ngati kuti mukukumana ndi chinthu chachilendo. Motowo ukuyaka pofuna kukuyesani.+ 13  Koma muzikondwera+ pamene mukugawana nawo masautso a Khristu,+ kuti mukasangalalenso ndi kukondwera kwambiri pa nthawi imene ulemerero wake udzaonekere.*+ 14  Ngati anthu akukunyozani chifukwa cha dzina la Khristu,+ ndinu odala+ chifukwa zikusonyeza kuti mzimu waulemerero, umene ndi mzimu wa Mulungu, wakhazikika pa inu.+ 15  Koma pasakhale wina wa inu wovutika+ chifukwa cha kupha munthu, kuba, kuchita choipa china kapena kulowerera nkhani za ena.+ 16  Koma ngati akuvutika+ chifukwa chokhala Mkhristu, asachite manyazi,+ koma apitirize kulemekeza Mulungu m’dzina la Khristuyo. 17  Pakuti ino ndiyo nthawi yoikidwiratu yakuti chiweruzo chiyambe, ndipo chiyambira panyumba ya Mulungu.+ Tsopano ngati chikuyambira pa ife,+ ndiye mapeto a anthu osamvera uthenga wabwino wa Mulungu adzakhala otani?+ 18  “Ndipo ngati munthu wolungama adzapulumuka movutikira,+ kodi munthu wosaopa Mulungu ndi wochimwa adzaoneka n’komwe?”+ 19  Choncho amene akuvutika mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu, aike miyoyo yawo m’manja mwa Mlengi wokhulupirika, pamene akupitiriza kuchita zabwino.+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “udzaululike.”