1 Petulo 2:1-25

2  Chotero, lekani zoipa zonse,+ zachinyengo zonse, zachiphamaso, kaduka ndi mtundu uliwonse wa miseche.+  Koma monga makanda obadwa kumene,+ muzilakalaka mkaka wosasukuluka+ umene uli m’mawu a Mulungu, kuti mwa kumwa mkakawo, mukule ndi kukhala oyenera chipulumutso,+  pakuti mwalawa n’kuona kuti Ambuye ndi wokoma mtima.+  Pamene mukubwera kwa iye, amene ndiye mwala wamoyo+ umene anthu+ anaukana,+ koma umene Mulungu anausankha, umenenso uli wamtengo wapatali kwa iye,+  inunso monga miyala yamoyo mukumangidwa n’kukhala nyumba yauzimu+ kuti mudzakhale ansembe oyera, n’cholinga chakuti mupereke nsembe zauzimu+ zovomerezeka pamaso pa Mulungu kudzera mwa Yesu Khristu.+  Pakuti Lemba limati: “Inetu ndikuika mwala m’Ziyoni, mwala wochita kusankhidwa mwapadera, wapakona pa maziko, wamtengo wapatali, ndipo aliyense woukhulupirira sadzakhumudwa.”+  Choncho iye ndi wamtengo wapatali kwa inu chifukwa ndinu okhulupirira, koma kwa osakhulupirira, “mwala umene omanga nyumba anaukana,+ umenewu wakhala mwala wapakona wofunika kwambiri,”+  komanso “mwala wopunthwitsa ndi thanthwe lokhumudwitsa.”+ Anthu amenewa akupunthwa chifukwa samvera mawu, ndipo anaikidwiratu kale kuti adzatero.+  Koma inu ndinu “fuko losankhidwa mwapadera, ansembe achifumu, mtundu woyera,+ anthu odzakhala chuma chapadera,+ kuti mulengeze makhalidwe abwino kwambiri”+ a amene anakuitanani kuchoka mu mdima kulowa m’kuwala kwake kodabwitsa.+ 10  Pakuti kale simunali mtundu, koma tsopano ndinu mtundu wa anthu a Mulungu.+ Munali anthu amene sanakuchitireni chifundo, koma tsopano ndinu amene mwachitiridwa chifundo.+ 11  Okondedwa, popeza ndinu alendo ndiponso anthu osakhalitsa m’dzikoli,+ ndikukudandaulirani kuti muzipewa zilakolako za thupi+ zimene zili pa nkhondo yolimbana ndi moyo.+ 12  Khalani ndi khalidwe labwino pakati pa anthu a m’dzikoli,+ kuti pamene akukunenerani monga anthu ochita zoipa, pa mapeto pake iwo pokhala mboni zimene zikuona ndi maso zochita zanu zabwino,+ adzatamande Mulungu m’tsiku lake loyendera.+ 13  Chifukwa cha Ambuye, gonjerani+ dongosolo lililonse lopangidwa ndi anthu:+ kaya mfumu+ chifukwa ili ndi udindo waukulu, 14  kapena nduna chifukwa n’zotumidwa ndi mfumuyo kuti zizipereka chilango kwa ochita zoipa ndi kuyamikira ochita zabwino.+ 15  Pakuti chifuniro cha Mulungu n’chakuti, mwa kuchita zabwino muwatseke pakamwa anthu opanda nzeru olankhula zaumbuli.+ 16  Khalani mfulu,+ koma ufulu wanu usakhale ngati chophimbira zoipa,+ koma monga akapolo a Mulungu.+ 17  Lemekezani anthu, kaya akhale amtundu wotani.+ Kondani gulu lonse la abale,+ opani Mulungu,+ lemekezani mfumu.+ 18  Antchito a panyumba akhale ogonjera+ mabwana awo ndi mantha oyenera,+ osati kwa mabwana abwino ndi ololera okha, koma ngakhalenso kwa ovuta kuwakondweretsa. 19  Pakuti zili bwino ngati wina, chifukwa cha chikumbumtima chake kwa Mulungu, akupirira zowawa ndi kuvutika popanda mlandu.+ 20  Kodi kupirira kumenyedwa mbama mutachimwa kuli ndi phindu lanji?+ Koma ngati mukupirira povutika chifukwa cha kuchita zabwino,+ zimenezo n’zabwino kwa Mulungu.+ 21  Ndipotu anakuitanirani ku moyo umenewu, pakuti ngakhale Khristu anavutika chifukwa cha inu,+ ndipo anakusiyirani chitsanzo kuti mutsatire mapazi ake mosamala kwambiri.+ 22  Iye sanachite tchimo,+ ndipo m’kamwa mwake simunapezeke chinyengo.+ 23  Pamene anali kunenedwa zachipongwe,+ sanabwezere zachipongwe.+ Pamene anali kuvutika,+ sanawopseze, koma anali kudzipereka kwa iye+ amene amaweruza molungama. 24  Iye ananyamula machimo athu+ m’thupi lake pamtengo,+ kuti tilekane ndi machimo+ n’kukhala amoyo m’chilungamo. Ndipo “munachiritsidwa ndi mabala ake.”+ 25  Pakuti munali ngati nkhosa zosochera,+ koma tsopano mwabwerera kwa m’busa+ wanu ndi woyang’anira miyoyo yanu.

Mawu a M'munsi