1 Petulo 3:1-22
3 Momwemonso+ inu akazi, muzigonjera+ amuna anu kuti ngati ali osamvera+ mawu akopeke,+ osati ndi mawu, koma ndi khalidwe lanu,+
2 poona okha ndi maso awo khalidwe lanu loyera+ ndi ulemu wanu waukulu.
3 Ndipo kudzikongoletsa kwanu kusakhale kwakunja, monga kumanga tsitsi,+ kuvala zodzikongoletsera zagolide,+ kapena kuvala malaya ovala pamwamba.
4 Koma kukhale kwa munthu wobisika+ wamumtima, atavala zovala zosawonongeka,+ ndizo mzimu wabata ndi wofatsa+ umene uli wamtengo wapatali pamaso pa Mulungu.
5 Pakuti ndi mmenenso kale akazi oyera amene anali kuyembekeza Mulungu anali kudzikongoletsera. Analinso kugonjera amuna awo,
6 monga mmene Sara analili womvera kwa Abulahamu, ndipo anali kumutcha kuti “mbuyanga.”+ Tsopano inuyo mwakhala ana ake, ndipo mukhalabe ana ake mukapitiriza kuchita zabwino ndi kusaopa chochititsa mantha chilichonse.+
7 Inunso amuna,+ pitirizani kukhala ndi akazi anu mowadziwa bwino,+ ndi kuwapatsa ulemu+ monga chiwiya chosalimba, kuti mapemphero anu asatsekerezedwe,+ pakuti mudzalandira nawo limodzi moyo+ umene Mulungu adzakupatseni chifukwa cha kukoma mtima kwake kwakukulu.
8 Pomaliza, nonsenu mukhale amaganizo amodzi,+ omverana chisoni, okonda abale, achifundo chachikulu,+ ndiponso amaganizo odzichepetsa.+
9 Osabwezera choipa pa choipa+ kapena chipongwe pa chipongwe,+ koma m’malomwake muzidalitsa,+ chifukwa anakuitanirani njira ya moyo imeneyi, kuti mudzalandire dalitso.
10 Pakuti “amene akufuna kusangalala ndi moyo ndi kuona masiku abwino,+ aletse lilime+ lake kuti lisalankhule zoipa ndi milomo yake kuti isalankhule chinyengo,+
11 koma aleke zoipa+ ndipo achite zabwino. Ayesetse kupeza mtendere ndi kuusunga.+
12 Pakuti maso+ a Yehova* ali pa olungama, ndipo makutu ake amamva pembedzero lawo,+ koma nkhope ya Yehova imakwiyira anthu ochita zoipa.”+
13 Ndithudi, ndani angakuchitireni zoipa mukakhala odzipereka pochita zabwino?+
14 Koma ngakhale mutavutika chifukwa cha chilungamo, mudzakhalabe odala.+ Musaope zimene iwo amaopa,+ ndipo musade nazo nkhawa.+
15 Koma vomerezani m’mitima mwanu kuti Khristu ndi Ambuye ndiponso kuti ndi woyera.+ Khalani okonzeka nthawi zonse kuyankha+ aliyense amene wakufunsani za chiyembekezo chimene muli nacho, koma ayankheni ndi mtima wofatsa+ ndiponso mwaulemu kwambiri.
16 Khalani ndi chikumbumtima chabwino,+ kuti ngakhale azikunenerani zoipa ndi kulankhula monyoza za khalidwe lanu labwino monga otsatira Khristu, adzachite manyazi.+
17 Pakuti ndi bwino kuvutika chifukwa chochita zabwino,+ ngati Mulungu walola, kusiyana ndi kuvutika chifukwa chochita zoipa.+
18 Pajatu ngakhale Khristu anafera machimo kamodzi kokha basi.+ Munthu wolungamayo anafera anthu osalungama,+ kuti akufikitseni kwa Mulungu.+ Iye anaphedwa m’thupi,+ koma anaukitsidwa monga mzimu.+
19 Kenako anapita kukalalikira kwa mizimu imene inali m’ndende,+
20 imene inali yosamvera+ pa nthawi imene Mulungu anali kuleza mtima+ m’masiku a Nowa, pamene chingalawa chinali kupangidwa,+ chimene chinapulumutsa pamadzi anthu owerengeka, miyoyo 8 yokha.+
21 Chofanana ndi chingalawacho chikupulumutsanso inuyo tsopano.+ Chimenechi ndicho ubatizo, (osati kuchotsa litsiro la m’thupi, koma kupempha chikumbumtima chabwino kwa Mulungu,)+ mwa kuukitsidwa kwa Yesu Khristu.+
22 Iye ali kudzanja lamanja la Mulungu,+ pakuti anapita kumwamba, ndipo angelo,+ maulamuliro, ndi mphamvu zinakhala pansi pake.+
Mawu a M'munsi
^ Onani Zakumapeto 2.