1 Petulo 5:1-14

5  Choncho, ndikulangiza akulu amene ali pakati panu mowadandaulira, pakuti inenso ndine mkulu+ ngati iwowo. Ndinenso mboni+ ya masautso a Khristu, ndiponso ndidzalandira nawo ulemerero umene udzaonekere.+ Kwa iwo ndikuti:  Wetani+ gulu la nkhosa za Mulungu+ lomwe analisiya m’manja mwanu, osati mokakamizika, koma mofunitsitsa.+ Osatinso chifukwa chofuna kupindulapo kenakake,+ koma ndi mtima wonse.  Osati mochita ufumu+ pa anthu amene ali cholowa chochokera kwa Mulungu,+ koma mukhale zitsanzo kwa gulu la nkhosa.+  Ndipo m’busa wamkulu+ akadzaonekera, mudzalandira mphoto* yosafwifwa,+ yaulemerero.+  Chimodzimodzinso inu anyamata. Muzigonjera+ amuna achikulire. Koma nonsenu muzichitirana zinthu modzichepetsa,+ chifukwa Mulungu amatsutsa odzikweza, koma odzichepetsa amawasonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu.+  Choncho dzichepetseni pansi pa dzanja lamphamvu la Mulungu, kuti adzakukwezeni m’nthawi yake.+  Chitani zimenezi pamene mukumutulira nkhawa zanu zonse,+ pakuti amakuderani nkhawa.+  Khalanibe oganiza bwino ndipo khalani maso.+ Mdani wanu Mdyerekezi akuyendayenda uku ndi uku ngati mkango wobangula, wofunitsitsa kuti umeze winawake.+  Koma inu khalani olimba+ m’chikhulupiriro ndipo mulimbane naye, podziwa kuti anzanunso m’gulu lonse la abale anu m’dzikoli akukumana ndi masautso ngati omwewo.+ 10  Koma mukavutika kwa kanthawi,+ Mulungu, yemwe amapereka kukoma mtima konse kwakukulu, amenenso anakuitanirani ku ulemerero wake wosatha+ kudzera mu mgwirizano wanu+ ndi Khristu, adzamalizitsa kukuphunzitsani. Adzakulimbitsani+ ndi kukupatsani mphamvu.+ 11  Mphamvu zikhale kwa iye+ mpaka muyaya. Ame. 12  Ndakulemberani m’mawu ochepa kudzera mwa Silivano,+ m’bale amene ndikumuona kuti ndi wokhulupirika. Ndakulemberani zimenezi+ kuti ndikulimbikitseni ndi kupereka umboni wamphamvu wakuti kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu n’kumeneku, ndipo mukugwire mwamphamvu.+ 13  Mayi* amene ali ku Babulo,+ wosankhidwa mwapadera ngati inuyo, komanso mwana wanga Maliko,+ akupereka moni. 14  Patsanani moni popsompsonana mwa chikondi chaubale.+ Nonse amene muli ogwirizana ndi Khristu, mtendere ukhale nanu.+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “chisoti chachitsulo chooneka ngati nkhata.”
“Mawu akuti “mayi,” n’kutheka kuti akutanthauza mpingo.