Pitani ku nkhani yake

OCTOBER 17, 2018
UNITED STATES

Mphepo Yamkuntho Yamphamvu Kwambiri ya Michael Yawononga Kwambiri ku United States

Mphepo Yamkuntho Yamphamvu Kwambiri ya Michael Yawononga Kwambiri ku United States

Pa 10 October, 2018, mphepo yamkuntho yotchedwa Michael inawomba ku Florida ndipo inawononga zinthu zambiri kum’mwera cha kum’mawa kwa United States. Mphepoyi ndi imodzi mwa mphepo zamphamvu kwambiri pa mphepo zomwe zakhala zikuwomba ku United States ndipo yawononga katundu wambiri. Mphepoyi yaphanso anthu osachepera 18.

Mphepoyi inakhudza abale ndi alongo m’mipingo 94 ndi m’madera 13. Palibe wa Mboni amene anafa chifukwa cha ngoziyi, koma atatu anavulala. Mphepoyi inawononga nyumba 528 za abale athu komanso Nyumba za Ufumu 34, ndipo Nyumba za Ufumu 39 zinalibe magetsi.

Ofesi ya nthambi ya United States mothandizidwa ndi Komiti Yothandiza Pangozi Zadzidzidzi komanso oyang’anira madera oposa 40, akuyendetsa ntchito yothandiza anthu omwe akhudzidwa ndi ngoziyi. Ntchitoyi ikuphatikizapo kupatsa abale athu zinthu monga chakudya, chithandizo cha mankhwala, malo okhala, madzi, komanso kukonza nyumba zowonongeka poika malona pa madenga komanso kuchotsa zinthu zomwe zawonongeka chifukwa cha mitengo yomwe inagwa. Pakonzedwanso zoti abale ndi alongo omwe akhudzidwa ndi ngoziyi alimbikitsidwe ndi mfundo za m’Mawu a Mulungu.

Ngakhale kuti abale ndi alongo athu amakumananso ndi mavuto m’dzikoli, kuphatikizapo mavuto omwe amabwera chifukwa cha ngozi zamwadzidzidzi, iwo amadalira kwambiri Mulungu wathu kuti awathandiza.—Salimo 142:5.