Pitani ku nkhani yake

OCTOBER 10, 2018
JAPAN

Mphepo Yamkuntho Yotchedwa Trami Yawononga ku Japan Posachedwapa

Mphepo Yamkuntho Yotchedwa Trami Yawononga ku Japan Posachedwapa

Lamlungu pa 30 September, 2018, Mphepo Yamkuntho yotchedwa Trami inawomba kum’mwera kwa dziko la Japan ndipo inachititsa kuti kuyambe mphepo yamphamvu ndiponso mvula yambiri. Mphepoyi inayamba kuchepa mphamvu pamene inkaomba chakumpoto kwa dzikolo ndipo kenako Lolemba pa 1 October, inafika mumzinda wa Tokyo. Anthu atatu anafa ndipo ena 200 anavulala komanso magetsi anazima m’nyumba zopitirira 1.3 miliyoni.

Malipoti ochokera kwa oyang’anira madera akusonyeza kuti mphepoyi inawononga kwambiri zinthu pachilumba cha Okinawa, chomwe chili kum’mwera kwa Japan. Pa kafukufuku woyambirira yemwe anachitika m’madera atatu a ku Okinawa komanso ena oyandikana nawo, anapeza kuti palibe wa Mboni aliyense yemwe anafa koma 9 anavulala. Pachilumba cha Okinawa pomwepo, mphepoyi inaononganso nyumba 120 za abale athu komanso Nyumba za Ufumu 5. Nyumba za Ufumu zinanso 41 zinaonongeka pa nthawi imene mphepoyi inkawomba m’madera enanso a m’dziko la Japan.

Oyang’anira madera komanso abale a mu Dipatimenti Yoona za Mapulani ndi Zomangamanga akupitirizabe kufufuza kuti adziwe kuchuluka kwa zinthu zomwe zaonongeka komanso kuti adziwe mmene angalimbikitsire abale awo ndi mfundo za m’Baibulo ndi kuwapatsa zinthu zofunika pamoyo.

Tikupitirizabe kupempherera Akhristu anzathu omwe akhudzidwa ndi mphepoyi komanso ngozi zadzidzidzi zinanso zomwe zachitika posachedwapa ku Japan. Tikukhulupirira kuti Atate wathu wakumwamba apitiriza kutonthoza mitima ya abale ndi alongo athu komanso kuwalimbikitsa.—2 Atesalonika 2:17.