South Korea
A Mboni za Yehova Anagwira Ntchito Yapadera Yogawira Mabuku Pampikisano wa 2018 wa Olimpiki Komanso wa Anthu Olumala
A Mboni za Yehova ku Korea anagwira ntchito yapadera yogawira mabuku ofotokoza Baibulo kwaulere kwa alendo ochokera m’mayiko ena ku mpikisano wa Olimpiki wa 2018.
A Mboni ku South Korea Anapempha Pulezidenti kuti Athetse Kumanga Anthu Okana Usilikali Chifukwa cha Zimene Amakhulupirira
A Mboni akudikira pamene akuluakulu a boma akuganizira nkhani yokhudza kumanga anthu amene akana usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira.
Makhoti a ku South Korea Akufufuza Njira Yabwino Yochitira Zinthu ndi Anthu Okana Usilikali
Oweruza a ku South Korea akufufuza njira yothandizira anthu okana usilikali m’malo mongowamanga. Khoti loona za malamulo lipereka chigamulo pa nkhaniyi.
Khoti la ku South Korea Lamva Madandaulo a Anthu Okana Usilikali
Khoti linagamula kuti likulu la asilikali lisiye kufalitsa pawebusaiti yawo mayina, ma adiresi komanso zinthu zina zokhudza anthu omwe amakana usilikali chifukwa cha zomwe amakhulupirira.
Dziko la South Korea Likuchitira a Dong-hyuk Shin Zinthu Zopanda Chilungamo
Ufulu wa a Shin wochita zinthu mogwirizana ndi chikumbumtima chawo komanso chipembedzo chawo ukuphwanyidwa powalanga mopanda chilungamo chifukwa chokana kuchita maphunziro a ntchito ya usilikali.
“Chigamulo cha Khoti Chabwino Kwambiri Chaka Chino”
Khoti la Apilo la Gwangju linagamula kuti anyamata atatu ndi osalakwa pa mlandu womwe ankaimbidwa chifukwa chokana usilikali. Aliyense akuyembekezera kuti khoti lapamwamba kwambiri lipereke chigamulo chake.
Posachedwapa Khoti Loona za Malamulo ku South Korea Litulutsa Chigamulo Chofunika Kwambiri
Khotili likagamula mlanduwu mwachilungamo, anthu omwe amakana usilikali potsatira zomwe amakhulupirira akhala ndi ufulu komanso pakhala ufulu wachipembedzo kwa nzika zonse za ku South Korea.
A Mboni za Yehova Omwe Ali M’ndende ku South Korea Aperekanso Madandaulo Ena
Dziko la South Korea likupitiriza kuzunza anyamata omwe ndi a Mboni za Yehova powaika m’ndende chifukwa chogwiritsa ntchito ufulu umene ali nawo wopembedza komanso wochita zinthu mogwirizana ndi zimene amakhulupirira.
Kodi Dziko la South Korea Liyamba Kulemekeza Ufulu wa Anthu Wochita Zinthu Mogwirizana ndi Zimene Amakhulupirira?
A Seon-hyeok Kim, omwe ndi a Mboni za Yehova ndipo sagwira ntchito ya usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira, poyamba anawapeza kuti ndi wosalakwa pa mlandu woti ankazemba usilikali. N’chifukwa chiyani khoti la apilo linasintha chigamulochi n’kunena kuti a Kim ndi wolakwa?
Komiti ina ya United Nations Yapempha Dziko la South Korea Kuti Lipereke kwa Anthu Ufulu Wokana Usilikali Chifukwa cha Zimene Amakhulupirira
Mayiko ambiri ali ndi chidwi kuti aone ngati boma la South Korea litsatire zimene komiti ya UN yapempha n’kuchita zinthu mogwirizana ndi Pangano la Dziko Lonse la Ufulu wa Anthu ndi wa Zandale.
A Mboni a ku Korea Anapereka Madandaulo Awo ku Gulu la United Nations Loona za Anthu Omangidwa Popanda Zifukwa Zomveka
Mayiko ena komanso makhoti a m’dziko la South Korea akufuna kuti dzikolo lisiye kumanga anthu amene amakana usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira, m’malo mwake liziwapatsa mwayi wogwira ntchito zina.
Khoti Lalikulu ku South Korea Lipereka Chigamulo pa Nkhani ya Anthu Okana Usilikali Chifukwa cha Zimene Amakhulupirira
Khotili linaimitsa mlanduwu kuti liganize kaye ngati malamulo a asilikali onena kuti anthu okana usilikali ayenera kulandira chilango akugwirizana ndi malamulo a dziko kapena ayi.
Dziko la South Korea Lapezeka ndi Mlandu Womanga Anthu Okana Kulowa Usilikali Chifukwa cha Zimene Amakhulupirira
Chaka chilichonse, dziko la South Korea limamanga anyamata a Mboni chifukwa chokana kulowa usilikali potsatira zimene amakhulupirira. Komiti Yoona za Ufulu Wachibadwidwe ya Bungwe la United Nations lanenetsa kuti dziko la South Korea lilibe zifukwa zomveka zomangira a Mboniwa. Aka ndi ka nambala 5 kuti komitiyi ikane zifukwazi.