MARCH 1, 2018
SOUTH KOREA
A Mboni ku South Korea Anapempha Pulezidenti kuti Athetse Kumanga Anthu Okana Usilikali Chifukwa cha Zimene Amakhulupirira
Posachedwapa zinthu zina zachitika kuti South Korea zomwe zikusonyeza kuti mwina boma lisintha kwambiri zimene limachita pa nkhani yolemekeza ufulu wa anthu. Pa 7 December 2017, pulezidenti wa dzikoli dzina lake Jae-in Moon anakumana ndi akuluakulu a Bungwe Loona za Ufulu wa Anthu m’dzikoli ndipo anawafunsa zimene angachite kuti ayambe kulemekeza ufulu wa anthu ngati mmene amachitira m’mayiko ena. Pulezidenti Moon anapempha bungweli kuti limuuze njira zimene zingathandize boma kuti lisiye kumanga anthu amene amakana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira.
Pambuyo pa msonkhano umenewu, a Mboni za Yehova ku South Korea anakonza zoti anthu ambirimbiri asaine zikalata zopita kwa pulezidenti. Zimene boma lakhala likuchita pa nkhani yomanga anthu okana usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira zakhudza a Mboni ambirimbiri. Pulezidenti Moon analamula akuluakulu a boma kuti aziyesetsa kuthandiza nzika za South Korea zimene zalemba zikalata. Choncho a Mboni analemba zikalata n’kupempha kuti pulezidenti awathandize pa vutoli, lomwe lakhalapo kwa zaka pafupifupi 70.
Ofesi ya Mboni za Yehova ku South Korea ndi imene inakonza zoti zikalatazi zilembedwe n’kusainidwa
Zikalatazi zinakonzedwa ndiponso kusainidwa ndi anthu ambiri milungu 4 isanathe. Ena mwa anthu amene anasaina zikalatazi anali amuna oposa 14,000 omwe analangidwa chifukwa chokana usilikali komanso achibale awo oposa 26,000 omwe anavutika chifukwa choti amunawa anaimbidwa mlandu n’kumangidwa.
Zikalata zimene zinaperekedwa ku Ofesi ya Pulezidenti pa 15 January 2018
Pa 15 January 2018, a Mboni 6 omwe ankaimira a Mboni za Yehova 41,275, omwe anasaina zikalatazo, anazipititsa ku Ofesi ya Pulezidenti. Zikalatazi zinayamikira pulezidenti chifukwa chofuna kuthetsa vutoli, zinafotokoza mavuto amene abwera pa zaka 70 zomwe akhala akumanga anthu okana usilikali komanso zinafotokoza ubwino umene dzikoli lingapeze akathetsa vutoli. Pa 16 January 2018, Ofesi ya Pulezidenti inatumiza zikalatazi ku Unduna wa Zachitetezo kuti uone zimene ungachite pa nkhaniyi.
Pa nthawi imene ankakonza zikalatazo, a Mboni za Yehova anakumananso ndi akuluakulu a Bungwe Loona za Ufulu wa Anthu. Iwo anafotokoza zifukwa zochokera m’Baibulo zimene zimachititsa kuti a Mboni za Yehova azikana kulowa usilikali. Anafotokozanso kuti ngati angapatsidwe ntchito ina yosakhudza usilikali ndiye kuti m’malo mongokhala m’ndende, boma lingawagwiritse ntchito kuti azichita zinthu zina zothandiza m’dzikoli. Akuluakulu a bungweli anauza a Mboniwo kuti nkhani yothetsa kumanga anthu okana usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira ndi yofunika kwambiri m’bungweli mu 2018.
Chiwerengero cha anthu amene amangidwa chifukwa chokana usilikali ku South Korea ndi chachikulu kuposa chiwerengero cha anthu amene amangidwa pa chifukwa chomwechi m’mayiko ena onse. Tikaphatikiza zaka zonse zimene anyamata a Mboni akhala m’ndende ku South Korea chifukwa chokana usilikali, zimaposa zaka 36,700. A Mboni za Yehova angakonde kuti akuluakulu amene akuionanso nkhaniyi afike pothetsa vutoli.