Pitani ku nkhani yake

28 MARCH 2023
NKHANI ZA PADZIKO LONSE

Mphepo Yamkuntho Yotchedwa Freddy Yawononga Kum’mawa kwa Africa

Mphepo Yamkuntho Yotchedwa Freddy Yawononga Kum’mawa kwa Africa

Posachedwapa m’mayiko a kum’mawa kwa Africa akhudzidwa ndi mphepo yamkuntho yotchedwa Freddy. Imeneyi ndi imodzi mwa mphepo yomwe inawomba kwa nthawi yaitali kwambiri poyerekeza ndi mphepo zina m’mbuyomu. Kumayambiriro kwa February 2023, mphepoyi itayamba inawononga m’mayiko enanso. Pa 21 February 2023, inawononga ku Madagascar kenako inadutsa m’chigawo china cha ku nyanja yaikulu ya Indian. Patapita masiku angapo inafika ku Mozambique ndi Malawi. Chimphepochi chinapitirizabe kuwomba ndipo chinabwereranso kachiwiri ku Mozambique pa 11 March 2023. Madera ambiri a ku Madagascar, Malawi ndi Mozambique akhudzidwa kwambiri. M’maderawa, mphepo zamphamvu komanso chimvula champhamvu zachititsa kuti madzi asefukire komanso zawononga nyumba ndi kupha anthu oposa 500 kuphatikizapo abale ndi alongo athu ambiri. Enanso ambiri athawa m’nyumba zawo.

Pofika pa 27 March 2023, talandira malipoti otsatirawa. Ziwerengerozi n’zotsimikizika ndipo zachokera kwa abale am’maderawa. Komabe, ziwerengerozi zikhoza kukwera chifukwa abale akupitiriza kufufuza mmene mphepoyi yawonongera m’madera ovuta kufikako.

Mmene Zakhudzira Abale ndi Alongo Athu

Madagascar

 • Ofalitsa 256 limodzi ndi anthu ena omwe amakhala nawo limodzi athawa m’nyumba zawo

 • Nyumba 8 zinawonongekeratu

 • Nyumba 29 zinawonongeka mbali zina

 • Nyumba za Ufumu zitatu zinawonongeka mbali zina

Malawi

 • N’zomvetsa chisoni kuti ofalitsa 8 anafa ndipo ena 6 akusowa mpaka pano

 • Ofalitsa atatu anavulala

 • Ofalitsa osachepera 4,300 limodzi ndi anthu ena am’banja mwawo anathawa m’nyumba zawo

 • Nyumba 821 zinawonongekeratu

 • Nyumba 174 zinawonongeka mbali zina

 • Nyumba za Ufumu 20 zinawonongeka mbali zina

Mozambique

 • N’zomvetsa chisoni ku wofalitsa mmodzi anafa ndiponso wina akusowa

 • Ofalitsa 880 limodzi ndi anthu ena am’banja mwawo anathawa m’nyumba zawo

 • Nyumba 248 zinawonongekeratu

 • Nyumba 185 zinawonongeka mbali zina

 • Nyumba za Ufumu 7 zinawonongeka mbali zina

Ntchito Yothandiza Anthu

 • Pakali pano zikuvutabe kufika kumadera ena amene mphepoyi inawononga

 • Makomiti Othandiza pa Ngozi za Mwadzidzidzi akuthandiza anthu okhudzidwa kupeza malo abwino okhala, chakudya, madzi ndi zinthu zina zofunika

 • M’bale wa m’Komiti ya Nthambi akulimbikitsa gulu la abale ndi alongo pafupi ndi dera lotchedwa Chókwè ku Mozambique

  M’dera la Gaza ku Mozambique kunakonzedwa kampu yoti ofalitsa 167 limodzi ndi mabanja awo amene akukhala pa Malo a Msonkhano kuti azikhalamo mongoyembekezera. Ofalitsa enanso ochuluka akukhala m’Nyumba za Ufumu komanso za anthu ena m’derali

 • Nyumba zosachepera 16 zakonzedwa kale

 • Abale a m’komiti ya nthambi komanso oyang’anira madera ndi akulu m’mipingo akuyendera mabanja okhudzidwa kuti adziwe zimene akufunikira komanso kuwalimbikitsa

Ngakhale kuti akumana ndi mavutowa, abale ndi alongowa akupitiriza kuchita misonkhano ngati zili zotheka kutero komanso kulimbikitsana. Sitikukayikira kuti Yehova awapatsa “mphamvu yoposa yachibadwa” kuti iwathandize kupirira.—2 Akorinto 4:7.