Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NSANJA YA OLONDA Na. 3 2017 | Kodi Ulosi wa Okwera Pamahatchi Umatikhudza Bwanji?

KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI?

Ambiri amadziwa ulosi wonena za anthu 4 okwera pamahatchi wopezeka m’buku la Chivumbulutso. Ena amachita mantha akawerenga ulosiwu, pomwe ena umawasangalatsa. Taonani zimene Baibulo limanena zokhudza ulosiwu:

“Wodala ndi munthu amene amawerengera ena mokweza, ndiponso anthu amene akumva mawu a ulosi umenewu.”Chivumbulutso 1:3.

Nsanja ya Olonda iyi ikufotokoza kuti ulosi umenewu ndi nkhani yosangalatsa kwa anthufe.

 

NKHANI YAPACHIKUTO

Kodi Ulosi wa Anthu 4 Okwera Pamahatchi Umakukhudzani Bwanji Inuyo?

Mahatchi 4—yoyera, yofiira, yakuda ndi yotuwa. Anthu ambiri amadziwa za ulosi wonena za mahatchi othamanga kwambiri wopezeka m’buku la chivumbulutso.

NKHANI YAPACHIKUTO

Kodi Anthu 4 Okwera Pamahatchi Akuimira Chiyani?

Werengani nkhaniyi kuti mudziwe tanthauzo la ulosi umenewu.

Umboni Wina Wosonyeza Kuti Baibulo Ndi Lolondola

Mwina simunamvepo za Tatenai, komabe ofukula zakale anapeza umboni wotsimikizira kuti iye anakhalako.

BAIBULO LIMASINTHA ANTHU

Ndinkakonda Kwambiri Masewera a Baseball Kuposa Chilichonse

A Samuel Hamilton ankakonda kwambiri masewera a Baseball koma atayamba kuphunzira Baibulo anasintha.

TSANZIRANI CHIKHULUPIRIRO CHAWO

“Ndiwe Mkazi Wokongola”

Ali ku Iguputo, akalonga a Farao anaona kuti Sara anali mkazi wokongola. Ndiye kodi mukuganiza kuti zinatha bwanji?

Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Kodi Yehova amakonda kwambiri mtundu wina wa anthu kuposa wina? Kodi anthu ena ndi odalitsidwa pamene ena ndi oterembereredwa?

Zina zimene zili pawebusaiti

Kodi dzina la buku la m’Baibulo, lakuti Chivumbulutso, limatanthauza chiyani?

Kodi Dzina la Buku la M’Baibulo, Lakuti Chivumbulutso, Limatanthauza Chiyani?