Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO | KODI ULOSI WA OKWERA PAMAHATCHI UMATIKHUDZA BWANJI?

Kodi Ulosi wa Anthu 4 Okwera Pamahatchi Umakukhudzani Bwanji Inuyo?

Kodi Ulosi wa Anthu 4 Okwera Pamahatchi Umakukhudzani Bwanji Inuyo?

Yerekezerani kuti muli pamalo enaake ndipo mwadzidzidzi patulukira mahatchi 4 omwe akuthamanga kwambiri. Nkhani ya mahatchi 4 ndi okwerapo ake inalembedwa m’Baibulo. Tikamawerenga nkhaniyi, zimangokhala ngati tikuona zimene zikuchitikazo. Hatchi yoyamba ndi yoyera ndipo wokwerapo wake ndi mfumu yaulemerero yomwe yangoikidwa kumene pa udindowu. Pambuyo pake pakubwera hatchi yofiira ngati moto ndipo wokwerapo wake akuchotsa mtendere padziko lonse lapansi. Kenako pakubweranso hatchi yakuda ngati mdima wandiweyani. Wokwerapo wake wanyamula sikelo ndipo ali ndi uthenga wonena za kusowa kwa chakudya. Ndiyeno pakubweranso hatchi yotuwa yomwe ikuimira matenda komanso zinthu zina zomwe zikupulula miyoyo ya anthu ambiri. Wokwerapo wake ndi Imfa, ndipo Manda akuitsatira pafupi kwambiri n’kumalandira anthu akufawo.Chivumbulutso 6:1-8.

Mayi ena dzina lawo a Crystal anati: “Nditawerenga nkhani yonena za anthu 4 okwera pamahatchi, ndinachita mantha kwambiri. Ndinkaona kuti Tsiku la Chiweruzo lili pafupi ndipo popeza ndinali ndisanakonzeke, ndinkaona kuti sindidzapulumuka.”

Bambo ena dzina lawo a Ed anati: “Nditawerenga za anthu 4 okwera pamahatchi komanso mmene anawafotokozera, ndinachita chidwi kwambiri. Ndiyeno nditazindikira tanthauzo la masomphenyawa, ndinaona kuti ndi zomvekadi.”

Kodi inuyo mukawerenga nkhani imeneyi mumamva bwanji? Kodi mumachita mantha ngati Mayi Crystal kapena mumachita chidwi ngati Bambo Ed? Kaya inuyo zimakukhudzani bwanji, mfundo ndi yakuti nkhaniyi ndi yodziwika kwambiri ndipo imapezeka m’Baibulo m’buku la Chivumbulutso. Kodi mukudziwa kuti kuzindikira tanthauzo la ulosi umenewu kungakuthandizeni kwambiri? Tikutero chifukwa chakuti Mawu a Mulungu amasonyeza kuti mukamawerenga ndi kuphunzira buku la Chivumbulutso komanso kutsatira zimene zili m’bukuli, mungakhale osangalala.Chivumbulutso 1:1-3.

Anthu ena amachita mantha akawerenga ulosiwu. Koma cholinga cha nkhani imeneyi si kuopseza anthu. Ndipotu anthu ambiri amaona kuti nkhani imeneyi imalimbitsa chikhulupiriro chawo komanso imawathandiza kudziwa kuti mavuto onse atha posachedwapa. Choncho tikukupemphani kuti muwerenge nkhani yotsatirayi ndipo muona kuti ulosi umenewu ungakuthandizeninso inuyo.