Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Phale lakale ili, lili ndi dzina la Tatanu m’mbali mwake

Umboni Wina Wosonyeza Kuti Baibulo Ndi Lolondola

Umboni Wina Wosonyeza Kuti Baibulo Ndi Lolondola

Kodi pali umboni uliwonse wochokera kwa akatswiri ofukula zinthu zakale wosonyeza kuti Baibulo ndi lolondola? M’chaka cha 2014 nkhani ya m’magazini ina inali ndi funso lakuti, “Kodi ndi anthu angati m’Malemba Achiheberi amene umboni woti analiko umapezekanso m’zinthu zimene akatswiri ofukula zakale anapeza?” (Biblical Archaeology Review) Yankho la funsoli linali lakuti “Osachepera 50.” Munthu wina wotchulidwa m’Baibulo amene sanatchulidwe pamndandanda wa anthu amenewa, ndi Tatenai. Kodi Tatenai anali ndani? Tiyeni tione mwachidule zimene Baibulo limanena zokhudza munthu ameneyu.

Pa nthawi ina mzinda wa Yerusalemu unkalamuliridwa ndi Ufumu wa Perisiya. Mzindawu unali kumadzulo kwa mtsinje wa Firate ndipo anthu a ku Perisiya ankatchula deralo kuti tsidya lina la Mtsinje. Aperisiya atagonjetsa Ababulo, anamasula Ayuda n’kuwauza kuti akamangenso kachisi wa Yehova ku Yerusalemu. (Ezara 1:1-4) Koma adani a Ayuda anayamba kutsutsa ntchito yomanga kachisiyo ndipo ankanena kuti Ayudawo akuukira Ufumu wa Perisiya. (Ezara 4:4-16) Pa nthawi ya ulamuliro wa Dariyo Woyamba (522-486 B.C.E.), mkulu wina wa boma la Perisiya, dzina lake Tatenai, anatsogolera ntchito yofufuza za nkhaniyi. Baibulo limati Tatenai anali “bwanamkubwa wa kutsidya lina la Mtsinje.”Ezara 5:3-7.

Akatswiri ofufuza zakale anapeza mapale angapo omwe ali ndi dzina la Tatenai. Mapalewa anasungidwa ngati mbiri ya banja linalake. Pa limodzi mwa mapale amenewa panali mawu osonyeza kuti panali mgwirizano pakati pa munthu wina wa ku banjali ndi munthu wina wotchulidwa m’Baibulo. Phaleli ndi la m’chaka cha 502 B.C.E., chomwe ndi chaka cha 20 cha ulamuliro wa Dariyo Woyamba. Paphale limeneli panalembedwa mawu osonyeza kuti anthu anagwirizana kuti adzapatsana ndalama. Ndiyeno munthu amene anali mboni ya nkhaniyi anali wantchito wa “Tatanu, bwanamkubwa wa kutsidya lina la Mtsinje.” Tatanu ameneyu, ndi Tatenai wotchulidwa m’Baibulo m’buku la Ezara.

Kodi munthu ameneyu anali ndi udindo wotani? Mu 535 B.C.E., Koresi Wamkulu anagawanso ufumu wake m’zigawo ndipo chigawo china ankachitchula kuti “Babulo Komanso Tsidya Lina la Mtsinje.” Kenako chigawo chimenechi anachigawa n’kukhala zigawo ziwiri ndipo chinacho ankangochitchula kuti Tsidya Lina la Mtsinje. M’chigawo chimenechi munali Kole-Siriya, Foinike, Samariya komanso Yuda ndipo bwanamkubwa wake ayenera kuti ankakhala ku Damasiko. Tatenai anali bwanamkubwa wa chigawo chimenechi kuyambira mu 520 mpaka 502 B.C.E.

Ndiyeno Tatenai atabwerako ku Yerusalemu kokafufuza nkhani yakuti Ayuda akuukira boma ija, anapereka lipoti kwa Dariyo. Lipotilo linali lakuti Ayudawo anati Koresi ndi amene anawapatsa chilolezo choti amange kachisi wa Yehova. Dariyo atafufuza za nkhaniyo m’mabuku, anapeza kuti zimene Ayuda ananena zinalidi zoona. (Ezara 5:6, 7, 11-13; 6:1-3) Choncho Tatenai anauzidwa kuti asalowerere nkhaniyo ndipo anamvera.Ezara 6:6, 7, 13.

Kunena zoona, Tatenai, yemwe anali “bwanamkubwa wa kutsidya lina la Mtsinje,” sikuti anachita zinthu zambiri zoti n’kumukumbukira nazo. Koma n’zochititsa chidwi kuti Baibulo limatchula munthuyu ndipo linafotokoza zoona pa nkhani ya udindo wake. Zimenezi ndi umboni winanso wosonyeza kuti nthawi zambiri akatswiri ofukula zakale amapeza zinthu zosonyeza kuti Baibulo ndi lolondola pa nkhani ya mbiri yakale.