Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MBIRI YA MOYO WANGA

Ndinapeza Chinthu Chamtengo Wapatali Kuposa Kukhala Wotchuka

Ndinapeza Chinthu Chamtengo Wapatali Kuposa Kukhala Wotchuka

Tsiku lina m’chaka cha 1984, zinthu zinasintha kwambiri pa moyo wanga. Pa tsikuli, ndinasankhidwa kukhala chiphadzuwa cha mzinda wa Hong Kong ndipo dzina langa linali m’kamwam’kamwa. Zithunzi zanga zinali patsamba loyamba la magazini komanso nyuzipepala. Kuchokera nthawi imeneyo, ndinayamba kuimba, kuvina, kulankhula pa zochitika zapadera, komanso kuchititsa mapulogalamu a pa TV. Ndinkatchena osati masewera komanso ndinkadziwana ndi anthu otchuka. Mwachitsanzo ndinkadziwana ndi gavanala wa mzinda wa Hong Kong.

Kenako m’chaka cha 1985, ndinakhala akita wa mafilimu ndipo nthawi zambiri ndinkakhala mwinifilimu. Atolankhani ambiri ankakonda kulemba nkhani zanga, ojambula zithunzi ankakonda zithunzi zanga komanso ndinkaitanidwa pa zochitika zapadera. Ndiponso anthu ambiri ankandiitana kuti ndikadye nawo limodzi. Aliyense ankachita nane chidwi.

Ali m’filimu ina ya nkhondo

Koma kenako ndinazindikira kuti zomwe ndinkachitazi sizinkandithandiza kukhala wosangalala. Mafilimu omwe tinkapanga ankakhala andewu komanso ankhondo. Zimene ndinkachita poakita mafilimuwa zinkakhala zoopsa. Mwachitsanzo, popanga mafilimu pamakhala mbali zina zovuta kwambiri zomwe ngati utapanda kusamala ukhoza kuvulala kwambiri. Oakita mafilimu a ku America amakhala ndi anthu ena omwe amachita mbali zimenezi n’cholinga choti mwinifilimu asavulale. Koma zimenezi si zimene ankachita akatswiri a mafilimu a ku Hong Kong moti inenso ndinkachita zinthu zoopsa monga kulumpha galimoto ndili panjinga yamoto. Mafilimu ambiri omwe ndinkapanga nawo anali achiwerewere, andewu komanso a zamizimu.

M’chaka cha 1995, ndinakwatirana ndi katswiri wokonza mafilimu. Pa nthawi imeneyo zinthu zinkaoneka kuti zikundiyendera chifukwa ndinali wotchuka, wachuma komanso ndinali ndi mwamuna wabwino. Koma zoona zake n’zakuti ndinkakhala wopanikizika ndipo sindinkakhala wosangalala. Kenako ndinaganiza zosiya kuchita mafilimu.

NDINAKUMBUKIRA ZIMENE NDINKACHITA NDILI MWANA

Nditasiya zamafilimu ndinayamba kuganizira zomwe ndinkakonda kuchita ndili mwana. Nthawi imeneyo, Loweruka lililonse ine ndi mkulu wanga tinkakonda kupita kukacheza ndi banja linalake la Mboni za Yehova. A Joe McGrath, omwe anali bambo a banja limenelo, ankatiphunzitsa Baibulo limodzi ndi ana awo aakazi atatu. Banja lawo linali losangalala ndipo ankakondana kwambiri. A McGrath ankakonda kwambiri ana awo komanso ankalemekeza kwambiri akazi awo. Tinawazolowera kwambiri moti tinkangowatchula kuti ankolo. Ndinkakondanso kupita nawo limodzi ku misonkhano mlungu uliwonse komanso ku misonkhano ikuluikulu. Nthawi imeneyo sindidzaiiwala chifukwa ndinkasangalala kukhala ndi a Mboni.

Koma umu si mmene zinthu zinalili kunyumba kwathu. Mayi anga ankangokhalira kudandaula zimene bambo anga ankachita. Ndili ndi zaka 10, amayi anasiya kusonkhana ndi a Mboni za Yehova. Koma ineyo ndinapitirizabe moti ndinabatizidwa ndili ndi zaka 17 ngakhale kuti chidwi changa chinali chitalowa pansi. Kenako ndinayamba kuchita makhalidwe oipa moti ndinasiya kusonkhana ndi a Mboni.

NDINAGANIZA ZOBWERERA KWA YEHOVA

Patangopita nthawi yochepa nditakwatiwa, akulu awiri a Mboni za Yehova anabwera kunyumba kwathu. Akuluwo anandifotokozera zimene ndingachite kuti ndibwererenso kwa Yehova ndipo anapempha mmishonale wina dzina lake Cindy kuti azindithandiza. Nthawi imeneyi n’kuti chikhulupiriro changa chitatheratu moti ndinapempha mmishonaleyo kuti andipatse umboni woti Baibulo ndi Mawudi a Mulungu. Cindy anandionetsa maulosi a m’Baibulo omwe anakwaniritsidwa. Patapita nthawi, tinayamba kugwirizana kwambiri ndipo tsiku lina anandipempha kuti ndiyambirenso kuphunzira Baibulo. Nditayamba kuphunzira, ndinaona kuti Yehova ndi Mulungu wachikondi ndipo amafuna kuti ndizisangalala.

Nditayambiranso kusonkhana ndi a Mboni, ndinkakhala wosangalala kwambiri kusiyana ndi mmene ndinkakhalira ndi anthu omwe ndinkapanga nawo mafilimu. Komabe zinthu zomwe ndinakumana nazo ndili mwana zinandichititsa kuti ndisamakhulupirire aliyense ndipo ndinkadziona kuti ndine wosafunika. Mayi wina wa mumpingo womwe ndinkasonkhana anandithandiza kudziwa zomwe ndingachite kuti ndithane ndi vuto langalo pogwiritsa ntchito Baibulo ndipo ndinayamba kukhala ndi anzanga apamtima.

NDINAPEZA CHINTHU CHAMTENGO WAPATALI

Mu 1997, ine ndi mwamuna wanga tinasamukira ku Hollywood, m’dziko la United States. Titafika kumeneko ndinayamba kuphunzitsa anthu ena Baibulo. Ntchito imeneyi imandithandiza kuti ndizikhala wosangalala ndipo ndimaona kuti ndi chinthu chamtengo wapatali kwambiri kuposa kukhala wotchuka komanso kupanga mafilimu. M’chaka cha 2002, ndinakumana ndi Cheri amene ndinadziwana naye ku Hong Kong. Nayenso anasankhidwapo kukhala chiphadzuwa cha ku Hong Kong ndipo ndi amene ndinadzamulowa m’malo. Pa nthawi ya mwambowu Cheri ndi amene anandiveka chisoti chomwe amaveka munthu amene wasankhidwa kukhala chiphadzuwa. Moyo wake unali wofanananso kwambiri ndi wa ine chifukwa nayenso anali akita wa m’mafilimu komanso ankakonza ndi kutulutsa mafilimu. Cheri anakhala munthu wotchuka kwambiri pa nkhani yokonza mafilimu.

Ndinamva chisoni kwambiri Cheri atandiuza kuti mnyamata amene ankafuna kukwatirana naye anamwalira atadwala mwadzidzidzi matenda a mtima. Anthu achipembedzo chake chachibuda sanamuthandize kuthetsa nkhawa yake. Ngakhale kuti nayenso anali wotchuka ndipo ankaoneka kuti zinthu zikumuyendera, sankasangalala komanso sankakhulupirira aliyense. Ndinayamba kumuuza zomwe ndinaphunzira m’Baibulo. Koma analibe nazo chidwi kwenikweni chifukwa cha zimene ankakhulupirira ku chipembedzo chake.

Cheri akupanga filimu inayake

Tsiku lina m’chaka cha 2003, Cheri anandiimbira foni ali ku Vancouver m’dziko la Canada komwe ankapanga filimu. Anandiuza kuti nthawi ina akuyendetsa galimoto anagoma ndi mmene malo ena ankaonekera. Kenako anayamba kupemphera mokweza kumufunsa Mulungu kuti: “Kodi ndingakudziweni bwanji? Nanga dzina lanu ndinu ndani?” Kenako anayenda n’kudutsa pa Nyumba ya Ufumu inayake pamene anaonapo dzina la Mulungu lakuti Yehova. Atangoona dzina limeneli anadziwa kuti basi Mulungu wayankha pemphero lake. Choncho anandiuza kuti akufuna atakumana ndi a Mboni. Ndinamuthandiza kupeza a Mboni za Yehova ndipo pasanapite nthawi anapita ku mpingo wina wa Chitchainizi ku Vancouver.

Atabwerako, Cheri anandiuza kuti “Anthu ake ndi achikondi komanso ochezeka kwambiri moti ndinali womasuka kucheza nawo.” Ndinasangalala ndi zimene anandiuzazi chifukwa pa nthawi imene ankapanga mafilimu analibe anzake apamtima. Cheri anapitirizabe kupita ku misonkhano. Koma m’chaka cha 2005, anasainirana kontirakiti ndi kampani ina ya ku China kuti akawapangire mafilimu awiri. Zimenezi zinachititsa kuti abwererenso ku Hong Kong. Koma mu 2006 ndinasangalala kwambiri nditamva kuti Cheri anabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova pa msonkhano wina ku Hong Kong komweko. Komabe, sanasiye kupanga mafilimu ndipo zimenezi zinamusokoneza kwambiri komanso ankakhala wosasangalala.

NDIMASANGALALA NDIKAMATHANDIZA ENA KUDZIWA MULUNGU

Koma m’chaka cha 2009, Cheri anaganiza zosiya kupanga mafilimu kuti azitumikira Yehova bwinobwino. Anakhala ndi anzake ambiri omwe analinso a Mboni. Kenako anayamba kugwiritsira ntchito nthawi yake yambiri polalikira za Ufumu wa Mulungu ndipo amasangalala kuthandiza ena kuti adziwe Yehova.—Mateyu 24:14.

Kenako Cheri anaganiza zophunzira Chinepali kuti azitha kuthandiza kagulu kena ka Mboni za Yehova kolankhula chinenerochi, komwe kanali ku Hong Kong. Anthu ambiri omwe amalankhula Chinepali amasalidwa chifukwa chakuti salankhula bwinobwino Chingelezi kapena Chitchainizi komanso chifukwa chakuti chikhalidwe chawo n’chosiyana ndi cha anthu ena. Cheri anandiuza kuti amasangalala kwambiri kuphunzira Baibulo ndi anthu amenewa. Tsiku lina akulalikira kunyumba ndi nyumba anakumana ndi mayi wina wachinepali yemwe ankadziwa pang’ono za Yesu koma anali asanamvepo za Yehova Mulungu. Cheri anasonyeza mayiyo kuchokera m’Baibulo kuti Yesu ankapemphera kwa Atate wake wakumwamba. Mayiyu atazindikira kuti nayenso akhoza kumapemphera kwa Yehova Mulungu, anavomera kuti aziphunzira Baibulo. Kenako mwamuna wa mayiyo komanso mwana wake wamkazi anayambanso kuphunzira Baibulo.—Salimo 83:18; Luka 22:41, 42.

Cheri akulalikira

Nditaona kuti Cheri akusangalala kwambiri chifukwa chogwiritsa ntchito nthawi yake yonse polalikira, ndinayamba kudzifunsa kuti: ‘Ndiye ineyo n’chiyani chikundilepheretsa kuchita zimenezi?’ Pa nthawi imeneyi n’kuti inenso nditabwerera ku Hong Kong. Ndinaganiza zosintha zina ndi zina kuti ndizilalikira nthawi zonse. Ndinazindikira kuti ukamaphunzitsa anthu Mawu a Mulungu komanso ukamawathandiza kuti awamvetse m’pamene umakhala wosangalala.

Ndinazindikira kuti ukamaphunzitsa anthu Mawu a Mulungu komanso ukamawathandiza kuti awamvetse m’pamene umakhala wosangalala

Mwachitsanzo, ndinathandiza mayi wina wa ku Vietnam amene ankangokhalira kudandaula komanso kulira. Panopa mayiyo amakhala mosangalala ndipo nthawi zonse amasonkhana ndi a Mboni za Yehova.

Ineyo ndi Cheri tinapeza chinthu chapamwamba kuposa kukhala munthu wotchuka. Ngakhale kuti tinali otchuka chifukwa chopanga mafilimu, timaona kuti panopa timakhala osangalala kwambiri tikamathandiza ena kudziwa Yehova komanso kumulemekeza. Timaona kuti mawu amene Yesu ananena ndi oona. Iye anati: “Kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.”—Machitidwe 20:35.