Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO | KODI A MBONI ZA YEHOVA NDI ANTHU OTANI?

Kodi a Mboni za Yehova ndi anthu otani?

Kodi a Mboni za Yehova ndi anthu otani?

A Mboni za Yehovafe timapezeka m’mayiko osiyanasiyana ndipo ndife gulu lachipembedzo lodziimira palokha. Ngakhale kuti likulu lathu lili ku United States, a Mboni ambiri amapezeka m’mayiko ena. Panopa tilipo 8 miliyoni ndipo timaphunzira Baibulo ndi anthu m’mayiko oposa 230. Timachita zimenezi pomvera zimene Yesu ananena. Iye anati: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse.”—Mateyu 24:14.

Kulikonse kumene timakhala timayesetsa kumvera malamulo a boma ngakhale kuti sitilowerera nawo m’nkhani zandale. Sitichita zimenezi chifukwa timamvera zimene Yesu anauza otsatira ake. Anawauza kuti: “Simuli mbali ya dzikoli.” N’chifukwa chake sitichita nawo zandale komanso kumenya nawo nkhondo. (Yohane 15:19; 17:16) Ndipotu pa nthawi ya nkhondo yachiwiri ya padziko lonse, a Mboni za Yehova ambiri anamangidwa, kuzunzidwa komanso ena anaphedwa chifukwa chokana kuchita zinthu zosemphana ndi chikhulupiriro chawo. Munthu wina, yemwe anali bishopu ku Germany, analemba kuti: “A Mboni za Yehova ndi anthu okhawo omwe anakanitsitsa kumenya nawo nkhondo pa nthawi ya ulamuliro wa Hitler, moti n’zomveka anthuwa akamanena kuti salowerera zandale komanso kumenya nawo nkhondo.”

Nyuzipepala ina ya ku Czech Republic inati: “[A Mboni za Yehova] ndi anthu a khalidwe labwino kwambiri ndiponso si anthu odzikonda. Zikanakhala zotheka, bwenzi anthu amenewa titawapatsa maudindo akuluakulu m’boma. Koma chifukwa choti sachita nawo zandale, zimenezi sizingatheke. . . . Amalemekeza boma limene likulamulira, kungoti amakhulupirira kuti ndi Ufumu wa Mulungu wokha umene udzathetse mavuto onse.”—Nová Svoboda.

Komabe timachita zinthu zina ngati mmene amachitira anthu ena onse. Ndipo sitidzipatula, chifukwa Yesu anapempherera otsatira ake kuti: “Sindikupempha kuti muwachotse m’dziko.” (Yohane 17:15) Choncho nafenso timapita kuntchito, kumsika komanso kusukulu ngati mmene anthu ena onse amachitira.