NSANJA YA OLONDA July 2014 | N’chifukwa Chiyani Anthu Abwino Nawonso Amakumana Ndi Mavuto?

Kodi amachititsa ndi Mulungu? Kodi anthu amavutika chifukwa cha zoipa zimene ankachita asanabadwe moyo uno? Kodi pali chimene chingatithandize kuti tisamakumane ndi mavuto?

NKHANI YAPACHIKUTO

Mavuto Ali Ponseponse

Ngati kuli Mulungu Wamphamvuyonse, n’chifukwa chiyani sateteza anthu abwino kuti asamakumane ndi mavuto?

NKHANI YAPACHIKUTO

N’chifukwa Chiyani Anthu Abwino Nawonso Amakumana Ndi Mavuto?

Baibulo limatchula zinthu zitatu zimene zimachititsa kuti anthu azivutika.

NKHANI YAPACHIKUTO

Mulungu Adzachotsa Mavuto Onse Padzikoli

Kodi mukufuna kudzakhala m’dziko lopanda mavuto, limene Mulungu walonjeza?

BAIBULO LIMASINTHA ANTHU

Ndinkayenda ndi Mfuti Kulikonse

Annunziato Lugarà anali wachiwawa, wakuba komanso chigawenga choopsa.

Kodi Mungatani Kuti Muzilangiza Bwino Ana Anu?

Baibulo limatchula zinthu zitatu zimene makolo ayenera kuchita polangiza ana.

Kodi Mukudziwa?

Kodi anthu akale ankatani kuti sitima zawo zisalowe madzi? Kodi kale anthu ankatani akafuna kusunga nsomba kuti zisawonongeke?

Kodi N’zotheka Kuona Mulungu Yemwe ndi Wosaoneka?

Werengani nkhaniyi kuti mudziwe mmene mungagwiritsire ntchito “maso a mtima wanu” kuona Mulungu.

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Kodi tiyenera kupemphera pa nthawi yokha imene tikufuna kuti Mulungu atithandize zinazake?