Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO | N’CHIFUKWA CHIYANI ANTHU ABWINO NAWONSO AMAKUMANA NDI MAVUTO?

Mavuto Ali Ponseponse

Mavuto Ali Ponseponse

Mayi wina wazaka 35, dzina lake Smita, * yemwe ankakhala mumzinda wa Dhaka ku Bangladesh, ankadziwika kuti anali wachikondi komanso woganizira ena. Anthu ankaona kuti mayiyu anali wolimbikira ntchito, banja lake linkayenda bwino komanso ankathandiza ena kuti adziwe Mulungu. Koma Smita anadwala mwadzidzidzi, n’kumwalira pasanathe mlungu umodzi. Zimenezi zinamvetsa chisoni kwambiri anthu a m’banja lake komanso anzake.

James ndi mkazi wake, omwe onse anali azaka za m’ma 30, ankakhala ku New York. Mofanana ndi Smita, iwonso ankadziwika kuti anali anthu abwino. Pa nthawi ina, anapita kudera lakumadzulo kwa dziko la United States kukacheza kwa anzawo. Koma chomvetsa chisoni n’choti sanabwererenso. Ali komweko, anachita ngozi yoopsa ya galimoto ndipo anafa n’kusiya abale ndi anzawo akuntchito manja ali m’khosi.

Masiku ano, mavuto ali ponseponse. Asilikali ambirimbiri komanso anthu osalakwa amafa pa nkhondo. Anthu enanso osalakwa amavutika chifukwa cha zinthu zophwanya malamulo ndi zachiwawa zimene anthu ena amachita. Palinso anthu ambiri amene amavutika chifukwa cha ngozi komanso chifukwa cha kulumala atadwala matenda oopsa. Izi zimachitikira aliyense kaya wolemera, wosauka, wamkulu kapenanso mwana. Ngozi zadzidzidzi, monga kusefukira kwa madzi, zimatha kusesa mudzi kapena dera lonse mosasankha. Ndiponso anthu ambiri amasankhana mitundu komanso amachita zinthu mwatsankho, ndipo mwina inunso mwavutikapo chifukwa cha zinthu zoterezi.

Choncho, n’zosadabwitsa kuti anthu amadzifunsa kuti:

  • N’chifukwa chiyani anthu abwino nawonso amakumana ndi mavuto?

  • Kodi Mulungu ndi amene amachititsa mavutowa?

  • Kodi mavutowa amangochitika mwangozi kapena anthu ndi amene amawachititsa?

  • Kodi anthu amavutika chifukwa cha zoipa zomwe anachita m’moyo wina umene anali nawo asanabadwe moyo uno?

  • Ngati kuli Mulungu Wamphamvuyonse, n’chifukwa chiyani sateteza anthu abwino kuti asamakumane ndi mavuto?

  • Kodi mavutowa adzatha?

Kuti tipeze mayankho a mafunso amenewa, tikufunikira kudziwa kaye mayankho a mafunso ofunika kwambiri awa: N’chifukwa chiyani zoipa zimachitika? Ndipo kodi Mulungu adzachita chiyani kuti athetse mavutowa?

^ ndime 3 Mayina asinthidwa.