Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO | N’CHIFUKWA CHIYANI ANTHU ABWINO NAWONSO AMAKUMANA NDI MAVUTO?

Mulungu Adzachotsa Mavuto Onse Padzikoli

Mulungu Adzachotsa Mavuto Onse Padzikoli

Baibulo limatiuza momveka bwino zimene Yehova ndi Mwana wake, Yesu Khristu, adzachite pothetsa mavuto omwe Satana anayambitsa padzikoli. Limati: “Mwana wa Mulungu [Yesu] anaonekera kuti awononge ntchito za Mdyerekezi.” (1 Yohane 3:8) M’dzikoli mwadzaza anthu adyera, achidani komanso oipa ndipo posachedwapa anthu amenewa awonongedwa. Ponena za Satana Mdyerekezi, yemwe ndi “wolamulira wa dzikoli,” Yesu analonjeza kuti ‘adzaponyedwa kunja.’ (Yohane 12:31) Kenako Mulungu adzakhazikitsa dziko latsopano lolungama ndipo anthu azidzakhala mwamtendere chifukwa Satana kudzakhala kulibe.—2 Petulo 3:13.

Nanga kodi n’chiyani chidzachitike kwa anthu amene akupitirizabe kuchita zoipa ndipo safuna kusintha? Baibulo limanena momveka bwino zomwe zidzachitikire anthu oterewa. Limati: “Owongoka mtima ndi amene adzakhale m’dziko lapansi, ndipo opanda cholakwa ndi amene adzatsalemo. Koma oipa adzachotsedwa padziko lapansi ndipo achinyengo adzazulidwamo.” (Miyambo 2:21, 22) Choncho anthu ochita zoipa sadzachititsanso kuti anthu ena azichita zoipa. M’kupita kwa nthawi, anthu omvera adzakhala angwiro chifukwa uchimo umene anatengera kwa Adamu udzakhala utatha.—Aroma 6:17, 18; 8:21.

M’dziko latsopano limenelo, kodi Mulungu adzachita zotani zimene zidzathandize kuti anthu asamachitenso zoipa? Sikuti adzalanda anthu ufulu wosankha zochita, kuti anthuwo azingochita zinthu ngati maloboti. Koma adzawaphunzitsa kuti azitsatira malamulo ake ndipo adzawathandiza kuti asamachitenso zoipa.

Mulungu adzachotsa zinthu zonse zimene zimayambitsa mavuto padzikoli

Nanga kodi Mulungu adzachita chiyani kuti ngozi komanso masoka achilengedwe zisamachitike? Iye analonjeza kuti posachedwapa Ufumu wake uyamba kulamulira dzikoli. Yesu Khristu, yemwe ndi Mfumu imene iye anasankha, ali ndi mphamvu zochiritsa odwala. (Mateyu 14:14) Alinso ndi mphamvu zoti angathe kuletsa masoka achilengedwe kuti asachitike. (Maliko 4:35-41) Choncho mavuto onse amene amayamba chifukwa cha ‘masoka ndi zinthu zosayembekezereka,’ adzatha. (Mlaliki 9:11) Mu Ufumu wa Khristu, anthu sadzakumananso ndi mavuto alionse.—Miyambo 1:33.

Nanga bwanji za anthu ambirimbiri amene anamwalira chifukwa cha mavuto osiyanasiyana? Yesu atatsala pang’ono kuukitsa Lazaro, yemwe anali mnzake wapamtima, anati: “Ine ndine kuuka ndi moyo.” (Yohane 11:25) Izi zikusonyeza kuti Yesu ali ndi mphamvu zotha kuukitsa anthu amene anamwalira.

Ngati mukufuna kudzakhala m’dziko lopanda mavuto, limene Mulungu walonjezali, tikukulimbikitsani kuti muyambe kuphunzira Baibulo kuti mudziwe zambiri zokhudza Mulungu woona komanso zimene adzachite m’tsogolo. A Mboni za Yehova a m’dera lanu ndi okonzeka kukuthandizani kuchita zimenezi. Tikukulimbikitsani kuti mulankhule nawo za nkhaniyi kapena mulembe kalata pogwiritsa ntchito adiresi ya m’dziko lanu pa ma adiresi omwe ali patsamba 2 la magaziniyi.