NSANJA YA OLONDA June 2014 | Kodi Mawu a Mulungu Amati Chiyani pa Nkhani ya Kusuta Fodya?

Kudziwa mmene Mulungu amaionera nkhaniyi kungakuthandizeni kusiya kusuta.

NKHANI YAPACHIKUTO

Mliri wa Padziko Lonse

N’chifukwa chiyani vutoli likupitirirabe ngakhale kuti mayiko akuyesetsa kuti lithe?

NKHANI YAPACHIKUTO

Kodi Mawu a Mulungu Amati Chiyani pa Nkhani ya Kusuta Fodya?

M’Baibulo mulibe mawu akuti fodya, ndiye tingadziwe bwanji zimene limanena pa nkhaniyi?

Kodi Munalawako Chakudya Chopatsa Moyo?

N’chifukwa chiyani Yesu ananena kuti iye ndi chakudya chopatsa moyo komanso chochokera kumwamba?

Kodi Makolo Athu Omwe Anamwalira Adzakhalanso ndi Moyo?

Baibulo limanena kuti Mulungu adzaukitsa olungama ndi osalungama omwe. N’chifukwa chiyani adzachite zimenezi?

Kodi Anthu Atatu Amene Ankafufuza Choonadi M’zaka za m’ma 1500 Anapeza Zotani?

Capito, Cellarius ndi Campanus anachita zinthu zimene zinachititsa kuti tchalitchi cha Katolika komanso anthu otsutsa tchalitchichi azidana nawo.

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Kodi Mulungu adzakwaniritsa cholinga chakechi?

Zina zimene zili pawebusaiti

Kodi Mulungu Ndi Amene Amachititsa Kuti Tizivutika?

N’chifukwa chiyani munthu aliyense amavutika, ngakhale amene Mulungu amamukonda?